Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mlomo wa Mbalame Yotchedwa Toucan

Mlomo wa Mbalame Yotchedwa Toucan

Panagona Luso!

Mlomo wa Mbalame Yotchedwa Toucan

▪ Mbalame ya toucan, imene imapezeka ku Central ndi ku South America, siikonda kuuluka ndipo imadalira kudumpha. Mbalame zina zamtunduwu zikamalira, mawu ake amafanana ndi a chule, koma ndi aakulu moti amatha kumveka m’nkhalango pamtunda wa pafupifupi kilomita imodzi. Koma mwina chimene asayansi amadabwa nacho kwambiri ndi mbalameyi, ndi mlomo wake.

Taganizirani izi: Mlomo wa mbalame zina zamtunduwu ndi wautali pafupifupi theka la utali wa mbalame yonseyo. Umaoneka ngati wolemera kwambiri, koma si choncho. Katswiri wina wa sayansi, dzina lake Marc André Meyers, anati: “Kunja kwa mlomowu kunapangidwa ndi puloteni yotchedwa keratini imene imapezekanso m’zikhadabo ndi m’tsitsi. Khungu la mlomowu lili ndi tizinthu ting’onoting’ono tamabokosimabokosi toyalana ngati matailosi padenga.”

Mlomo wa mbalameyi umakhala ngati chinkhupule cholimba kwambiri. Mbali zina zili ndi mphako, pamene mbali zina zili ndi khungu komanso zochirikizira. Chifukwa cha zimenezi, mlomowu ndi wopepuka koma wolimba kwambiri. Meyers anati: “Zikukhala ngati mbalame ya toucan ili ndi luso la zopangapanga.”

Kapangidwe ka mlomo wa mbalameyi kamaithandiza kuti isavulale ngakhale itamenyetsa mlomowu pazinthu zolimba. Asayansi amakhulupirira kuti akatswiri opanga ndege ndi galimoto atatengera kapangidwe ka mlomo wa mbalameyi, angamapange zinthu zabwino kwambiri. Meyers anati: “Ngati mbali zina za galimoto atamazipanga motengera kapangidwe ka mlomo wa [mbalameyi] zingateteze kwambiri oyendetsa galimoto patachitika ngozi.”

Ndiyeno kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika kuti mlomo wa mbalame ya toucan ukhale wolimba koma wopepuka? Kapena kodi pali amene anaupanga?

[Chithunzi patsamba  17]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mphako

Mbali yooneka ngati chinkhupule