Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Ndinkafuna Kuchidziwa Bwino Chipembedzo Changa’

‘Ndinkafuna Kuchidziwa Bwino Chipembedzo Changa’

‘Ndinkafuna Kuchidziwa Bwino Chipembedzo Changa’

MTSIKANA wina wa zaka 12 wa ku Florida, ku United States, dzina lake Ciara atapatsidwa ntchito kusukulu pa phunziro la mbiri yakale, anasankha nkhani yochititsa chidwi kwambiri. Iye anafotokoza nkhani ya kuzunzika kwa Mboni za Yehova ku Germany pamene chipani cha Nazi chinali kulamulira. Iye anati: “Ndinasankha nkhani imeneyi chifukwa ndinkafuna kudziwa bwino mbiri ya chipembedzo changa. Ndinkafuna kumvetsa bwino momwe Mboni za Yehova zinavutikira panthawi imene chipani cha Nazi chinapha anthu ambiri pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse.”

Atafufuza kwambiri nkhaniyi, Ciara anakonzetsa bokosi lofiirira lamatabwa losongoka pamwamba, lomwe mbali yake iliyonse inali ndi makona atatu. Bokosili limaimira kansalu kofiirira ka makona atatu kamene ankakasoka pa mayunifolomu a Mboni za Yehova m’ndende zozunzirako anthu, kuti azidziwika. Pa bokosipo Ciara anaikapo zithunzi ndi mawu ofotokozera zithunzizo. Anaikaponso kalata yomvetsa chisoni kwambiri koma yolimbitsa chikhulupiriro yomwe analemba ndi Wolfgang Kusserow, wa Mboni za Yehova, atangotsala pang’ono kuphedwa.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1986, tsamba 10.

Zomwe Ciara anaonetsazo zinasonyeza bwino kuti Mboni zinali ndi mwayi winawake womwe akaidi ena analibe. Wamboni aliyense akanatha kumutulutsa m’ndende akanasaina chikalata chinachake chonena kuti wasiya chipembedzo chake. Popeza ambiri a iwo sanasaine chikalatacho, ndi umboni wakuti Mboni za Yehova n’zokhulupirikadi.

Ciara anati anapindula chifukwa chosankha nkhani imeneyi. Inamuthandiza kuchidziwa bwino chipembedzo chake. Iye anati: “Ngakhale kuti Mboni za Yehova zinalipo zochepa chabe ku Germany panthawi imeneyo, zinali ndi chikhulupiriro cholimba, chomwe chinawathandiza kupirira chizunzo chomwe anakumana nacho.”

Ngati ndinu mwana wasukulu wa Mboni za Yehova, kodi pali njira zomwe nanunso mungalankhulire za mbiri ya chipembedzo chanu?