Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
FOTOKOZANI CHITHUNZICHI
1. Lembani zida zauzimu zimene Paulo anatchula pa Aefeso 6:11-17.
Lembani mzere kulumikiza yankho lanu lililonse ku chithunzichi.
․․․․․
․․․․․
․․․․․
․․․․․
․․․․․
․․․․․
2. Kodi msilikaliyu akusoweka chida chiti?
․․․․․
3. Kodi mivi yamotoyi ikuimira chiyani?
․․․․․
▪ Zoti Mukambirane: N’chifukwa chiyani tiyenera kuvala zida zonse zauzimu?
ZINACHITIKA LITI?
Lembani mzere kuchokera pa chithunzichi kufika pa deti lolondola limene ufumu umenewo unayamba.
1077 B.C.E. 607 B.C.E. 539 B.C.E. 455 B.C.E. 331 B.C.E.
4. Zachokera pa Danieli 7:4-6
5. Zachokera pa Danieli 7:4-6
6. Zachokera pa Danieli 7:4-6
NDINE NDANI?
7. Ndinavomera kuti ndinaba ndalama mazana khumi ndi limodzi kwa amayi anga; kenako ndinawabwezera.
NDINE NDANI?
8. Ndinasankha kukwatira mitala, ndipo mkazi wanga wina dzina lake anali Yuditi.
KUCHOKERA M’MAGAZINI INO
Yankhani mafunso awa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowekapo.
Tsamba 3 Kodi ukalamba wa Abrahamu unafotokozedwa bwanji? (Genesis 25:․․․)
Tsamba 8 Kodi okalamba chidzawachitikire n’chiyani mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu? (Yobu 33:․․․)
Tsamba 13 Mosiyana ndi zimene Oyeretsa ankaphunzitsa, kodi Baibulo limati munthu akafa chimamuchitikira n’chiyani? (Mlaliki 9:․․․)
Tsamba 19 Kodi pemphero lingathandize bwanji achinyamata amene akuvutika? (Salmo 55:․․․)
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? M’mawu anuanu, fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
(Mayankho pa tsamba 22)
MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31
1. M’chuuno momangidwa ndi choonadi, chapachifuwa cha chilungamo, mapazi ovala Uthenga Wabwino wa mtendere, chikopa cha chikhulupiriro, chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu.
2. Nsapato.
3. Zimene Satana akuchita pofuna kugonjetsa chikhulupiriro chathu.—1 Petro 5:8, 9.
4. Mediya ndi Perisiya, kuyambira mu 539 B.C.E.
5. Girisi, kuyambira mu 331 B.C.E.
6. Babulo, kuyambira mu 607 B.C.E.
7. Mika.—Oweruza 17:1-3.
8. Esau.—Genesis 26:34, 35.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Top circle: North Wind Picture Archives; second circle from top: Photo courtesy of Ossur/Photographer: David Biene