Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Buku Labwino Kwambiri Pophunzitsa”

“Buku Labwino Kwambiri Pophunzitsa”

“Buku Labwino Kwambiri Pophunzitsa”

Analemba mawu amenewa ndi mtumiki wa nthawi zonse wa Mboni za Yehova ku Panama. Anali kunena za buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Buku lokongolali lili ndi masamba 224 ndipo likugwiritsidwa ntchito kwambiri pophunzitsira anthu Baibulo. Iye analemba kuti: “Bukuli ndi losavuta kumva, lotsatirika bwino, ndi logwira mtima moti simungakhulupirire. Bukuli lili ndi njira yatsopano yogwiritsa ntchito mawu olozera zakumapeto. Anthu akangowerenga mawu amenewo, amafuna kufufuza ndi kudziwa zambiri.”

Mphunzitsi wa Baibulo ku Missouri m’dziko la United States anati: “Bukuli limandisangalatsa kwambiri chifukwa n’losavuta kumva. Nkhani zake zalembedwa motsatirika bwino kwambiri. Sindinaonenso!” Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani litangotuluka kumene, mphunzitsiyo anakalipereka kwa mayi wina amene kale anayamba kuphunzira Baibulo koma sanapitirize.

Mphunzitsiyo anasimba kuti: “Asanamalize kuwerenga mutu woyamba, anandiimbira foni ndi kundiuza kuti akusangalala nalo kwambiri bukulo.” Mayiyo anati anamva ngati bukulo linalembedwera iyeyo ndipo anapempha kuti ayambenso kuphunzira Baibulo. Mphunzitsiyo anati ataphunzira mitu 10 yoyambirira, mayiyo anali wosangalala ndipo mphunzitsiyonso anali wosangalala ndi zimenezi.

Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani silinathe zaka ziwiri chitulukireni. Ngakhale zili choncho, mabuku oposa 50 miliyoni asindikizidwa kale m’zinenero zoposa 150. Ngati mukufuna kuitanitsa bukuli, lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku lomwe lasonyezedwa panoli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo panyumba kwaulere.