Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akatswiri Ochapa Zovala ku Abidjan

Akatswiri Ochapa Zovala ku Abidjan

Akatswiri Ochapa Zovala ku Abidjan

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU CÔTE D’IVOIRE

TSIKU lina tikulowera ku madzulo kwa mzinda wa Abidjan m’dziko la Côte d’Ivoire, tinasangalala kuona ndi kumva zochitika m’mzinda wa kumadzulo kwa Africa umenewu. Ndipo mwadzidzidzi tinaona zochititsa chidwi. Tinaona zovala zambiri zamitundu yosiyanasiyana zokongola zitayanikidwa mu udzu. Kodi n’chifukwa chiyani zovalazi zinayanikidwa kumeneko? Anzathu a komweko anatiuza chifukwa chake. Anati imeneyi ndi ntchito ya a fanico.

A fanico ndi gulu la akatswiri ochapa zovala. Kuyambira m’mawa mpaka madzulo, amuna ambirimbiri ndi akazi owerengeka amphamvu amagwira ntchito yochapa zovala mumtsinje wa Banco. Dzina lakuti fanico limachokera ku mawu a Chidyula kapena Chijula akuti fani, kutanthauza “nsalu” kapena “zovala,” ndiponso ku mawu akuti ko, kutanthauza “kuchapa.” Choncho mawu a Chidyula akuti fanico amatanthauza “munthu wochapa zovala.”

Ntchito ya Akatswiriwa

Tsiku lina tinalawirira kupita kumene a fanico amachapa zovala kuti tikaone ntchito yawo yochititsa chidwiyi. Tinawapeza ali kalikiliki. Anali atayamba kale ntchito yawo. Mumtsinje wa Banco, womwe madzi ake ndi oderapo, munaikidwa matayala akuluakulu ndipo pakatikati pa matayalawo pali miyala. Patayala lililonse panali wochapa zovala, madzi akumulekeza m’ntchafu kapena m’chiuno, ndipo aliyense anali wotanganidwa kupaka sopo, kumenyetsa zovala pamwala ndi kuzitikita.

M’mawa dzuwa lisanatuluke, a fanico amayenda nyumba ndi nyumba kutolera zovala zakuda. Anthu ena amene amawachapira amakhala pa mtunda wa makilomita atatu kuchokera kumene amachapira zovalako. Amakoka zovala zonsezo pangolo kapena amazimanga pamodzi n’kuzisenza pa mutu, ulendo wa kumtsinje wa Banco. Akafika, anzake amamulandira ndi moni wa m’zilankhulo zosiyanasiyana za m’madera ambiri a mu Africa kumene ochapa zovalawo anachokera. Ena anachoka kwawo kalekale ndipo akhala m’derali zaka zambiri monga a Brama, munthu wamphamvu zake wa zaka zoposa 60. A fanico amagwira ntchito tsiku lililonse kupatulapo masiku atatu okha pachaka.

Kuchapa zovalazo ndi ntchito yaikulu kwambiri. Tinaona munthu wina akutula zovala zoti achape koma zinali zambiri moti amayi ambiri sangakwanitse kuzichapa. Anamasula zovalazo ndi kuyamba kunyika m’madzi chovala chilichonse. Kenako, anapaka zovalazo sopo ndi kuyamba kumenyetsa chimodzi ndi chimodzi pamwala. Nthawi zina ankagwiritsa ntchito bulashi pochapa zovala zakuda kwambiri. Kodi amalandira ndalama zingati akachapa zovala? Amalandira pafupifupi 10 kwacha malaya amodzi kapena 20 kwacha nsalu yofunda imodzi. N’chifukwa chake a fanico amachapa zovala zambiri kuti apeze ndalama zokwanira.

Mukanaona mulu wa zovala zimene amachapa, mukanadabwa kuti ‘Kodi amakumbukira bwanji mwini wa chovala chilichonse?’ Gulu linalake la ochapa zovala ku India limaika zizindikiro zodziwa okha pazovala ndipo ife tinkaganiza kuti mwina nawonso amatero. Koma njira yodziwira zovala imene a fanico amagwiritsa ntchito ndi yabwinonso, ngakhale kuti ndi yosiyana kwambiri ndi ya anzawo a ku India.

