Kodi Kuba M’masitolo Ndi Nkhani Yaikulu Bwanji?
Kodi Kuba M’masitolo Ndi Nkhani Yaikulu Bwanji?
TAYEREKEZERANI kuti mukuona zochitika zotsatirazi. Khomo lakumaso la sitolo yaikulu likutseguka, ndipo mukulowa atsikana awiri atatchena bwino. Akuyenda m’sitolomo kufika pamene pali zodzoladzola. Mlonda wovala yunifolomu akuwatsatira koma akuima atatalikirana nawo mamita 10, ndipo akuika manja ake kumbuyo. Mlondayo akuwayang’ana atsikanawo pamene iwo akugwiragwira mafuta ofiiritsa m’milomo ndi odetsa nsidze.
Nawonso akumuyang’ana mlondayo, ndipo mlondayo akupitirizabe kuwayang’ana. Mitima yawo ikugunda. Mtsikana mmodzi akupita pamene pali mafuta opaka m’makadabo ndipo akunyamula mabotolo angapo. Akuipitsa kunkhope kwake pamene akunamizira kusankha mtundu umodzi pakati pa mitundu iwiri yofiirira. Akuika botolo limodzi pansi n’kusankha lina la mtundu wofiira modera.
Mlondayo akuyang’ana pansi n’kutembenuka kuyang’ana mbali ina ya sitoloyo. Ngati kuti apangana, nthawi yomweyo atsikanawo akuika mabotolo a mafuta ofiiritsa m’milomo ndi opaka m’makadabo m’zikwama zawo. Nkhope zawo zikuoneka zodekha, koma panopa mitima yawo ikugunda kwambiri. Akukhalabe m’sitolomo kwa mphindi zina zingapo, wina akuyang’ana timatabwa tosalalitsira makadabo pamene winayo akuyang’ana mapensulo odetsera nsidze.
Kenaka atsikanawo akuyang’anana n’kugwedezerana mitu, ndipo akuyamba kuyenda molowera ku khomo lotulukira m’sitoloyo. Mlondayo akuwapatsa mpata, ndipo akumumwetulira pamene akumudutsa. Akuyandikira pamene ayalapo zinthu zokhudzana ndi mafoni a m’manja moyang’anizana ndi polipirira, ndipo akuziyang’ana zinthuzo. Akunong’onezana za timatumba tachikopa toikamo mafoni a m’manja tomwe tili pamenepo. Kenaka akuyamba kuyenda kutuluka panja.
Pamene akuyenda choncho, mitima yawo ikugunda kwambiri ngati iphulika, ndipo zonsezi n’chifukwa cha mantha osaneneka komanso chisangalalo chadzaoneni. Pamene atsikanawo akudutsa pakhomo lotulukira panja, akufuna kukuwa chifukwa chosangalala, koma akudzigwira. Pofika panja, nkhope zawo zikuoneka zofiira kwambiri chifukwa cha kusangalala, ndipo zafiira kuposa momwe zodzoladzola zilizonse zikanafiiritsira nkhope zawo. Mitima yawo pang’ono ndi pang’ono ikukhala m’malo, ndipo akupuma mousa moyo chifukwa choti apulumuka. Atsikanawo akuyamba kuyenda ndawala, koma akungoseka. Chinthu chimene akuganizira m’mutu mwawo n’chimodzi chokha basi, choti aba osagwidwa.
Nkhani ya atsikanawa ndi yongopeka koma zomwe tafotokozazi zimachitikadi. Ku United States kokha, tsiku lililonse anthu osiyanasiyana amaba nthawi zokwana pafupifupi wani miliyoni, ndipo vuto limeneli n’lapadziko lonse. Monga momwe tionere, khalidwe limeneli limapweteketsa anthu kwambiri. Koma anthu ambiri oba m’masitolo saganizirako n’komwe za mavuto amene amabweretsa. Ngakhale anthu ambiri amene angathe kulipira, salipira koma m’malo mwake amaba. N’chifukwa chiyani amatero?