Bwanji Ndimakomokakomoka?
Bwanji Ndimakomokakomoka?
Dokotala anakonzeka kuti andione m’maso. Kuti achite zimenezi anafunika kukhudza diso langa ndi zipangizo zake. Ndinadziwa chimene chichitike chifukwa zimandichitikirachitikira. Zimandichitikiranso nesi akandibaya kuti anditenge magazi. Nthawi zina zimandichitikiranso anthu akangolankhula za kuvulala. Ndimakomoka.
Malinga ndi nkhani ina imene inatuluka ku Britain, pafupifupi anthu 3 pa anthu 100 alionse amakomoka akakumana ndi zinthu zimene tazitchulazi. Ngati nanunso mumakomoka, mwina mwayeserapo kudziletsa kuti musamakomoke koma mumakomokabe. Mwinanso mwayeserapo kuthamangira ku bafa kuti anthu asakuoneni mukukomoka. Koma imeneyo si nzeru. Mutha kukomokera m’njira ndi kuvulala. Nditakomoka kambirimbiri, ndinati ndi bwino ndipeze chimene chikuchititsa.
Nditakambirana ndi dokotala womvetsa ndi kuwerengawerenga mabuku, ndinadziwa mtundu wa matenda anga. Matenda amenewa amatchedwa vasovagal reaction. Matendawa akuganiziridwa kuti amayamba chifukwa cha kusayenda bwino kwa magazi m’thupi. Kuyenda kwa magazi kumadalira zimene munthu akuchita, kaya wakhala pansi kapena waimirira.
Nthawi zina, akamakuunikani m’maso kapena mukaona magazi, thupi lanu limasokonekera. Limamva ngati mwagona pansi, pamene kwenikweni mwakhala pansi kapena mwaimirira. Poyamba, mtima wanu umathamanga chifukwa cha mantha. Kenako mwamsanga umayamba kugunda pang’onopang’ono. Mitsempha ya kumiyendo imakula ndipo magazi ambiri amathamangira ku miyendo pamene kumutu kumapita ochepa. Zikatero, magaziwo amapititsa mpweya wochepa kuubongo, choncho mumakomoka. Kodi mungatani kuti mupewe zimenezi?
Akamakutengani magazi, zingathandize kuyang’ana kumbali kapena kugona pansi. Monga tanenera kale, nthawi zambiri mumadziwa mukafuna kukomoka. Choncho, mumakhala ndi mpata wodziteteza kuti musakomoke. Madokotala ambiri amalimbikitsa kuti ndi bwino kugona pansi ndi kukweza miyendo yanu pampando kapena kukhoma. Zimenezi zimaletsa magazi kuthamangira ku miyendo, ndipo mwina vutolo silingapitirire mpaka kufika pokomoka. Zingangotenga mphindi zochepa chabe kuti muyambenso kumva bwino.
Ngati mfundo zimenezi zingakuthandizeni monga mmene zandithandizira, mudzatha kudziwa kuti mukufuna kukomoka. Kenako mungadziteteze msanga kuti musakomoke.—Nkhaniyi tachita kutumiziridwa ndi munthu wina.
[Mawu Otsindika patsamba 28]
Kugona pansi kungathandize