Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungakonde Kuyenda pa Galimoto Yopalasa?

Kodi Mungakonde Kuyenda pa Galimoto Yopalasa?

Kodi Mungakonde Kuyenda pa Galimoto Yopalasa?

MUKAFIKA mumzinda wa Dhaka, womwe ndi likulu la dziko la Bangladesh, mumaona kuti mwafikadi malo achilendo. Mumaona njinga zambirimbiri zamatayala atatu zikudutsana paliponse. Nthawi zambiri njingazi zimakhala zitanyamula anthu komanso katundu.

Mumzinda wa Dhaka, anthu amakonda kugwiritsa ntchito njingazi akakhala paulendo. Njinga zodziwika ndi boma zilipo 80,000, komabe anthu ambiri amaona kuti chiwerengero cha njinga zomwe zimayenda mumzindawu patsiku n’choposa pamenepa. Panopa ku Dhaka kumadziwika kuti ndi kuchimake kwa njingazi padziko lonse.

Njinga Zoyambirira

Ngakhale kuti njinga zoyambirira zamtunduwu zinayamba kugwiritsidwa ntchito mu ulamuliro wa mfumu Louis ya ku France (1638-1715), njinga yoyamba yodziwika bwino inapangidwa ndi munthu wina wochokera ku America, dzina lake Jonathan Gable, amene anali m’mishonale ku Japan m’zaka za m’ma 1870. Akuti njingayi anapangira mkazi wake yemwe ankadwaladwala, ndipo inali njinga yoyamba kutchedwa dzina lakuti jinrikisha, lomwe ku Japan limatanthauza galimoto yokokedwa ndi anthu. M’kupita kwa nthawi, anthu ambiri ku Asia anayamba kukwera njingazi chifukwa zinali zotsika mtengo. Charles Taze Russell (kumanjaku), yemwe ankatsogolera pa ntchito ya gulu la Ophunzira Baibulo (lomwe panopa limadziwika kuti Mboni za Yehova), atapita ku Japan mu 1912 ndi anzake ena, ankakwera njinga zimenezi.

Njinga zamatayala atatu zinayamba kupangidwa ku Dhaka chakumapeto kwa m’ma 1930. Mosiyana ndi njinga zamatayala awiri zochita kukokedwa ndi anthu, njinga zamatayala atatuzi zinali zopalasa. Zimenezi zinkathandiza kuti azinyamula katundu ndi anthu mosavuta podutsa m’misewu yodzaza ndi magalimoto komanso anthu.

Amazikongoletsa Kwambiri

Pafupifupi njinga iliyonse ku Dhaka amaikongoletsa. Kodi luso limeneli linayamba bwanji? Pamene njingazi zimayamba ku Dhaka, zinkapikisana ndi ngolo zokokedwa ndi mahatchi, zomwe zinkatchedwa tomtom. Ngolo zimenezi zinkanyamulanso anthu ndi katundu. Pofuna kuti anthu azithamangira njingazi, eni ake anayamba kuzikongoletsa pojambula zinthu zosiyanasiyana.

Anthu akaona njingazi amachita nazo chidwi kwambiri. Munthu wina wa ku Bangladesh yemwe amadziwa zojambulajambula, dzina lake Syed Manzoorul Islam, ananena kuti munthu ukamaona njinga za ku Dhaka umakhala ngati wapita “kumalo oonetserako zojambulajambula.” Pafupifupi njinga yonse imakhala ndi zithunzi zosiyanasiyana. M’mbali mwake ndiponso pamwamba pake amakongoletsapo ndi tinsalu, timapepala ndiponso timikanda tosiyanasiyana.

Munthu aliyense amakongoletsa njingazi mmene iyeyo akufunira. Njinga zina zimaoneka ngati zikwangwani zoitanira malonda, ndipo zimakhala ndi zithunzi za ku India ndi ku Bangladesh zimene amaziona m’mafilimu. Zithunzi zimenezi zimasonyeza moyo wakumudzi ndiponso zochitika zandale. Ambirinso amakonda kujambula nyama, mbalame, anthu akusaka, ndiponso malo okongola a kumudzi.

M’zaka za m’ma 1950, ku Bangladesh kunali anthu ochepa odziwa kukongoletsa njingazi. Masiku ano, kuli anthu 200 kapena 300 amene amagwira ntchito imeneyi. M’dzikoli muli malo amene amalumikizirako njingazi, ndipo zitsulo zake zimapangidwa kuchokera ku zitsulo zimene zinagwiritsidwa kale ntchito. Mwachitsanzo, amatha kugwiritsa ntchito mgolo kapena zinthu zina zimene zinatayidwa. Kenako amazipenta bwinobwino kuti zioneke zokongola. Anthu ambiri ku Bangladesh luso lawo ndi limeneli ndipo njingazi zangokhala ngati chizindikiro cha dziko lawo.

Anthu Oyendetsa Njingazi

Mungaone kuti kuyendetsa njinga zimenezi si ntchito yamasewera. Tsiku lonse amakhalira kupalasa njinga yodzaza katundu ndi anthu. Anthu amene amakonda kukwera njingazi ndi amayi, ana a sukulu, ndiponso amalonda. Nthawi zambiri, njingazi zimanyamula anthu awiri kapena kuposa pamenepa. Zimanyamulanso matumba a mpunga, mbatata, anyezi, ndi zinthu zina zokagulitsa kumsika. Anthu okwera amatha kukhala pamwamba pa katundu wawo. Mungaone kuti n’zovuta kuti munthu ayendetse katundu wolemera choncho. Koma anthu amenewa amagwira ntchito mwakhama popanda kudandaula ngakhale kunja kukutentha kwambiri kapena kukugwa mvula.

Anthu ambiri amene amayendetsa njingazi amachokera m’madera osauka a kumudzi. Anthuwa amasiya mabanja awo n’kubwera ku Dhaka kudzafuna ntchito. Akalephera kupeza ntchito yabwino, amangoyamba ntchito yopalasa njinga. Ngakhale kuti ntchitoyi ndi yokhetsa thukuta, iwo amapeza ndalama zochepa.

Kuyenda Panjingazi N’kosangalatsa

Njingazi zikupitirizabe kuchuluka ku Dhaka chifukwa chakuti kulibe zitunda zambiri, ndiponso zimafika malo ambiri amene galimoto sizingafike. Anthu ambiri amakonda kukwera njingazi chifukwa chakuti siziwononga chilengedwe komanso n’zosangalatsa kukwera.

Komabe m’mizinda yambiri ku Asia, chiwerengero cha njingazi chikuchepa chifukwa anthu ambiri akukonda kukwera galimoto ndiponso akuona kuti kukwera njingazi n’kwachikale. Koma anthu opanga njingazi akuyesetsa kuti zisathe ndipo akupanga zina zooneka zamakono.

Mukamayenda mumzinda wa Dhaka, mutha kukwera basi, galimoto kapena njinga yamoto. Koma mutakwera njingazi, mungasangalale kwambiri ndipo ulendo wanu ungakhale wosaiwalika.

[Chithunzi chachikulu patsamba 23]