Munthu amene anatiperekeza anatifotokozera bwino njira imene a fanico amagwiritsa ntchito kuti asasokoneze zovala. Akamatolera zovala, amaona msinkhu wa munthu aliyense m’banja kuti adziwe mwini wa chovala chilichonse. Saika chizindikiro chilichonse pazovalazo. Koma amamanga mfundo chovala chilichonse chochokera banja limodzi pamalo ofanana. Mwachitsanzo, amamanga mfundo zovala za banja lina pamkono wakumanzere, lina mkono wakumanja, lina m’kolala, ndi linanso m’chiuno. Akamachapa amaonetsetsa kuti zovala za banja lililonse zili pamodzi. Ife tinkaonabe kuti n’zovuta kukumbukira. Choncho tinafunsa munthu wina wa m’gululi ngati anasokonezapo chovala. Kudabwa kwake kunangotipatsa yankho lakuti, Ayi, a fanico sasokoneza zovala!

Kodi munthu wina aliyense angangobwera ndi kuyamba kuchapa nawo zovala mumtsinje wa Banco? N’zosatheka! Pali ndondomeko yofunika kutsatira. Munthu akafuna kuyamba kuchapa nawo zovala, amamuyesa kaye miyezi itatu uku akuphunzitsidwa ndi katswiri wodziwa ntchitoyi. Panthawi imeneyi ndi pamene amaphunzira luso lokumbukira zovala za anthu. Akalephera mayesowa, ndiye kuti walepheranso ntchito. Koma akakhoza, amalipira ndalama pang’ono kuti amam’patse malo akeake ochapirapo zovala.

Sopo Yochapira

Ntchito yochapa zovala singayende popanda sopo. Choncho, munthu akamaphunzira ntchitoyi amaphunziranso kugwiritsa ntchito bwino sopo. Sopo imeneyi imapangidwa kuchokera ku mafuta a mgwalangwa ndipo ilipo mitundu itatu. Zovala zosada kwambiri amachapira sopo yoyera ndi yachikasu, koma zovala zakuda kwambiri amachapira sopo yakuda. Mafuta a mgwalangwa ndi amene amachititsa kuti mitundu yonse ya sopoyi izioneka yodera. Popeza kuti wochapa zovala aliyense amagwiritsa ntchito pafupifupi mitanda 10 ya sopo patsiku, anthu opanga sopo apafupi amaonetsetsa kuti anthu ochapawa sopo isawathere.

Tinakaona malo ena aang’ono kumene amapanga sopoyo cha kuphiri pafupi ndi malo ochapirawo. Ntchito yopanga sopo imayamba 6 koloko mamawa. Nthawiyi ikamakwana, amakhala atagula kale zinthu zonse zopangira sopo monga mafuta oundana a mgwalangwa, mchere, madzi a mtengo wa m’gulu la mpoza, mafuta a koko ndi a kokonati. Zinthu zonsezi siziwononga chilengedwe. Popanga sopo amawiritsa zinthuzi m’mgolo pankhuni. Ataziwiritsa maola 6, amazithira m’tizikombole n’kudikira kuti ziume. Pakapita maola angapo, amadula sopoyo mitandamitanda.

Ndiyeno, opanga sopowo amasenza chibekete cha sopo pamutu n’kutsika phiri kukagulitsa kwa a fanico. Kodi amawapatsira bwanji sopoyo popeza kuti amakhala akuchapa mumtsinje? Iwo amalowa m’madzi momwemo ngakhale kuti madzi amafika mpaka m’chiuno. Kenako amayandamitsa chibekete chawo chapulasitiki pamadzi n’kumaperekera sopo kwa amene akufuna.

Akamaliza Kuchapa

A fanico akamaliza kuchapa, amakayanika zovalazo paudzu kapena pazingwe zawo m’mphepete mwa phiri. Zovala zimenezi ndi zomwe zinatichititsa chidwi poyambirira paja. Akamaliza kuyanika zovala, m’pamene amapeza nthawi yopuma pang’ono. Madzulo zovalazo zikauma, amazipinda bwinobwino, ndipo mwina zina amasita ndi simbi ya makala. Dzuwa likamalowa, amapakira zovala zoyera ndi zosita n’kukazipereka kwa eni ake.

Titaona zovalazi zitayanikidwa, sitinadziwe kuti pamakhala ntchito yaikulu. Choncho ndife osangalala kuti tinakaona a fanico ku Abidjan ndipo panopa tikutha kumvetsa ntchito yotamandika imene amuna ndi akazi ochapa zovala amagwira pa dziko lonse.

[Mapu patsamba 10]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

CÔTE D’IVOIRE

[Chithunzi patsamba 12]

Wopanga sopo akugulitsa mitanda ya sopo

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

PhotriMicroStock™/C. Cecil