Kodi N’zotheka Kuti Banja Likhale Losangalala?
Kodi N’zotheka Kuti Banja Likhale Losangalala?
Chaka chatha mayi wina wachitsikana analembera kalata ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico ndipo anapempha kuti amuthandize mmene angakhalire ndi banja losangalala. Iye anafotokoza kuti anasangalala kuwerenga magazini ya Galamukani! ndipo anati:
“Ndakhala ndili pabanja kwa zaka zitatu tsopano, ndipo ndikupempha uphungu ndi malangizo a mmene ndingakhalire ndi banja labwino. Zaka ziwiri zapitazo, ine ndi mwamuna wanga tinakhala ndi mwana wamwamuna ndipo ndikufunanso n’tamulera bwino kwambiri.”
Mayiyu anamvapo za buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja ndipo analemba kalata yakeyi kupempha buku limeneli. Anthu ena ambirimbiri achitanso chimodzimodzi. Pambuyo powerenga bukuli anthu ambiri afotokoza mmene lawathandizira. Ina mwa mitu yothandiza ya m’bukuli ndi “Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake,” “Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga,” ndi “Sungani Mtendere m’Banja Mwanu.”
Mungaitanitse buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kutumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.