Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kudzivulaza?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kudzivulaza?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kudzivulaza?

“Ndinali kuvutika koopsa ndipo palibe chomwe ndikanachita. Kenaka ndinatulukira chinthu chomwe ndikanatha kuchita. Ndikanatha kumadzimvetsa dala ululu m’thupi.”Anatero Jennifer, wa zaka 20. *

“Ndikakwiya, ndinkadzicheka. Imeneyi inali njira yanga yolilira. Pambuyo pake ndinkasangalala.” —Anatero Jessica, wa zaka 17.

“Sindinadzivulaze pafupifupi milungu iwiri tsopano. Imeneyi ndi nthawi yaitali kwa ine kukhala osadzivulaza. Sindikuganiza kuti ndidzasiyiratu.”—Anatero Jamie, wa zaka 16.

JENNIFER, Jessica, ndi Jamie sakudziwana, koma amachita zinthu zambiri zofanana. Atatu onsewa ankazunzika m’maganizo. Ndipo atatu onsewa anasankha njira yofanana yolimbanirana ndi kutaya mtima kwawo. Jennifer, Jessica, ndi Jamie ankapezako mpumulo wa kanthawi kochepa podzivulaza. *

Ngakhale kuti zikumveka zachilendo kwambiri, kudzivulaza, komwe kungaphatikizepo kudzicheka kapena kudzipundula, kwayamba kufala kwambiri pakati pa achinyamata. Nyuzipepala ya ku Canada yotchedwa National Post inati khalidwe limeneli “limaopsa makolo, limathetsa nzeru alangizi [a ku sukulu] ndipo limavutitsa madokotala.” Inanenanso kuti kudzivulaza “kungathe kusanduka chimodzi mwa zizolowezi zovuta kwambiri kuzisiya zomwe madokotala akudziwa.” Kodi inuyo kapena munthu wina amene mukumudziwa bwino ali n’chizolowezi chimenechi? Ngati ndi choncho, kodi mungachitepo chiyani?

Choyamba, yesani kuzindikira chimene chimakuchititsani kufuna kudzipweteka. Musaiwale kuti kudzivulaza ndi vuto lalikulu, osati chizolowezi choipa chabe. Nthawi zambiri kumakhala njira yolimbanirana ndi kupanikizika m’maganizo pa chifukwa chinachake. Munthu wodzivulaza amagwiritsira ntchito kupweteka kwa m’thupi kuti achepetseko kupweteka kwa m’maganizo. Choncho dzifunseni kuti: ‘Kodi kudzivulaza kumandithandiza bwanji? Kodi chilakolako chofuna kudzivulaza chimabwera ndikamaganizira za chiyani?’ Kodi pali zinazake zimene zikuchitika pa moyo wanu, mwina m’banja mwanu kapena ndi anzanu, zimene zikukuvutitsani maganizo?

Mwachidziwikire m’pofunika kulimba mtima kuti mudzifunse mafunso amenewa n’kupeza mayankho ake. Koma zotsatirapo zake zikhoza kukhala zabwino kwambiri. Nthawi zambiri imeneyi imakhala mbali yoyamba yomuthandiza munthu kusiya kudzivulaza. Komabe, pakufunika zambiri, osati kungozindikira chomwe chikuyambitsa vutoli basi.

Ubwino Wouzako Ena

Ngati mwayamba kudzivulaza, mungapindule mutauzako mnzanu wokhwima maganizo amene mumam’khulupirira zimene zikukuvutitsani maganizozo. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.” (Miyambo 12:25) Mukauza munthu wina, zingachititse kuti akuuzeni mawu otonthoza ndi okoma mtima amene mukufunikira kumva.—Miyambo 25:11.

Kodi mungalankhule ndi ndani? Zingakhale bwino mutasankha munthu wokulirapo kuposa inuyo amene amasonyeza kuti ndi wanzeru, wokhwima maganizo, ndiponso wachifundo. Akristu ali ndi mwayi chifukwa ali ndi akulu, amene ali “monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.”—Yesaya 32:2.

