Ubwino Wosonyezana Chikondi
Ubwino Wosonyezana Chikondi
Mayi wina wachitsikana atabereka ana awiri amapatsa anapempha pulofesa wina kuti amupatse malangizo a mmene angalerere ana akewo. Pulofesayo anamuuza kuti: “Muziwakumbatira nthawi zambiri.” Iye ananenanso kuti: “Muziwasonyeza m’njira zinanso zosiyanasiyana kuti mumawakonda. Muziwapsompsona, kuwasonyeza kuti mukumvetsa zimene akufuna, kuwasonyeza kuti mwasangalala, kuwapatsa zinthu, kuwakhululukira, ndiponso kuwapatsa chilango ngati pangafunike kutero. Sitiyenera kungoganizira kuti ana athu amadziwa kuti timawakonda, tiyenera kuwasonyeza chikondicho.”
Tiffany Field, yemwe ndi mkulu wa bungwe lina la zakafukufuku ku yunivesite ya Miami, ku Florida, m’dziko la United States, ananena zofanana ndi zimenezi. Iye anati: “Kukumbatira ana n’kofunika kwambiri kuti anawo akule bwino ngati mmene zimakhalira akamadya chakudya chopatsa thanzi komanso kuchita masewera olimbitsa thupi.”
Kodi anthu achikulirenso amafunika kukumbatiridwa? Inde. Munthu wina amene anachita maphunziro a mmene anthu amaganizira, dzina lake Claude Steiner, atachita kafukufuku anapeza kuti, kaya munthu ndi mwana kapena wamkulu, amasangalala kwambiri akauzidwa mawu olimbikitsa kapena kukumbatiridwa. Mayi wina amene amasamalira anthu okalamba, dzina lake Laura, anati: “Ndaona kuti kusonyeza anthu okalamba chikondi n’kofunika kwambiri. Mukamawakumbatira komanso kuwachitira zinthu zina zosonyeza kuti mumawakonda, iwo amakudalirani ndipo amatsatira malangizo anu mosavuta. Chikondi choterocho chimasonyezanso kuti mumawalemekeza.”
Ndiponso, kusonyeza ena chikondi kumapindulitsa anthu amene tikuwasonyeza chikondiwo komanso ifeyo. Nthawi ina Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Timasangalala kwambiri ngati tasonyeza chikondi kwa anthu amene akuvutika kapena amene ali ndi nkhawa. M’Baibulo muli nkhani zambiri za anthu amene anasonyezedwapo chikondi.
Tangoganizirani mmene ‘munthu wina amene anali wakhate thupi lonse,’ yemwe anthu ankamusala, anamvera Yesu Khristu atamukhudza.—Luka 5:12, 13; Mateyo 8:1-3.
Ganiziraninso mmene mneneri wokalamba Danieli anamvera mngelo wa Mulungu atamuuza mawu olimbikitsa ndiponso kumukhudza katatu. Zimenezi zinathandiza Danieli kuti apezenso mphamvu.—Danieli 10:9-11, 15, 16, 18, 19.
Panthawi ina, anzake apamtima a mtumwi Paulo anayenda ulendo wa makilomita 50 kuchokera mumzinda wa Efeso kupita ku Mileto kukakumana naye. Kumeneko Paulo anawauza anzakewo kuti mwina sadzamuonanso. Paulo ayenera kuti anasangalala kwambiri anzakewo ‘atam’kupatira ndi kumpsompsona.’—Machitidwe 20:36, 37.
N’chifukwa chake Baibulo komanso akatswiri ambiri masiku ano amalimbikitsa kusonyezana chikondi. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti tikhale osangalala. Ndipo n’zoonekeratu kuti kusonyeza chikondi n’kofunika kwa ana ndi akulu omwe.