Mabanja Amene Zinthu Zikuwayendera Bwino—Chigawo Chachiwiri
Mabanja Amene Zinthu Zikuwayendera Bwino—Chigawo Chachiwiri
Monga mmene tafotokozera m’chigawo choyamba, mfundo za m’Baibulo zingathandize mabanja amene akukumana ndi mavuto. * Yehova Mulungu amalonjeza anthu amene amatsatira mfundo zake kuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.”—Salmo 32:8.
Banja likamakumana ndi mavuto a ndalama. Nkhani za ndalama ndi zimene nthawi zambiri zimayambitsa mikangano m’banja. Koma mfundo za m’Baibulo zingathandize mabanja kuti asamakonde kwambiri ndalama. Yesu anati: “Lekani kudera nkhawa moyo wanu chimene mudzadya kapena chimene mudzamwa, kapena matupi anu chimene mudzavala. . . . Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti zinthu zonsezi inu mukuzisowa.”—Mateyo 6:25, 32.
Patsamba 23, pali nkhani ya Issachar wa ku United States. Iye ndi banja lake anakumana ndi mavuto a ndalama, nyumba yawo itawonongedwa ndi mphepo yamkuntho, yotchedwa Katrina.
Ngati wina m’banja mwanu akudwala matenda aakulu. Tonse timadwala koma matenda ambiri amene timadwala sakhalitsa ndipo sitichedwa kuchira. Bwanji ngati wina m’banja lanu akudwala matenda aakulu? Baibulo limanena kuti Yehova amathandiza anthu amene akudwala. (Salmo 41:1-3) Kodi Yehova angagwiritse ntchito bwanji anthu ena m’banja kuti asamalire wodwalayo?
Patsamba 24, pali nkhani ya bambo wina wa ku Japan, dzina lake Hajime. Iye ndi ana ake anathandizana kusamalira mkazi wake, Noriko, atamupeza ndi matenda aakulu.
Ngati mwana wamwalira. Imfa ya mwana ndi yopweteka kwambiri kwa makolo. Yehova analonjeza kuti adzapukuta misozi imene imabwera chifukwa cha imfa. (Chivumbulutso 21:1-4) Koma ngakhale panopa, iye amatonthoza anthu amene aferedwa.—Salmo 147:3.
Patsamba 25, pali nkhani ya Fernando ndi Dilma a ku United States. Baibulo linawathandiza kwambiri mwana wawo wamkazi, yemwe anali atangobadwa kumene, atamwalira.
Baibulo lili ndi malangizo odalirika amene angathandize mabanja omwe akukumana ndi mavuto. Onani zimenezi m’nkhani zotsatirazi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Onani tsamba 14 mpaka 17 m’magazini ino.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 23]
Banja Likamakumana ndi Mavuto a Ndalama
Yosimbidwa ndi Issachar Nichols, wa ku United States
“Mphepo yamkuntho ya Katrina inawonongeratu nyumba yathu. Ndipo sukulu imene ndinkaphunzitsa inamira m’madzi kwa mwezi ndi theka.”
M’CHAKA cha 2005, ine ndi mkazi wanga Michelle, ndiponso mwana wathu Sydney, yemwe panthawiyo anali ndi zaka ziwiri, tinkakhala m’tawuni ya Bay St. Louis, ku Mississippi, U.S.A. Ine ndi mkazi wanga ndife a Mboni za Yehova, ndipo tinkathera nthawi yaitali tikugwira ntchito yolalikira. Ndinalinso mphunzitsi pasukulu ina mumzinda wa New Orleans, ku Louisiana. Ndinkagwira ntchito masiku atatu pamlungu, ndipo masiku enawo ndinkakhala ndi mpata wophunzitsa anthu Baibulo. Zimenezi zinkachititsa kuti ine ndi mkazi wanga tizikhala osangalala kwambiri. Kenako tinamva chenjezo lakuti kukubwera mphepo yamkuntho ya Katrina. Mwamsanga tinakonza zosamuka mumzindawo.
Mphepoyi itatha, nyumba yathu ndiponso sukulu imene ndinkaphunzitsa zinali zitawonongekeratu. Ndalama zimene boma ndi makampani a inshuwalansi anatipatsa zinatithandiza kumanganso nyumba ina, koma ndinavutika kupeza ntchito yodalirika. Nayenso mkazi wanga anayamba kudwala atamwa madzi oipa. Chitetezo cha thupi lake chinachepa kwambiri, ndipo kenako udzudzu utamuluma anayamba kudwala matenda enanso otchedwa West Nile. Panthawiyi tinkawononga ndalama zambiri.
