N’chifukwa Chiyani Anthu Amasankhana?
N’chifukwa Chiyani Anthu Amasankhana?
“Nditangoyamba sukulu ya pulayimale ku Spain, ana a sukulu anzanga ankanditchula maina achipongwe chifukwa chakuti ndinali wamfupi kwambiri. Pafupifupi tsiku lililonse ndinkapita kunyumba ndikulira.”—Anatero Jennifer, yemwe makolo ake ndi ochokera ku Philippines.
“Nditakayamba kuphunzira pasukulu ina, ana ena achizungu ankandisala ndiponso ankandipatsa maina achipongwe. Nthawi zambiri ankandiyamba dala ndi cholinga choti timenyane. Ndinkayesetsa kuugwira mtima koma zinkandipweteka kwambiri.”—Anatero Timothy, yemwe amakhala ku America koma makolo ake ndi ochokera ku Africa.
“Ndili ndi zaka 7, anthu a fuko la Igbo ndi la Hausa ku Nigeria, anamenyana kwambiri. Chidani chimenechi chinandikhudza kwambiri ndipo inenso ndinayamba kudana ndi mnzanga wina wa fuko la Hausa amene ndinali naye kalasi imodzi.—Anatero John, wa fuko la Igbo.
“Tsiku lina, ine ndi m’mishonale mnzanga tinkalalikira anthu a m’dera lathu ndipo ana ena omwe anatumidwa ndi m’busa wina anayamba kutitsatira uku akutigenda ndi miyala. M’busayo ankadana nafe ndipo ankafuna kuti tisamuke m’deralo.”—Anatero Olga.
KODI munayamba mwanyozedwapo ndi anthu ena atsankho? Mwina anthu ena anakusalanipo chifukwa cha khungu, chipembedzo, msinkhu, kapena kusauka. Anthu amene nthawi zambiri amasalidwa, amakhala mwamantha. Nthawi zonse amakhala ndi nkhawa akakhala pagulu, akapita kokagula zinthu, kapena akasamukira kusukulu ina.
Komanso, tsankho lingalepheretse munthu kupeza ntchito, kulandira chithandizo cha mankhwala kuchipatala, kupeza maphunziro abwino ndiponso kupatsidwa ufulu wachibadwidwe. Nthawi zina atsogoleri andale amalimbikitsa tsankho ndipo zimenezi zimachititsa kuti anthu ayambe kumenyana ndi anthu amitundu ina. Nkhani yonena za kupha anthu amtundu wina chifukwa cha tsankho imapezeka m’Baibulo palemba la Estere 3:5, 6.
Ngakhale m’mayiko amene tsankho ndi loletsedwa, anthu amatha kumachitabe zinthu zatsankho. Mkulu wakale wa bungwe lina loona za ufulu wa anthu, anati: “Papita zaka 60 kuchokera pamene malamulo okhudza ufulu wa anthu anakhazikitsidwa . . . , koma anthu akusankhanabe mitundu.” Zimenezi n’zokhumudwitsa chifukwa masiku ano m’mayiko ambiri muli anthu amitundu yosiyanasiyana omwe anathawa nkhondo kwawo.
Choncho kodi zingatheke kuti anthu azikhala mogwirizana popanda kusankhana? Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.