Kuchokera kwa Owerenga
Kuchokera kwa Owerenga
Chikhulupiriro cha Mwana (August 2006) Ndikuyembekezera kudzaona Dustin, ndi anthu enanso ambiri amene anamwalira, akuthamangathamanga ndi kudumphadumpha ndi nyonga zawo zaunyamata m’dziko latsopano limene likubwera posachedwa.
A. A., Sri Lanka
Ndinachita chidwi kwambiri ndi chikhulupiriro cha Dustin ndi kulimba mtima kwake. Nkhani yake yandithandiza kuunikanso mmene ndimaonera choonadi pamoyo wanga ndiponso kuika zinthu zofunika patsogolo. Tsopano ndadziwa kuti kukhala pa ubale wolimba ndi Yehova komanso kuika zinthu za Ufumu patsogolo ndi kofunika kwambiri.
M.C.V., Brazil
Ndinakhudzidwa mtima kwambiri ndi mmene Dustin ankakondera choonadi. Zochita zake zinasonyeza kuti anali ndi mtima wofuna kukondweretsa Yehova ndi kuthandiza ena. Inenso, mofanana ndi Dustin, ndikufuna ‘kuthamanga panjirayo mpaka pomalizira pake ndi kusunga chikhulupiriro.’
M. N., Japan
Ndili ndi zaka 7. Zikomo kwambiri chifukwa cholemba nkhani imeneyi. Ndinachita chidwi ndi chikhulupiriro cholimba chimene Dustin anali nacho mwa Yehova, ngakhale kuti anali ndi matenda oopsa. Nkhani yake yandilimbikitsa kutumikira Mulungu ndi mtima wanga wonse.
T. D., Italy
Dongosolo Lodabwitsa la Zomera (September 2006) Ndinawerenga nkhaniyi mwachidwi kwa ola limodzi ndi theka. Ndi nkhani yophunzitsa kwambiri! Ndinajambulanso zithunzi zanga kuti ndiimvetse. Koma ndikufuna kukudziwitsani kuti fulakishoni ya 13/21 siimira nambala ya kupendekeka kwapadera. Nambala imene imaimira kupendekeka kwapadera ndi madigiri 222.5.
L. C., United States
Yankho la “Galamukani!”: Owerenga ambiri ananena zoona kuti kupendekeka kwapadera ndi pafupifupi madigiri 222.5. Nanga n’chifukwa chiyani nkhani yathu inanena kuti kupendekeka kwapadera ndi madigiri 137.5? Pa Intaneti, danga lakuti MathWorld limati: “Kupendekeka kwapadera ndi kupendekeka kumene kumagawa mwapadera madigiri 360 pawiri kukhala 137.5 ndi 222.5 (gawo lake linalo silikwana madigiri 180°).” Pofotokoza chifukwa chake akatswiri a masamu ndi a sayansi amawerenga kupendekeka kwapadera mwanjirayi, katswiri wa masamu wa ku Britain, Dr. Ron Knott, anati: “Timakonda kutenga gawo laling’ono la kupendekekako.” Choncho, ngakhale kuti nambala ya 13/21 (yoposa madigiri 180) ndi fulakishoni ya kupendekeka kwapadera, koma madigiri 137.5 (osakwana madigiri 180) ndi amene amaimira kupendekeka kwapadera.
“Anaikidwa M’ndende Chifukwa cha Chikhulupiriro Chawo” (April 2006) Ngakhale kuti sindine wa Mboni za Yehova, ndimalemekeza kwambiri anthu a chipembedzo chanu. Ndinakumana ndi Mboni zambiri ndili kundende zozunzirako anthu ku Gross-Rosen ndi Buchenwald. Izo zinali ndi khalidwe labwino ndipo chikhulupiriro chawo chinali cholimba kwambiri moti akaidi ambiri ankazilemekeza ndi kuzisirira. Ngakhale asilikali a SS ankachita nazo chidwi. A Mboni muzibwera nthawi ina iliyonse kunyumba kwanga.
P. V., United States