“Mbalame ya Chinsansa” Mu Ngalande za ku Venice
“Mbalame ya Chinsansa” Mu Ngalande za ku Venice
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU ITALY
MBALAME imeneyi imayenda m’ngalande zokhala ndi makoma onyowa, milato yamiyala, ndi nyumba zamawindo okongola ndi makonde amaluwa. Ndi yakuda, yokongola, ndipo imayenda mwakachetechete. Imeneyi si mbalame yeniyeni, koma ndi bwato limene mumati mukalionera kutali, limaoneka ngati mbalame yakuda ya chinsansa. Ngakhale kuti bwatoli ndi lamatabwa ndipo khosi lake ndi lachitsulo ndiponso lopanda nthenga, limayenda mochititsa kaso ngati mbalame yokongolayo m’ngalande za mumzinda wa Venice, ku Italy. Bwato limeneli limatchedwa gondola, ndipo anthu ambiri amati ndilo lotchuka kwambiri padziko lonse. Kodi chiyambi cha bwatoli ndi chotani? N’chifukwa chiyani lili lotchuka kwambiri? Limasiyana bwanji ndi mabwato ena?
Chiyambi Chake
Ndi zovuta kudziwa kuti bwato loyamba la gondola linapangidwa liti, ngakhale kuti ena amati linapangidwa zaka za pakati pa 1000 ndi 1100 C.E. Linapezeka koyamba mu zithunzi zojambulajambula kumapeto kwa zaka za m’ma 1400. Komabe, munali cha m’ma 1600 ndi 1700 pamene anasintha kapangidwe kake kuti lizioneka losiyana ndi mabwato anzake komanso kuti likhale ndi maonekedwe amene
analitchukitsa. Bwato limeneli linali lophwatalala, koma analisintha m’zaka zimenezi kuti likhale lalitali komanso kuti kutsogolo kwake kukhale kwachitsulo.Ndi zovutanso kudziwa kumene kunachokera dzina lakuti gondola. Anthu ena amati dzina limeneli linachokera ku mawu achilatini akuti cymbula, omwe anali dzina la bwato laling’ono, kapena kumawu akuti conchula, amene ankawagwiritsa ntchito kuchepetsa mawu akuti concha, amene amatanthauza “chikamba cha nkhono.”
Mzinda wa Venice Umadziwika ndi Bwato Limeneli
Zimene tikudziwa ndi zakuti pali kugwirizana kwambiri pakati pa bwatoli ndi mzinda wa Venice. Ndipotu, anthu sangatchule Venice popanda kuganiza za bwatoli. Pazithunzi zambiri za Venice sipalephera kukhala bwato la gondola.
Palinso kugwirizana kwina pakati pa bwatoli ndi mzindawo. Roberto, amene amayendetsa gondola ndiponso amaperekeza alendo m’ngalande za ku Venice, amauza anthu kuti kuyenda m’ngalande mutakwera gondola “ndi njira yabwino yodziwira Venice. Simumangoona malo odziwika okha, mumafika podziwa mmenedi mzinda wa Venice ulili.” Mlembi wotchuka ku Germany, dzina lake Johann Wolfgang von Goethe, anati atakwera bwatoli anamva ngati “ndiye Mwini Nyanja ya Adriatic, mofanana ndi mmene nzika iliyonse ya Venice imamvera ikangokwera ndi kugona mu gondola yake.” Roberto akutinso: “Kuyenda pang’onopang’ono kwa gondola kumayenderana bwino ndi moyo wa ku Venice. Utatsamira mipando yawofuwofu, umaona ngati uli ndi nthawi yonse yochita chilichonse.”
