“Kodi Ndipeze Chibwenzi pa Intaneti?”
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
“Kodi Ndipeze Chibwenzi pa Intaneti?”
“Tinkatumizirana makalata pa kompyuta tsiku lililonse. Tinagwirizana komwe tizidzakhala ndi ntchito yomwe tizidzagwira. Ineyo ndimafunika kupeza mphete zochitira chinkhoswe. Tinali titadziwana nthawi yosakwana ndi mwezi umodzi womwe, ndipo tinali tisanakumanepo pamaso m’pamaso.”—Anatero Monika, wa ku Austria. *
MWINA mukufunitsitsa mutakumana ndi munthu amene mungakhale naye pachibwenzi, woti mwina mungamange naye banja. Koma mpaka pano, kuyesayesa kwanu kuti mupeze munthu woteroyo sikunaphule kanthu. Anzanu ndi achibale anu pofuna kukuthandizani ayesera kukupezerani munthu woti muyambe naye chibwenzi koma zimenezi sizinathandize. M’malo mwake, zangokuchititsani manyazi ndipo zakuchititsani kukhala wokhumudwa kwambiri kuposa kale. Choncho mukuganiza kuti mwina muyesere kugwiritsa ntchito luso lamakono lolankhulirana.
Masiku ano, pamene anthu ambiri akugwiritsa ntchito makompyuta, kupeza munthu woti mungakwatirane naye kungaoneke ngati n’kosavuta. Mungaganize kuti mumangofunika kudinikiza batani pa kompyuta basi. Ena amati zomwe mumafunika kuchita ndi kungotsegula malo ena ake pa Intaneti amene anawakonzera makamaka anthu osakwatira. Nyuzipepala inayake (The New York Times) inati m’mwezi umodzi ku United States kokha, anthu 45 miliyoni anatsegulako malo a pa Intaneti othandiza anthu kupeza zibwenzi. Kampani inayake yothandiza anthu kupeza zibwenzi pa Intaneti inati ikuthandiza makasitomala nayini miliyoni m’mayiko 240.
Chifukwa Chake Anthu Ambiri Amafuna Kupeza Chibwenzi pa Intaneti
Kodi ndinu munthu wamanyazi, ndipo kodi mumamangika mukaganiza zokumana ndi anthu achilendo? Kodi mumaopa kukanidwa? Kapena kodi mukuona kuti ku dera kumene mukukhala kulibe anthu ambiri omwe mungathe kumanga nawo banja? Ngati ndi choncho, mungafune kupeza chibwenzi pa Intaneti. Chifukwa chimodzi chomwe chingakuchititseni zimenezi n’choti makampani othandiza anthu kupeza zibwenzi pa Intaneti angakuuzeni kuti mudzakhala ndi ufulu wosankha munthu amene mungakonde kuyamba
naye chibwenzi. Mukatsegula malo amenewa pa Intaneti, mumapezapo mabokosi ofotokoza zaka za anthuwo, dziko limene amakhala, makhalidwe awo, zithunzi zawo, ndi mayina awo ongopeka ogwiritsa ntchito pa Intanetipo. Popeza mungathe kusankha nokha munthu amene mukufuna, zingaoneke kuti kukhala ndi chibwenzi pa Intaneti n’kophweka ndiponso sikudetsa nkhawa kwenikweni kusiyana n’kukumana ndi munthu pamaso m’pamaso.Koma kodi zoona zake n’zotani? Kodi kuchita chibwenzi pa Intaneti kumabweretsadi chimwemwe chokhalitsa? Taganizirani izi: Pa zaka sikisi, kampani inayake yothandiza anthu kupeza zibwenzi pa Intaneti inali ndi makasitomala 11 miliyoni. Koma maukwati amene anachitika pakati pa anthu amenewa analipo 1,475 okha. Kampani ina yokhala ndi makasitomala opitirira wani miliyoni inati maukwati amene anachitika pakati pawo analipo 75 okha. Kodi cholakwika n’chiyani ndi njira imeneyi yopezera munthu wokwatirana naye?
Kodi Mungadziwanedi?
