Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizani Ana Anu Kuti Akule Bwino

Thandizani Ana Anu Kuti Akule Bwino

Thandizani Ana Anu Kuti Akule Bwino

YOLEMBEDWA KU CANADA

▪ Nkhani ina ya mu nyuzipepala ya New York Times inanena kuti: “Ana angaphunzire zambiri chifukwa choonera TV. Komabe, kungokhala pansi n’kumaonera TV kwa maola ambiri kukuwononga ana.” Izi zili choncho chifukwa zimachititsa anawo kuti asakhale ndi luso lochita zinthu, kuphunzira ndiponso kucheza ndi anzawo.

Nyuzipepalayi inanena kuti akatswiri a pachipatala cha ana ku Seattle, mu mzinda wa Washington, ku U.S.A., anachita kafukufuku pa ana 2,500 amene amakonda kuonera TV. Ndipo “anapeza kuti ana a chaka chimodzi mpaka zaka zitatu akamaonera kwambiri TV amavutika kuphunzira zinthu akafika zaka 7.” Ana otere amakhala aukali, amafuna zinthu zichitike panthawi imene iwo akufuna ndiponso sachedwa kutopa akamaphunzira. Mogwirizana ndi zimene ananena mphunzitsi wina dzina lake Dr. Jane M. Healy, “makolo ambiri amene ana awo anapezeka ndi vuto losatha kumvetsera zinthu nthawi yaitali, anaona kuti vutoli linachepa ataletsa anawo kuonera TV.”

Kodi makolo angatani kuti achepetse nthawi imene ana awo amaonera TV? Akatswiri ofufuza aja anati: Muziikira ana malire a nthawi yoonera TV. Musamagwiritse ntchito TV ngati cholerera ana. M’malomwake muziwapatsa ana anu zochita zokwanira. Muzisankha mapulogalamu oti ana anu aonere, ndipo muzithimitsa TV mapulogalamuwo akangotha. Ngati zingatheke, muzionera pamodzi ndi ana anu ndipo mukatha muzikambirana zimene mwaonera. Ndiponso inuyo chepetsani nthawi imene mumaonera TV.

Pamafunika nthawi, kudzipereka komanso kudziletsa, kuti muthandize ana anu kukhala ndi luso lochita zinthu ndiponso locheza ndi anthu. Koma mukayesetsa kuchita zimenezi, ana anu amakula bwino. Zimenezi ndi zoona chifukwa mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miyambo 22:6) Mbali yaikulu ya kuphunzitsa kumeneku ndi kuthandiza ana anu kukhala ndi makhalidwe abwino.

Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso pophunzitsa ana awo makhalidwe abwino. Makolo akamaphunzitsa ndiponso kuyang’anira bwino ana awo ali aang’ono, anawo amakula bwino. Makolo amasangalala kwambiri ana awo akakula ndi makhalidwe abwino ndiponso akakhala odalirika.