Kudabwitsa Kwake kwa Gondola
Mukaona bwatoli, mungadabwe kuti limalunjika ku tsogolo bwinobwino ngakhale kuti lili ndi nkhafi imodzi yokha yomangiridwa mbali ya kumanja kwake. Mungaganize kuti popanda kumasinthasintha nkhafiyo, bwato lingamazungulire malo amodzimodzi, koma silitero ayi. Chifukwa chiyani? Gilberto Penzo, katswiri wa mbiri ya mabwato, analemba kuti: “Tikayerekeza bwatoli ndi thupi la munthu, diwa lake ndi fupa la msana, matabwa ake ndi nthiti, tinganene kuti gondola ili ngati munthu wodwala matenda opindika msana.” Kunena kwina, mbali ya kumanzere ndi yaikulu ndi masentimita 24 kuposa mbali ya kumanja. Choncho gondola ikamayenda, mbali ya kumanja imalowa kwambiri m’madzi kuposa mbali ya kumanzere. Kupendekeka kumeneku kumathandizira kuti bwato lizilunjikabe kutsogolo akamapalasa, ngakhale kuti wopalasayo amaimirira kumbali.
Mbali yapadera ya “chinsansa” chimenechi ndi khosi lake, kapena kuti kutsogolo kwake. Kupatulapo mbali ina ya kumbuyo, ndi mbali yokhayi imene ili yachitsulo. Mlembi wina, dzina lake Gianfranco Munerotto, anati mbali ya
kutsogolo imeneyi ndi “yochititsa kaso ndi yapadera kwambiri moti ukaiona koyamba, suiwala.” Poyamba, mbali yachitsuloyi inkathandizira kuti kutsogolo kuzilemera mofanana ndi kumbuyo kumene kumakhala munthu wopalasa. Koma masiku ano, chitsulocho chimangokongoletsa bwatolo. Anthu amati mano 6 akutsogolo kwake amaimira madera 6 a mzinda wa Venice, pamene dzino la kumbuyo kwa khosilo limaimira chilumba cha kumeneko cha Giudecca. Kupindika kwa khosilo konga S amati kumaimira ngalande yaikulu ya ku Venice komweko.Mbali ina yapadera ndi yakuti mabwatowo ndi akuda. Anthu amanena zifukwa zambiri pofotokoza chifukwa chake mabwatowo ali akuda. Ena amati, zaka za m’ma 1500 ndi 1600 nyumba ya malamulo ya ku Venice inkalipiritsa anthu amene ankapenta mabwato awo mowala kwambiri. Ankachita zimenezi kuti aletse anthu amene ankanyanyira kukongoletsa mabwato awo. Komabe, ambiri ankalolera kulipira ndalama m’malo mosiya kukongoletsa mabwato awo. Mapeto ake, panakhazikitsidwa lamulo lakuti mabwato onse a gondola aziwapaka penti yakuda. Enanso amati, mtundu wakuda unkasonyeza chisoni chimene anthu anali nacho chifukwa cha anthu zikwizikwi amene anafa ndi mliri wa makoswe. Ndiponso ena amati mabwato a gondola anali akuda kuti adona a ku Venice azioneka oyera kwambiri akakweramo. Koma chifukwa chake chenicheni si chapatali. Zoona zake ndi zakuti, kumayambiriro kwenikweni, mabwato a gondola anali akuda chifukwa chakuti ankawapaka phula lakuda kuti asamalowe madzi.
Tsopano mwamaliza kuyenda bwinobwino pamadzi odikha mutakwera chinsansa chakuda chimenechi, ndipo mukubwerera ku doko kumene munayambira ulendo wanu. Mutaimirira pa dokopo ndi kuponya maso anu kumene gondola ikupita, mwina maganizo angakupezeni akuti kodi bwanji chinsansa chija sikutembenuza mutu wake kuti chikonze nthenga zake zanyankhalala.
[Chithunzi patsamba 24]
Mbali ina ya gondola ndi yaikulu kuposa inzake
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
Kutsogolo kwake ndi kwapadera kwambiri
[Chithunzi patsamba 25]
Roberto, amayendetsa gondola m’ngalande za ku Venice
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
© Medioimages