N’zoona kuti mukaganiza zouza chinsinsi chanu munthu wina mukhoza kuchita mantha. Mungamve ngati mmene anamvera Sara. Iye anati: “Poyamba, zinkandivuta kukhulupirira aliyense. Ndinkaganiza kuti anthu akandidziwa kuti ndine wotere, adzayamba kundithawa ndiponso kudana nane ndi kunyansidwa nane.” Koma ataululira munthu wina zakukhosi kwake, Sara anaona kuti zimene Baibulo limanena pa Miyambo 18:24 n’zoona. Lemba limeneli limati: “Lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.” Iye anati: “Akristu okhwima maganizo amene ndinalankhula nawo sanandikalipirepo, kaya ndiwauze zotani zokhudza khalidwe langa lodzivulaza. M’malo mwake, anandipatsa malangizo othandiza. Anakambirana nane pogwiritsa ntchito Malemba, ndipo ankandilimbikitsa moleza mtima ndikakhumudwa n’kumadziona ngati wopandiratu ntchito.”

Bwanji osalankhula ndi munthu wina za vuto lanu lodzivulaza? Ngati mukuona kuti simungalimbe mtima kulankhula naye pamaso m’pamaso, yesani kumulembera kalata kapena kumulankhula pa telefoni. Kulankhula ndi munthu wina ingakhale njira yabwino yokuthandizani kupeza bwino. Jennifer anati: “Chimene chinali chofunika kwambiri kwa ine chinali kudziwa kuti alipo anthu amene amandikondadi, kuti alipo amene ndingalankhule naye zinthu zikafika poipa kwambiri.” *

Kufunika kwa Pemphero

Donna anali atafika poti zinthu sizinalinso bwino. Iye ankatha kuona kuti akufunika thandizo la Mulungu. Komabe, iye ankaganiza kuti Mulungu sangamuthandize mpaka atasiya kudzicheka. Kodi n’chiyani chinathandiza Donna? Chinthu chimodzi chomwe chinamuthandiza chinali kusinkhasinkha za lemba la 1 Mbiri 29:17, lomwe limati Yehova Mulungu ‘amayesa mitima.’ Donna anati: “Yehova ankadziwa kuti pansi pa mtima ndinkafunitsitsadi kusiya kudzivulaza. Nditayamba kupemphera kwa iye kuti andithandize, zinali zodabwitsa kwambiri. Pang’ono ndi pang’ono, ndinayamba kulimba mtima n’kumatha kudziletsa kudzivulaza.”

Wamasalmo Davide, amene anakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wake, analemba kuti: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza.” (Salmo 55:22) Zoonadi, Yehova akudziwa za kuvutika kwanu. Kuwonjezera apo, “Iye asamalira inu.” (1 Petro 5:7) Ngati mtima wanu ukukuimbani mlandu, kumbukirani kuti Mulungu ‘ali wamkulu woposa mtima wanu, nazindikira zonse.’ Indedi, iye amamvetsa chifukwa chomwe mumadzivulazira ndiponso chifukwa chake mukuvutika kusiya. (1 Yohane 3:19, 20) Ngati mulankhula naye m’pemphero n’kuyesetsa kuthana ndi chizolowezi chimenechi, iye adzakuthandizani.—Yesaya 41:10.

Koma bwanji ngati mwayambiranso kudzivulaza pambuyo poti munasiya? Kodi zimenezo zikutanthauza kuti basi mwalephera? Ayi! Lemba la Miyambo 24:16 limati: “Wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso.” Poganizira lemba la m’Baibulo limeneli, Donna anati: “Ndinagwa nthawi zoposa kasanu ndi kawiri, koma sindinataye mtima.” Donna anaona kuti pamafunika khama. Karen nayenso anaona chimodzimodzi. Iye anati: “Ndinaphunzira kuona kuti kuyambiranso kudzivulaza pambuyo posiya kuli ngati kungobwerera m’mbuyo pang’ono, osati kulephera, ndipo ndinaphunziranso kuti ndisamagwe mphwayi koma ndiziyesetsa mobwerezabwereza kuchita zinthu zoti ndisiyiretu kudzivulaza.”

Pakafunika Thandizo Lowonjezera

Yesu anadziwa kuti odwala amafunika dokotala. (Marko 2:17) Nthawi zambiri pamafunika kukaonana ndi dokotala wodziwa za vuto limeneli kuti mudziwe ngati pali nthenda inayake imene ikukuchititsani kudzivulaza komanso thandizo limene mungafunikire. * Jennifer anasankha kupeza thandizo loterolo, lomwe linali lowonjezera pa thandizo limene anali kupeza kwa oyang’anira achikristu achikondi. Iye anati: “Akulu si madokotala, koma andithandiza kwambiri. Ngakhale kuti chilakolako chofuna kudzivulaza chimabwerabe nthawi zina, ndatha kulimbana nacho bwinobwino ndi thandizo la Yehova, mpingo, ndiponso pogwiritsira ntchito njira zomwe ndaphunzira zolimbanirana ndi vutoli.” *

Dziwani kuti mukhoza kupeza njira zabwino zolimbanirana ndi mavuto m’malo modzivulaza. Pempherani ngati mmene anapempherera wamasalmo kuti: “Khazikitsani mapazi anga m’mawu anu; ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse.” (Salmo 119:133) N’zachidziwikire kuti mudzasangalala ndiponso muzidzadzipatsa ulemu mukadzagonjetsa khalidwe limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena mu nkhani ino tawasintha.