Nkhani ya mu nyuzipepala inayake inati: “Pa Intaneti, aliyense amakhala wokongola, wokhulupirika, ndiponso woti zinthu zikumuyendera bwino pamoyo wake.” Koma kodi zinthu zimene anthu amanena zokhudza iwowo zimakhala zoonadi? Nkhani ina ya m’nyuzipepala inafotokoza zimenezi motere: “Aliyense amadziwa kuti anthu amanamako pang’ono.” Mkonzi wamkazi wa magazini inayake yotchuka ya achinyamata anachita yekha kafukufuku kuti aone ngati anthu amanamadi. Anaika dzina lake pa malo atatu otchuka kwambiri opezerapo zibwenzi pa Intaneti, ndipo pasanapite nthawi yaitali analandira makalata angapo. Kenaka anayamba zibwenzi ndi amuna angapo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Zibwenzizo sizinapite patali n’komwe. Amunawo ananama kwambiri podzifotokoza. Iye anachenjeza kuti: “Malinga ndi zomwe ineyo ndakumana nazo, anthuwa amanama.”
Kunama pofotokoza kutalika kapena kulemera kwa munthu kungaoneke ngati nkhani yaing’ono. Ena anganene kuti, ‘Maonekedwe si ofunika kwenikweni.’ N’zoona kuti ngakhale Baibulo limati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe.” (Miyambo 31:30) Koma kodi kumanamizana pa zinthu zooneka ngati zazing’ono ndi njira yabwino yoyambira chibwenzi? (Luka 16:10) Kodi mungakhulupirire bwanji zinthu zina zimene munthuyo anganene pa nkhani zikuluzikulu, monga zolinga zake za m’tsogolo? Baibulo limati: “Nenani choonadi yense ndi mnzake.” (Zekariya 8:16) Indedi, kunena zoona kumayala maziko olimba a chibwenzi chimene chingayende bwino.
Koma anthu akamachita chibwenzi pa Intaneti nthawi zambiri amaganizira zinthu zoti sizingachitike. Nkhani imene inalembedwa m’magazini inayake (Newsweek) inati: “Anthu amene akufuna kupeza chibwenzi pa Intaneti akhoza kulemba makalata awo mosamala kwambiri kuti aoneke ngati anthu abwino kwambiri. . . . Zotsatirapo zake n’zoti popeza wolemba kalatayo akuoneka ngati munthu wabwino, wolandira kalatayo poyankha amadzifotokoza ngati iyeyonso ndi munthu wabwino, basi n’kumangotero.” Monga momwe anaonera pulofesa winawake wa pa sukulu inayake ku New York (Rensselaer Polytechnic Institute) amene amafufuza za anthu ochita zibwenzi pa Intaneti, anthu akhoza kuyamba kukondana kwambiri panthawi yochepa akamachita chibwenzi pa Intaneti. Komabe, monga mmene zimachitikira nthawi zambiri, zimenezi sizitanthauza kuti anthuwo adzakwatirana n’kukhala achimwemwe. Pofotokoza zomwe waona atachitapo zibwenzi pa Intaneti, mwamuna wina anati: “Zimakhala zachinyengo. Maganizo ako amawonjezera zinthu zomwe sukudziwa zokhudza munthu winayo ndi zomwe iweyo ukufuna.”
Kukumana Pamaso M’pamaso
Koma ena angaganize kuti popeza simuonana pamaso m’pamaso, zimenezi zili ndi ubwino wake. Angaganize kuti kuchita chibwenzi pa Intaneti kumathandiza anthuwo kuganizira kwambiri mtima wa munthu amene akufuna kukwatirana nayeyo popanda kutengeka ndi maonekedwe ake. N’zoona kuti Baibulo limatilimbikitsa kuganizira kwambiri mtima wa munthu. (1 Petro 3:4) Koma vuto lomwe lilipo n’loti pochita chibwenzi pa Intaneti simungaone momwe munthuyo akuyendetsera manja ake, kumwetulira kwake, kapena momwe nkhope yake ikuonekera. Simungaone momwe amachitira zinthu akakhala ndi anthu ena kapena akakhala pampanipani. Koma zimenezi n’zofunika kwambiri kuzidziwa kuti muthe kudziwa ngati munthuyo mungathe kumukhulupirira ndi kumukonda. Tawerengani momwe Baibulo limafotokozera chikondi pa 1 Akorinto 13:4, 5. Onani kuti pamenepa afotokoza chikondi malinga ndi khalidwe, osati mawu. Choncho mufunika kumupenda bwinobwino munthuyo kuti muone ngati khalidwe lake likugwirizana ndi zomwe amanena.
