Mwendo wa Mbalame Yotchedwa Seagull
Panagona Luso!
Mwendo wa Mbalame Yotchedwa Seagull
▪ Mbalame imeneyi sifa ndi kuzizira ngakhale itaima pa aisi popanda choteteza mapazi ake. Kodi mbalameyi imatani kuti thupi lake likhalebe lotentha? Mwa zina, chinsinsi chake chagona pa mitsempha yake imene imapatsirana kutentha ndi kuzizira.
Taganizirani izi: Mtsempha wonyamula magazi otentha umakhala pafupi ndi mtsempha wonyamula magazi ozizira. Ngati magaziwo akupita mbali imodzi, theka la kutentha ndi limene limapita kozizirako. Koma ngati magaziwo akupita mbali zosiyana, pafupifupi kutentha konse kumapita kozizirako.
Mitsempha ya m’miyendo ya mbalameyi imaziziritsa kwambiri magazi akamabwera ku mapazi mpaka kutsala pang’ono kuundana, ndipo kenako imatenthetsa magaziwo akamabwerera m’thupi. Ponena za mbalame za m’madera ozizira, katswiri wa mbalame Gary Ritchison anati: “Njira yopatsirana kutentha ndi kuzizira imeneyi ndi yothandiza kwambiri, ndipo panagona luso kwambiri mwakuti ngakhale anthu atengera luso limeneli. Iwo akuligwiritsa ntchito pa zomangamanga poopa kuwononga magetsi.”
Ndiyeno kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika kuti mbalameyi izigwiritsa ntchito njira yopatsirana kutentha ndi kuzizira m’miyendo yake? Kapena kodi alipo amene anaipanga? *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Njira yopatsirana kutentha ndi kuzizira imeneyi imapezekanso mwa anthu, m’mitundu ina ya nsomba ndi nyama zina zambiri.
[Zithunzi patsamba 25]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Mitsempha ya m’miyendo ya “seagull” imatenthetsa magazi obwerera m’thupi
[Diagram]
32°C
0-5°C
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Seagull: © Michael S. Nolan/age fotostock