Kuchokera kwa Owerenga
Kuchokera kwa Owerenga
Sindinenso Kapolo wa Mowa (May 2007) Mboni zikandibweretsera magazini, nthawi zina ndimawawerenga. Ndimaona kuti nkhani zake zimakhala zabwino poyerekezera ndi nkhani zoipa zimene timaona pa TV ndiponso zimene timawerenga m’nyuzipepala. Ine sindinakhalepo ndi vuto lomwa mowa mwauchidakwa, koma ndili ndi achibale ndi anzanga amene ali ndi vuto limeneli. Munthu amene anafotokozedwa m’nkhaniyi ananena kuti anathetsa vuto lomwa mowa mwauchidakwa m’miyezi itatu yokha. Zimenezi zinachitika munthuyu atakhala ndi vutoli kwa zaka zambiri. Ngakhale ndikumuthokoza pa zimene anachitazi, ndikukayikira ngati zimenezi ndi zenizeni komanso ndikuganiza kuti sangalimbikitse ena amene akulimbana ndi vuto limeneli. Munthu yemwe alidi ndi vutoli nthawi zambiri samalithetsa kamodzinkamodzi.
G. A., United States
Yankho la “Galamukani!”: Sitinatanthauze kuti n’kosavuta kuthetsa vuto la kumwa mowa mwauchidakwa. Tikudziwa kuti anthu amene akufuna kuthetsa vutoli samalithetsa kamodzinkamodzi ndipo pamakhala zinthu zina zowalepheretsa. Ngakhale anthu amene angathetse vutoli kamodzinkamodzi, amafunika kusamala kuti asayambirenso. N’chifukwa chake nkhaniyi inanena kuti, “kapolo wa mowa” atatha zaka 10 osamwa anati: “Ambiri sadziwa nkhondo yaikulu imene ndili nayo kuti ndikangomwa botolo limodzi lokha, nditha kuyambiranso moyo wanga wakale. Chilakolako cha mowa ndikadali nachobe. Kuti ndikane mowa, ndimafunika kupemphera kwambiri ndiponso kulimba mtima.” Anthu ambiri athetsa vutoli mwa kudalira Mulungu.—Salmo 55:22.
Kodi Tiyenera Kukhulupirira Baibulo? (November 2007) Ndili ndi zaka 12, ndipo ndikufuna ndikuthokozeni kwambiri chifukwa cha nkhani yosangalatsa komanso mfundo zabwino za m’magazini yapadera ya Galamukani! Ndinasangalala kwambiri ndi mfundo za patsamba 7 zosonyeza kugwirizana kwa nkhani za m’Baibulo. Mfundo zina zimene zinafotokozedwa m’nkhaniyi zinali zachilendo kwambiri kwa ine. Ndipo ndikuyembekezera mwachidwi magazini ina yapadera.
D. F., United States
Zoti Muganizire Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cha kalembedwe katsopano ka Galamukani! Mafunso amene akumakhala ku mapeto kwa nkhani zina andithandiza kwambiri. Andithandiza kuti ndizitha kukumbukira ndi kusinkhasinkha zimene ndawerenga. Masiku ano, timakhala ndi zochita zambiri moti powerenga tingaphonye mfundo zofunika ndi zolimbikitsa.
M.A.S., Brazil
Kodi Imfa ndi Mapeto a Zonse? (December 2007) Miyezi 6 yapitayi mayi anga anamwalira pangozi. Nkhaniyi inandilimbikitsa kwambiri chifukwa inawonjezera chikhulupiriro changa kuti ndidzawaonanso akadzaukitsidwa. Ndikukuthokozani kwambiri.
L.L.R., Brazil
Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Ndizitsatira Mfundo za M’Baibulo Chifukwa Chiyani? (November 2007) Ndinkaganiza kuti sikulakwa kukhala ndi chibwenzi malinga ngati sitikugonana. Koma sindimakhutira kumangocheza ndi bwenzi langalo. Ndinayamba kukhala ndi zilakolako zoipa. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cholemba nkhani za m’Baibulo zimenezi mwa njira imene achinyamata amene sadziwa zinthu zambiri angamve mosavuta.
E.F., Japan