Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinayamba N’chiyani?

Chinayamba N’chiyani?

Chinayamba N’chiyani?

MU 1973, Dr Martin Cooper anapanga foni yam’manja ndipo iye anali munthu woyamba kupanga foni yotere. Foniyi inali ndi batire, wailesi komanso kachipangizo ka kompyuta kamene kamagwira ntchito ngati ubongo. Anthu a ku New York anali ndi chidwi kwambiri kuona Cooper akulankhula pa foni mumsewu. Koma iye anakwanitsa kupanga foniyi chifukwa chakuti m’chaka cha 1800, Alessandro Volta anapanga batire. Ndiponso m’chaka cha 1876 kunapangidwa telefoni, m’chaka cha 1895 kunapangidwa wailesi ndipo m’chaka cha 1946 kunapangidwa kompyuta. Kenako mu 1971 kunapangidwa kachipangizo ka kompyuta kamene kamagwira ntchito ngati ubongo, ndipo zimenezi n’zimene zinachititsa kuti zisakhale zovuta kupanga foni yam’manja. Komabe, mwina tingafunse kuti, ‘Kodi aka kanali koyamba kupanga chipangizo cholankhulirana?’ Ayi, chifukwa chipangizo chotere chinalipo kale m’chilengedwe.

Taganizirani zimene zimathandiza kuti inuyo muzitha kutulutsa mawu. Mu ubongo wanu muli maselo mabiliyoni ambiri amene amatumiza mauthenga. Ndipo kupitirira theka la maselo amenewa amathandiza kuti muzitha kulankhula. Palinso minofu pafupifupi 100 ya lilime, milomo, msagwada, kholingo ndiponso ya pachifuwa imene imathandiza kuti muzitha kulankhula.

Makutu anunso amathandiza kuti muzitha kulankhulana ndi anthu ena. Mawu akalowa m’makutu, amatumizidwa ku ubongo ndipo ubongowo umatha kukuthandizani kusiyanitsa mawu a anthu osiyanasiyana komanso kudziwa kumene mawuwo akuchokera. Zimenezi ndi zina mwa zinthu zimene zimakuthandizani kuti muzitha kumvana ndi munthu mmodzi ngakhale kuti enanso akulankhula.

Choncho zipangizo zolankhulirana monga mafoni a m’manja (omwe amatha kusonyeza kuti akuimba ndani) si zachilendo. Zinthu zimenezi zinalipo kale m’chilengedwe.

[Zithunzi patsamba 3]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

1800

Batire

1876

Telefoni

1971

Kachipangizo ka kompyuta kamene kamagwira ntchito ngati ubongo

1973

Dr. anapanga foni yam’manja

[Mawu a Chithunzi]

Dr. Cooper and mobile phone: © Mark Berry

[Zithunzi patsamba 2]

Zithunzi zakumanja kwa tsamba 2, kuyambira pansi kupita m’mwamba: Guglielmo Marconi anapanga wailesi, Thomas Edison anapanga babu, Granville T. Woods anapanga telefoni, Wilbur ndi Orville Wright anapanga ndege mu 1903.