Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Mfundo 7 Zolerera Bwino Ana (August 2007) Magaziniyi inali yankho la mapemphero anga. Ndili ndi mwana wamkazi wazaka zinayi yemwe amakonda Yehova, koma ndimachita mantha kuti mwina sindingakwanitse kumulera bwino. Choncho, ndimapempha Yehova tsiku lililonse kuti andithandize kumuphunzitsa. Zikomo kwambiri chifukwa chotiganizira makolofe.

Y.M.A., Mexico

Nkhani zimenezi zinali ngati buku lamalangizo lolembera banja lathu, ndipo zinafotokoza zinthu zambiri zimene zakhala zikundivutitsa maganizo. Nkhanizi zinandipatsa umboni winanso wosonyeza mmene Yehova amasamalira anthu ake. Iye wamva mapemphero anga ndipo waona misozi yanga, komanso akudziwa kuti ndimafunikira kwambiri zimenezi.

J. M., United States

M’masamba ochepa chabe, munafotokoza mfundo zofunika kwambiri ndi malangizo othandizadi. Ifeyo tikungofunikira kutsatira malangizowo.

E. L., Finland

Munthu Wosangalala—Kodi Amakhaladi ndi Thanzi Labwino? (September 2007) Nkhani imeneyi inandithandiza kwambiri, chifukwa chakuti nthawi zambiri ndakhala ndikudziimba mlandu chifukwa cha mavuto amene ndinakumana nawo. Ndinafika poganiza kuti ndine mayi wolephera, ndipo ndinali wopanikizika kwambiri. Ngakhale kuti zimandivuta kukhalabe wosangalala, nkhani imeneyi inandithandiza kuchepetsa nkhawa. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa chotiganizira potipatsa nkhani ngati imeneyi.

A. S., Ecuador

Mano Akhala Akuvutitsa Anthu Kuyambira Kalekale (September 2007) Ndine dokotala wamano ndiponso mphunzitsi wa zamano. Ndinachita chidwi kwambiri ndi nkhani yanu yolembedwa bwino ndiponso yosangalatsa. Nkhani yanu inafotokoza mwachidule koma momveka bwino mbiri ya ukatswiri wa zamano. Nkhani imeneyi ndaisonyeza kwa anzanga komanso ogwira nawo ntchito ambiri.

C. R., United States

Kodi Mulungu Ndiye Amawachititsa? (September 2007) Ine ndi anzanga ena tikamacheza, timakambirana njira zothandiza zokhudza mmene tingakonzekerere masoka. Pamene tikumwa zakumwa zoziziritsa kukhosi, timakambirana mfundo zothandiza m’bokosi lakuti “Kodi Ndinu Wokonzeka Kuthawa?” m’nkhani imene ndatchulayi, ndi kuona zinthu zofunika kutenga pakagwa tsoka zimene ena a ife takonzekera. Timakambirananso kuti m’pofunika kumaiona bwino nkhani yokonzekera masoka. Timadziwa kuti kusonkhanitsa zinthu zofunikira pakagwa tsoka si ntchito yathu yaikulu monga atumiki a Mulungu. Ntchito yathu yaikulu ndiyo kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kuuza ena kuti lonjezo la Mulungu losangalatsa ndi lakuti, padziko lapansi sipadzakhala masoka alionse, kaya achilengedwe kapena ochititsidwa ndi anthu.

R. G., United States

Tetezani Ana Anu! (October 2007) Ndili mwana, ndinagwiriridwapo. Mpaka pano, sindikwanitsa kuuza makolo anga zimene zinachitika. Choncho nkhani zimenezi zinanditonthoza kwambiri. Ndikukhulupirira ndi mtima wanga wonse kuti makolo awerenga magazini imeneyi ndi kuteteza ana awo. Ndikuthokoza kwambiri Yehova potipatsa mfundo zofunikirazi. Zinali zotonthoza kwambiri kwa ife amene tinagwiriridwapo.

R. I., Japan