Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
FOTOKOZANI FANIZO
1. M’fanizo la Yesu lolembedwa pa Mateyo 18:23-35, kodi kapolo ankafuna kuti mfumu imuchitire chiyani?
․․․․․
2. Kodi kapolo woyambirirayo anachita chiyani kwa kapolo m’nzake?
․․․․․
3. N’chifukwa chiyani mfumu inakwiya ndi kapolo woyamba uja?
․․․․․
▪ Kambiranani: Kodi mwakhululukirapo liti munthu wina? Kodi munthu ameneyo anakulakwirani chiyani? N’chifukwa chiyani munam’khululukira?
ZINACHITIKA LITI?
Tchulani munthu kapena anthu amene analemba mabuku a m’Baibulo amene ali m’munsiwa, ndipo lembani mzere kuchokera padzina la bukulo kufika pachaka chimene bukulo linamalizidwa kulembedwa.
1657 B.C.E.
1513 B.C.E. Cha m’ma 1100 B.C.E. Cha m’ma 56 C.E. Cha m’ma 61 C.E.
4. Genesis
5. Oweruza
6. Machitidwe
NDINE NDANI?
7. Ana anga amapasa anakhala makolo a mitundu iwiri ikuluikulu.
NDINE NDANI?
8. Mayere sanandigwere kuti ndikhale mtumwi.
KUCHOKERA M’MAGAZINI INO
Yankhani mafunsowa, ndipo lembani mavesi kapena vesi la m’Baibulo lomwe likusowapo.
Tsamba 3 Kodi ndi mavuto ati okhudza thanzi amene adzathetsedwe posachedwapa? (Yesaya 35:․․․)
Tsamba 11 N’chiyani chingakupangitseni kukhulupirira kuti matenda adzatha? (Luka 18:․․․)
Tsamba 20 Kodi chingalawa cha Nowa chinali chotalika bwanji m’mbali zake zosiyanasiyana? (Genesis 6:․․․)
Tsamba 30 Kodi muyenera kupewa khalidwe lotani ndipo ndi maganizo otani amene muyenera kukhala nawo musanaganize zolowa m’banja? (Aefeso 4:․․․)
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pachithunzi chilichonse.
(Mayankho ali patsamba 26)
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
1. Am’chitire chifundo pangongole yake.
2. Anam’ponya m’ndende.
3. Chifukwa kapoloyu sanasonyeze chifundo.
4. Mose, mu 1513 B.C.E.
5. Samueli, cha m’ma 1100 B.C.E.
6. Luka, cha m’ma 61 C.E.
7. Rabeka.—Genesis 25:21-23.
8. Barasaba.—Machitidwe 1:23-26.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Middle circle: Scott Bauer/Agricultural Research Service, USDA