Popeza anthu akamachita chibwenzi pa Intaneti sadziwa zinthu zimenezi, nthawi zambiri amayamba kuuzana zinthu zachinsinsi chibwenzi chitangoyamba kumene. Mosaganizira za mawa, anthu ena amalonjezana za ukwati msangamsanga, ngakhale kuti sakudziwana n’komwe. Nkhani ina yake yomwe inali ndi mutu wakuti “Pa Intaneti, Chikondi Chimakhaladi Chakhungu” inafotokoza za anthu awiri omwe ankakhala ku malo otalikirana makilomita pafupifupi 12,800 amene anadziwana pa Intaneti. Patatha milungu itatu anakumana pamaso m’pamaso. Mwamunayo anati: “Mtsikanayo anadzipenta kwambiri nsidze zake. Ine sindichita chibwenzi ndi anthu amene amadzipenta nsidze.” Chibwenzicho chinatha nthawi yomweyo. Zomwe zinachitika mwamuna ndi mkazi wina atakumana pamaso m’pamaso zinali zokhumudwitsa kwambiri moti mwamunayo, amene anamulipirira mkaziyo tikiti yake ya ndege, anakafufutitsa mbali ya tikiti yomwe mkaziyo amafunika kugwiritsa ntchito pobwerera kwawo.
Mtsikana wina dzina lake Edda anafotokoza zomwe zinamuchitikira atapeza chibwenzi pa Intaneti. Iye anati: “Chibwenzicho chinkayenda bwino kwambiri moti zinkaoneka zosakhulupirika. Tinkakonza zoti tikwatirane.” Koma atakumana pamaso m’pamaso, zinthu sizinayende bwino n’komwe. Edda anati: “Mnyamatayo anali wosiyana ndi mmene ndinkaganizira ndipo anali wokonda kutola anzake zifukwa ndiponso wongodandaula zilizonse. Zinachita kuonekeratu kuti chibwenzicho sichingayende bwino.” Patatha mlungu umodzi chibwenzicho chinatha, ndipo Edda anakhumudwa kwambiri.
Popeza zinthu sizikhala ngati zenizeni pochita chibwenzi pa Intaneti, anthu akhoza kuyamba kukondana kwambiri pa kanthawi kochepa. Zimenezi zingakuchititseni kusweka mtima kwambiri ngati chibwenzicho chitatha, zomwe zimachitika kawirikawiri. Lemba la Miyambo 28:26 limachenjeza kuti: “Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa.” Indedi, si chinthu chanzeru kuchita zinthu zikuluzikulu pongodalira zimene mukuganiza, kapena mmene mukumvera mumtima mwanu. Choncho mwambiwo umapitiriza kuti: “Koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.”
Kuipa Kopupuluma
Kupupuluma kuyamba chibwenzi pamene simukudziwana bwino n’kupandadi nzeru. Mlembi wachingelezi dzina lake Shakespeare akuti analembapo kuti: “Ukwati wochitika mopupuluma nthawi zambiri suyenda bwino.” Malangizo a m’Baibulo amanena mfundo imeneyi mwachindunji. Amati: “Yense wansontho angopeza umphawi.”—Miyambo 21:5.
N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amene amachita zibwenzi pa Intaneti apeza kuti mawu amenewo ndi oona. Atalemberana makalata ndi munthu wina kwa mwezi umodzi wokha, Monika, amene tamutchula koyambirira uja, ankaganiza kuti basi, wapeza munthu woti akwatirane naye. Ngakhale kuti anali atakonza zoti akwatirane, mpaka kukonza zoti agule mphete zochitira chinkhoswe, chibwenzi chake chamsangamsangacho chinatha “momvetsa chisoni kwambiri.”
Mukhoza kupewa kupwetekedwa mtima potsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miyambo 22:3) Komabe, kukhumudwa ndi kupwetekedwa mtima si mavuto okhawo amene mungakumane nawo mukamachita chibwenzi pa Intaneti. Nkhani ya m’tsogolo idzafotokoza mavuto enanso omwe amakhalapo.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Mayina ena asinthidwa.
[Chithunzi patsamba 25]
Pa Intaneti, anthu nthawi zambiri amakokomeza kapena kunama akamafotokoza momwe alili
[Chithunzi patsamba 26]
Pambuyo polemberana makalata ambiri achikondi pa Intaneti, kukumana pamaso m’pamaso nthawi zambiri kumakhala kokhumudwitsa