Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
▪ Anthu ambiri amaganiza kuti kukanakhala kuti kunja kuno kuli Mulungu, sakanalola kuti anthu azivutika kwambiri ngati mmene akuvutikira panopo. Funso limene anthu ambiri amafunsa ndi loti, “Mulungu anali kuti pamene tinkafuna kuti atithandize?” M’mbiri yonse ya anthu, anthu ambiri avutika koopsa, mwina kufa kumene chifukwa chozunzidwa.
Komabe, kulinganizidwa ndi kupangidwa bwino kwa zinthu zamoyo ndi umboni wabwino woti kunja kuno kuli Mlengi. Kodi Mulungu amene amatisamalira angalole bwanji zinthu zoipa choncho kuchitika? Kuti tipembedze Mulungu moyenera, tiyenera kupeza yankho lokhutiritsa la funso lofunika limeneli. Kodi tingalipeze kuti?
Tikukupemphani kuti mupeze kabuku kakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Tikukhulupirira kuti mukawerenga mosamala mitu yakuti “Chifukwa Chake Mulungu Walola Kuvutika” ndi “Kodi N’chiyani Chakhala Chotulukapo Chachipanduko?” mupeza mayankho okhutiritsa.
Ngati mukufuna kuitanitsa kabukuka, lembani zofunika m’mizere ili panoyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.