Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Pa zaka 20 zapitazi, masoka achilengedwe awonjezereka kuwirikiza kanayi. Anthu oposa 250 miliyoni amakhudzidwa chaka chilichonse.—EL UNIVERSAL, MEXICO.

“Kwa zaka zambiri ndithu, mphepo zimene zimawomba kunyanja yamchere ya Pacific zasonkhanitsa mulu waukulu wa zinyalala womwe ukuyandama panyanja.” Dera limene lili ndi zinyalalazi lakula kufika pa saizi ya Australia.—LA DÉPÊCHE DE TAHITI, TAHITI.

Kuti apange mafuta a galimoto yaing’ono okwana malita 50 ochokera ku zomera, pamafunika chimanga cholemera makilogalamu 200. Chimanga chimenechi “n’chokwanira kudya munthu mmodzi chaka chonse!”—GAZETA WYBORCZA, POLAND.

Mabaibulo Akufalitsidwa ku China

Mkulu wa Bungwe la Boma Loona za Chipembedzo ku China, dzina lake Ye Xiaowen, anati: “Dziko la China ndi limodzi mwa mayiko amene akufalitsa Mabaibulo ochuluka padziko lonse.” Kampani ina yosindikiza mabuku ya ku China imene ili ku Nanjing, likulu la Chigawo cha Jiangsu, tsopano yasindikiza Mabaibulo athunthu 50 miliyoni, ndipo n’koyamba kukwanitsa chiwerengero chimenechi m’dzikolo. Malinga ndi nyuzipepala ina, “m’zaka zaposachedwapa, Mabaibulo pafupifupi 3 miliyoni akhala akusindikizidwa ndi [kampaniyi] pachaka.” (People’s Daily Online) Malipoti akuti chiwerengero cha anthu amene akuti ndi Akhristu chikuwonjezereka ku China.

Anthu Akuba Zithunzi za Chipembedzo

Magazini ina inati: “Pa zaka zisanu zapitazi, matchalitchi oposa 1,000 akhala akuthyoledwa ndi akuba ku Russia.” (Russky Newsweek) Unduna wa za M’dziko wa ku Russia wakhala ukulandira malipoti akuti zithunzi pafupifupi 40,000 zabedwa. Panopa, undunawu ndi a Tchalitchi cha Orthodox agwirizana zakuti aziika chizindikiro chapadera pa zithunzi zonse. Chizindikirocho chizioneka pokhapokha atachiunika mwapadera. Zimenezi zizithandiza ofufuza kudziwa eni ake a zithunzi zimene zapezeka. Malinga ndi magazini ija, Ansembe a ku Moscow avomereza zimenezi “chifukwa chakuti chizindikiro ‘chapadziko lapansicho’ sichingasokoneze mphamvu ya zithunzizo yochita zozizwitsa.”

Nkhondo Zawononga Chuma cha mu Africa

Nyuzipepala ina inati: “Pakati pa 1990 ndi 2005, mayiko 23 mu Africa anali pa nkhondo, ndipo nkhondozo zinawonongetsa ndalama zokwana madola pafupifupi 300 biliyoni a ku United States.” (International Herald Tribune) Pulezidenti wa ku Liberia, Ellen Johnson-Sirleaf anati: “Ndalama zimene zinawonongeka zikanathandiza pa ntchito yolimbana ndi kachilombo ka HIV komanso matenda a Edzi mu Africa, kapena kutukula maphunziro, kubweretsa madzi abwino ndiponso kupewa ndi kuchiza TB ndi malungo. Tikanatha kumanga zipatala zambirimbiri, sukulu ndi misewu.” Pomaliza, nyuzipepepalayo inanena kuti popanda nkhondo, dera la Africa “likanakhala lotukuka kwambiri, osati losaukitsitsa.”

Kugona Pang’ono Masana Kungakuthandizeni

Pakafukufuku amene anachitika pa amuna ndi akazi a ku Greece oposa 23,000, anapeza kuti kugona pang’ono masana kosachepera katatu pamlungu, kungachepetse ndi 37 peresenti imfa zobwera chifukwa cha matenda a mtima. Dimitrios Trichopoulos, katswiri wa kafukufuku yemwenso ndi katswiri wofufuza chiyambi ndi kufalikira kwa matenda, pa Harvard School of Public Health ku U.S.A., anati: “Pali umboni wochuluka wakuti kupanikizika kwambiri komanso kosatherapo kungayambitse matenda a mtima. Koma katulo pang’ono masana kangathandize kuchepetsa kupanikizika ndi imfa zobwera chifukwa cha matenda a mtima.”