Choncho, tinayamba kugwiritsa ntchito ndalama zathu mosamala kwambiri, ngakhale pa zinthu zofunika. Ndinayambanso kugwira ntchito iliyonse imene ingapezeke.
Kunena zoona, kuwonongeka kwa zinthu zimene tinali nazo kunali kopweteka. Koma tinasangalala kuti tili ndi moyo. Ndipo zinthu zimene takumana nazo zatithandiza kuona kuti katundu kapena chuma ndi zosafunika kwenikweni. Timakumbukira mawu a Yesu akuti: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15.
Tinazindikiranso kuti ngakhale kuti tinataya chuma chambiri, pali anthu ena amene anataya zinthu zambiri komanso moyo wawo. Ichi n’chifukwa chake ndinayamba kugwira ntchito yothandiza ndi kulimbikitsa anthu amene katundu wawo anawonongeka.
Lemba la Salmo 102:17 lakhala likutilimbikitsa kwambiri panthawi yonseyi. Lembali limati Yehova Mulungu ‘amasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapeputsa pemphero lawo.’ Tikuona kuti Mulungu wakhala akusamalira banja lathu.
[Bokosi patsamba 23]
Ku America kutachitika mphepo ya mkuntho ya Katrina ndi Rita mu 2005, Mboni za Yehova zinakhazikitsa mwamsanga malo 13 operekera thandizo, malo 9 osungira zakudya ndiponso malo anayi osungira mafuta. Pafupifupi Mboni za Yehova 17,000 za ku United States ndi mayiko ena 13 zinabwera kudzathandiza ntchitoyi. Iwo anakonza nyumba masauzande ambiri.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 24]
Ngati Wina M’banja Mwanu Akudwala Matenda Aakulu
Yosimbidwa ndi Hajime Ito, wa ku Japan
“Nthawi zambiri ndinkasangalala kuphika chakudya pamodzi ndi mkazi wanga, Noriko. Koma kenako anayamba kudwala ndipo panopa iye sangathe kudya, kumwa, ngakhale kulankhula kumene. Ndipo amayenda pa njinga ya anthu olumala komanso amapuma pogwiritsa ntchito makina opumira.”
M’MWEZI wa May, chaka cha 2006, mkazi wanga anayamba kuvutika kulankhula. Kenako anayambanso kuvutika kudya ndi kumwa. M’mwezi wa September, madokotala anamupeza ndi matenda oopsa amene amawononga ubongo komanso mitsempha ya msana. Patangotha miyezi inayi yokha moyo wathu unasinthiratu. Ndipo matenda a mkazi wanga anakulirakulirabe.
Patapita nthawi lilime ndi dzanja limodzi la Noriko zinasiya kugwira ntchito. Ndipo ankadya kudzera m’machubu komanso anapangidwa opaleshoni ya pakhosi kuti azitha kupuma bwino. Koma opaleshoniyi inamuchititsa kuti asamathe kulankhula. Zimenezi zinamukhudza kwambiri Noriko chifukwa poyamba iye sankatha kungokhala. Ndife a Mboni za Yehova ndipo Noriko ndi ana athu ankathera nthawi yawo yambiri akulalikira. Koma panopa mkazi wangayu amangogona ndipo amapuma mothandizidwa ndi makina.
Komabe Noriko amatha kuchita zinthu zambiri. Mwachitsanzo, amapita kumisonkhano yachikhristu panjinga yake, yomwe ili ndi makina omuthandiza kupuma. Panopa amavutika kumva, choncho mwana wathu amamulembera mfundo za pamsonkhanowo m’zilembo zazikulu kuti nayenso adziwe zimene zikunenedwa. Ngakhale kuti Noriko anasiya utumiki wa nthawi zonse, iye amalembera anthu makalata kuti awaphunzitse zimene Baibulo limanena. Amachita zimenezi pogwiritsira ntchito kachipangizo kenakake komwe kanaikidwa pa kompyuta yathu.—2 Petulo 3:13; Chivumbulutso 21:1-4.
Ine ndi ana anga timathandizana posamalira Noriko. Ana anga onse anasintha ntchito zimene ankagwira poyamba n’cholinga choti azikhala ndi nthawi yosamalira Noriko. Komanso tonse atatu tinagawana ntchito imene Noriko ankagwira asanayambe kudwala.
