Kodi Ndani Akudyerera Chuma cha Dzikoli?
Kodi Ndani Akudyerera Chuma cha Dzikoli?
DZIKO lonse latukuka kwambiri. Mwinatu zimakuvutani kukhulupirira zimenezi. Komatu dziwani kuti pali mayiko ena amene ndalama zawo zina amachita kusowa nazo chochita. Akuti ndalama zonse zimene mayiko anapeza m’chaka cha 2005 zinaposa madola 60 thililiyoni. Moti titati tigawe ndalamazi padziko lonse, munthu aliyense angalandire ndalama zokwana madola 9,000. Ndipotu ndalama zimenezi zikuchulukirachulukira.
Inde dzikoli lalemeradi. Komatu n’zodabwitsa kuti malingana ndi mmene linanenera buku laposachedwapa la United Nations, chuma cha anthu atatu olemera kwambiri padziko lonse n’choposa chuma chonse chimene mayiko 48 osauka amapeza pa chaka. Ndipo bungwe loona za chitukuko la UN Development Programme linati pafupifupi anthu 3 biliyoni ndi osauka kwambiri moti amachita kusowa ndi ndalama yasopo yomwe. Komanso anthu mamiliyoni ambiri akusowa chakudya ndi madzi abwino.
M’dziko la United States akatswiri akufufuza za gulu la anthu amene akuti “angathe kusauka nthawi ina iliyonse.” Ngakhale kuti dzikoli ndi lolemera, kuli anthu pafupifupi 50 miliyoni oterewa.
N’chifukwa chiyani padziko lonse pali anthu ankhaninkhani osauka pomwe ndalama zochuluka zedi zikulowa m’mabanki n’kumangounjikana? N’chifukwa chiyani anthu ambiri sakudyerera nawo chuma chochuluka cha padzikoli?
[Mawu Otsindika patsamba 3]
Chuma cha anthu atatu olemera kwambiri padziko lonse n’choposa chuma chonse chimene mayiko 48 osauka amapeza pa chaka
[Chithunzi pamasamba 2, 3]
Ana awa amawagwiritsa ntchito youmba zidina ndipo amawapatsa ndalama zokwana pafupifupi theka la dola patsiku
[Mawu a Chithunzi]
© Fernando Moleres/Panos Pictures
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
© Giacomo Pirozzi/Panos Pictures