^ ndime 6 Kuti mumve zambiri pa nkhani ya kudzivulaza, monga mitundu yake ndi zoyambitsa zake, onani nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa—N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?” mu Galamukani! ya January 2006.

^ ndime 14 Mungayeserere kunena zakukhosi kwanu pozilemba m’buku nthawi zina. Olemba Baibulo amene analemba masalmo anali anthu amene nthawi zina ankavutika maganizo kwambiri ndipo ankafotokoza kudandaula kwawo, mkwiyo wawo, kukhumudwa kwawo, ndi chisoni chawo polemba m’buku. Mwachitsanzo, mwina mungawerenge Masalmo 6, 13, 42, 55, ndi 69.

^ ndime 20 Nthawi zina munthu amadzivulaza chifukwa cha matenda enaake, monga kuvutika maganizo, matenda ochititsa munthu kusinthasintha zochitika, matenda olephera kudziletsa kuchita zinthu zinazake, kapena matenda ovutika kudya. Galamukani! silangiza anthu kuti atsatire njira yakutiyakuti ya chithandizo. Akristu ayenera kuonetsetsa kuti chithandizo chilichonse chimene akulandira sichikutsutsana ndi mfundo za m’Baibulo.

^ ndime 20 Magazini a m’mbuyomu a Galamukani! afotokozapo nkhani zokhudza zinthu zimene nthawi zambiri zimayambitsa kudzivulaza. Mwachitsanzo, onani nkhani zakuti “Kumvetsetsa Matenda a Maganizo” (January 8, 2004), “Kuthandiza Achinyamata Amene Akuvutika Maganizo” (September 8, 2001), ndi nkhani zonena za matenda ovutika kudya za mu Galamukani! ya February 8, 1999, komanso nkhani ya “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” yakuti “Kholo Chidakwa—Kodi Ndingalake Motani?” (August 8, 1992).

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi mungachite chiyani mukamavutika maganizo m’malo modzivulaza?

▪ Kodi mungalankhule ndi ndani ngati muli ndi vuto lodzivulaza?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 20]

KUTHANDIZA MUNTHU AMENE AMADZIVULAZA

Kodi mungathandize bwanji wachibale kapena mnzanu amene ali ndi vuto lodzivulaza? Popeza n’kutheka kuti munthu amene amadzivulazayo angakhale akufuna kwambiri munthu woti amuululire zakukhosi, mukhoza kumumvetsera mwatcheru akamalankhula. Yesetsani kukhala ‘bwenzi lobadwira kuti muthandize pooneka tsoka.’ (Miyambo 17:17) Mwina mukamva zimenezi mungakwiye n’kumuuza kuti asiyiretu nthawi yomweyo kudzivulazako. Koma kuchita zimenezi kungangochititsa wovutikayo kudana nanu. Komanso, pamafunika zambiri, osati kungomuuza munthuyo kuti asiye. Pamafunika nzeru kuti muthandize munthu amene amadzivulazayo kuphunzira njira zatsopano zolimbanirana ndi mavuto. (Miyambo 16:23) Pamafunikanso nthawi. Choncho lezani mtima. Khalani “wotchera khutu, wodekha polankhula.”—Yakobo 1:19.

Ngati ndinu wachinyamata, musaganize kuti mungathandize nokha munthu amene amadzivulaza. Musaiwale kuti mwina akhoza kukhala kuti ali ndi vuto kapena nthenda inayake imene ikufunika mankhwala. Komanso, kudzivulaza kukhoza kuika moyo pangozi, ngakhale ngati munthuyo sakufuna kudzipha. Choncho n’chinthu chanzeru kulimbikitsa munthu amene amadzivulazayo kuti alankhule ndi wachikulire wokhwima maganizo ndiponso wachikondi.

[Zithunzi patsamba 19]

Musamachepetse phindu lolankhula ndi munthu amene amakukondani komanso kufunika kopemphera