Masiku ena ndikadzuka m’mawa, Noriko amaoneka wofooka kwambiri. Ndipo ndimaganiza zomuuza kuti, ‘Lero usalalikire kuti upume.’ Koma Noriko amafunitsitsa kuuza anthu uthenga wa m’Baibulo. Ndikamuyatsira kompyuta kuti aigwiritse ntchito, Noriko amasangalala kwambiri. Iye akayamba kulemba amapezako bwino. Panopa ndazindikira kuti n’zofunika kwambiri kukhala ndi “zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye.”—1 Akorinto 15:58.
Nkhani ya Jason Stuart, amenenso anam’peza ndi matenda ngati amenewa, imene ili mu Galamukani! ya January 2006, yathandiza kwambiri Noriko kuti asamangokhala wokhumudwa. Ndipo madokotala atamufunsa chomwe chimamulimbitsa mtima, iye anawauza za nkhaniyi. Kenako tinawapatsa madokotalawo Galamukani! imene inali ndi nkhaniyi. Kulalikira ena kumamuthandiza kwambiri mkazi wanga kuti azikhala wosangalala.
Ineyo ndi Noriko takhala pabanja kwa zaka 30, koma zaka zitatu zapitazi m’pamene ndadziwa zinthu zambiri zabwino zokhudza iyeyo. Ndimasangalala kuti ndinakwatira mkazi wabwino.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 25]
Ngati Mwana Wamwalira
Yosimbidwa ndi Fernando ndi Dilma Freitas, a ku United States
“Mwana akamwalira zimapweteka kwambiri, ndipo n’zovuta kufotokoza mmene zimapwetekera.”
MWANA wathu wamkazi, amene tinam’patsa dzina lakuti Precious, anamwalira pa April 16, 2006, atangotha masiku 10 kuchokera pamene anabadwa. Mayi ake ali ndi pakati pa miyezi itatu, madokotala ananena kuti mwanayu anali ndi vuto la mtima. Ndipo patatsala masiku ochepa kuti abadwe, anatiuza kuti akhoza kubadwa wakufa kale koma ngati angabadwe wamoyo, sakhalitsa. Tinakhumudwa kwambiri titamva zimenezi. Zinali zovuta kukhulupirira kuti mwana wathu amwalira.
Mwana wathu Precious atabadwa, dokotala wina wamkulu anamuyeza ndipo anamupeza ndi matenda enaake oopsa (Trisomy 18) amene amagwira mwana mmodzi pa ana 5,000 aliwonse. Zinali zodziwikiratu kuti sakhala ndi moyo nthawi yaitali. Koma panalibe chilichonse chimene tikanachita kuti tim’pulumutse kupatulapo kumusamalira panthawi yochepa kwambiri yomwe anakhala ndi moyo.
Timathokoza kuti tinali ndi mwayi wokhala ndi Precious kwa masiku 10. Panthawiyi, ifeyo ndi ana athu atatu aakazi tinkamukonda kwambiri Precious. Tinkamunyamula, kulankhula naye, kumukumbatira, kumupsompsona ndiponso kumujambula zithunzi zambiri. Tinkakambirananso za munthu yemwe mwanayu akufanana naye. Dokotala amene anatiuza za matenda a Precious uja, ankabwera kudzamuona tsiku lililonse. Iye ankalira nafe limodzi ndipo ankatiuza kuti akutimvera chisoni kwambiri. Tsiku lina akucheza nafe, anajambula pamanja chithunzi cha Precious n’cholinga choti azidzamukumbukira. Ndipo anachichita fotokope n’kutipatsa.
Ndife a Mboni za Yehova ndipo sitikayikira ngakhale pang’ono zimene Baibulo limaphunzitsa. Timakhulupirira kuti Mulungu adzakonza dziko lapansi kuti likhale paradaiso ndiponso adzaukitsa anthu amene anafa, kuphatikizapo ana aang’ono monga Precious. (Yobu 14:14, 15; Yohane 5:28, 29) Tikuyembekezera nthawi imene tidzaonanenso ndi mwana wathuyu. Nthawi zonse tikamva mawu akuti “paradaiso,” timaganizira za Precious. Panopa timalimba mtima chifukwa timadziwa kuti Mulungu akumukumbukira ndipo ali kumanda kumene sakuvutika.—Mlaliki 9:5, 10.