Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zithunzi Zokongola Kwambiri Zamiyala

Zithunzi Zokongola Kwambiri Zamiyala

Zithunzi Zokongola Kwambiri Zamiyala

YOLEMBEDWA KU ITALY

PANJIRA zonse zojambulira zithunzi, njira yovuta kwambiri ndi imene imagwiritsidwa ntchito ku mzinda wa Florence, m’dziko la Italy. Kumeneku amajambula zithunzi pogwiritsa ntchito miyala, matailosi kapena magalasi. Zinthu zimenezi amayamba azidula kaye kuti zigwirizane ndi mmene akufunira. Ndipo nthawi zambiri miyalayi imadulidwa mwaluso kwambiri moti akailumikiza, munthu sangathe kudziwa molumikizira mwake.

Ojambula zithunzi zimenezi amakhala ndi miyala yamitundumitundu. Amakhala ndi miyala ina yonyezimira ya mwina mwa buluu komanso mwina moyera. Pali miyala ina ya timizere tobiriwira, ina imakhala yokongola kwambiri chifukwa imakhala yamitundumitundu yokhala ndi mwina mwa chikasu, modera, mobiriwira ndi mofiira. Miyala ina imakhala yonyezimira kwambiri ndipo amagwiritsa ntchito miyala imeneyi pojambula malo a miyala, a chilengedwe, madzi kapena mitambo.

Kujambula zithunzi mwa njira imeneyi kunayamba kale kwambiri. N’kutheka kuti kunayambira ku Near East, ndipo kunafika ku Roma cha m’ma 100 B.C.E. Panthawiyo, imeneyi inali njira yofala yokongoletsera m’nyumba. Ngakhale kuti kale kwambiri lusoli linkapezeka m’madera ambiri, anthu a m’tauni ya Tuscan, m’mzinda wa Florence ndi amene anachititsa kuti luso limeneli litchuke kwambiri kuyambira m’ma 1500 C.E. Masiku ano zithunzi zokongola za ku Florence zimapezekabe ku Ulaya m’nyumba za mafumu ndiponso m’nyumba zosungira zinthu zakale.

Kupanga zithunzi zamiyala ndi ntchito yaikulu kwambiri. Magazini ina inanena kuti nthawi imene amathera popanga “chithunzi, ngakhale chaching’ono, imakhala yochuluka kwambiri moti anthu ofufuza za nthawi imene anthu amathera pantchito inayake ingawadabwitse kwambiri.” N’chifukwa chake masiku ano, monga zinalili kale, zithunzi zimenezi n’zodula moti ambiri sangakwanitse kugula.

Kodi Zimapangidwa Bwanji?

Wopanga zithunzi zamiyala amayamba ndi kujambula chithunzi choonerapo. Ndiyeno amadula chithunzi choonerapochi mogwirizana ndi mmene chidzaonekere. Zikatere wojambula chithunziyo amasankha mwala woyenera mbali iliyonse ya chithunzicho. Posankha miyalayi satengera ndendende mmene chithunzi choonerapocho chikuonekera. Kenako zidutswa za chithunzi choonerapo chija amazimata ku mwala umene wasankha kugwiritsa ntchito pambali imeneyo.

Kenako wojambula chithunziyo amapanitsa mwala uliwonse, umene umakhala wa mamilimita awiri kapena atatu, ku chinthu chopanira. Ndiyeno amadula mwalawo mosamala pogwiritsa ntchito kachipangizo kodulira (monga tikuonera pachithunzi pamwambapa). Akamadula amathira mankhwala enaake ku choduliracho. Akatero amapala bwinobwino mbali zimene wadulazo kuti akazilumikiza, polumikizirapo pasaoneke. Tangoganizani mmene zimavutira popanga tizidutswa ting’onoting’ono ta nthambi ya mtengo.

Tizidutswati amatiyala pa chinthu chinachake changati nsalu, n’kutiwalitsa kuti chithunzicho chioneke bwino kwambiri. Ndipo chithunzichi chimaoneka bwino kuposa chojambulidwa ndi kamera. N’zodabwitsa mmene ojambula zithunzi zimenezi amagwiritsira ntchito miyala popanga zinthu zokongola kwambiri ngati maluwa. Zina mwa zinthu zimene ojambulawo amapanga ndi monga zipatso, moika maluwa, agulugufe, mbalame ndiponso maonekedwe a malo enaake.

Chochititsa chidwi kwambiri ndi luso limeneli n’chakuti, ojambulawo sadziwa zonse zokhudza zithunzi zawozo. Iwo amangogwiritsa ntchito miyala yamitundumitundu imene Mulungu analenga. Pamfundo imeneyi buku lina linati: “Miyala ing’onoing’ono imeneyi imasonyeza kukongola kwa zinthu zimene zili m’chilengedwechi, ndipo nthawi zonse imatikumbutsa za Mlengi wathu.”

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

All photos pages 16 & 17: Su concessione del Ministero per i Beni e le Attività Culturali-Opificio delle Pietre Dure di Firenze, Archivio Fotografico