Imene Imatchedwa “Milungu”
Imene Imatchedwa “Milungu”
MTUMWI Paulo atachiritsa munthu wolumala ku Lustra, anthu anafuula kuti: “Milungu yatsikira kwa ife monga anthu.” Paulo anamutcha Herme ndipo mnzake Barnaba anamutcha Zeu. (Machitidwe 14:8-14) Ku Efeso, munthu wina wosula siliva dzina lake Demetriyo anachenjeza anthu kuti Paulo akaloledwa kupitiriza kulalikira, “kachisi wa mlungu wamkazi Artemi adzayamba kuyesedwa wachabe.”—Machitidwe 19:24-28.
Monga anthu ambiri masiku ano, anthu a m’zaka 100 zoyambirira Yesu atabwera ankalambira “yoti yonenedwa milungu, kapena m’mwamba, kapena pa dziko lapansi.” Ndipo Paulo anati: “Iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri.” Komabe, iye anafotokozanso kuti: “Kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate” ndi “Ambuye mmodzi Yesu Kristu.”—1 Akorinto 8:5, 6.
Kodi Yesu Ankatchedwanso Mulungu?
Ngakhale kuti Yesu sananenepo kuti anali Mulungu, monga wolamulira woikidwa ndi Yehova, iye amafotokozedwa mu ulosi wa Yesaya kuti ndi “Mulungu wamphamvu” ndi “Kalonga wa mtendere.” Ulosi wa Yesaya unapitiriza kuti: “Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.” (Yesaya 9:6, 7) Choncho monga “Kalonga,” mwana wa Mfumu Yaikulu, Yehova, Yesu adzakhala Wolamulira wa boma lakumwamba la “Mulungu Wamphamvuyonse.”—Eksodo 6:3.
Komabe, munthu angafunse kuti, ‘Kodi Yesu ndi “Mulungu wamphamvu” m’lingaliro lotani, ndipo kodi mtumwi Yohane si paja ananena kuti Yesu ndiye Mulungu?’ Pa Yohane 1:1, Baibulo limati: “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu.” Ena amati zimenezi zikutanthauza kuti “Mawu,” amene anabadwa padziko lapansi monga Yesu wakhanda, ndiye Mulungu Wamphamvuyonse. Kodi zimenezi n’zoona?
Ngati tinganene kuti vesi limeneli likutanthauza kuti Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse, lingatsutsane ndi mawu amene ali m’vesi lomwelo akuti: “Mawu anali kwa Mulungu,” kapena kuti anali ndi Mulungu. Munthu amene ali “ndi” munthu wina sangakhalenso munthu winayo. Choncho, mabaibulo ambiri amawasiyanitsa awiriwa ndipo amasonyeza momveka bwino kuti Mawu sanali Mulungu Wamphamvuyonse. Mwachitsanzo, Baibulo la New World Translation ndi Baibulo lachingelezi la The Emphatic Diaglott, lolembedwa ndi Benjamin Wilson limanena kuti ‘Mawuyo anali mulungu.’ Malinga ndi mabaibulo amenewa, Mawu si Mulungu. Koma chifukwa choti ali ndi udindo wapamwamba kwambiri pa zolengedwa zonse za Yehova, Mawu amatchedwa “mulungu” (“m” wa chilembo chaching’ono). Panopa mawu akuti “mulungu” akutanthauza “wamphamvu.” Baibulo lotchedwa An American Translation, lolembedwa ndi J.M.P. Smith ndi E. J. Goodspeed, limafotokoza zimenezi momveka bwino kwambiri, chifukwa limati, “Mawuyo anali waumulungu.”
Mavesi ena a m’Baibulo amene m’chinenero chachigiriki Yohane 1:1 ndiwo Machitidwe 12:22 ndi 28:6. Mavesi amenewa amasonyeza kuti kugwiritsa ntchito mawu akuti “mulungu” sikutanthauza kuti amene akunenedwayo ndi chimodzimodzi ndi Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova. Mwachitsanzo, pamene Herode Agripa Woyamba ankalankhulitsa khamu la anthu amene anabwera pa msonkhano wake, anthuwo anatengeka maganizo kwambiri moti anayamba kukuwa kuti: “Ndiwo mawu a Mulungu.” Ndipo pamene Paulo anapulumuka atalumidwa ndi njoka yaululu, anthu anati Pauloyo “ndiye Mulungu.” Choncho, kunena kuti Mawu si “Mulungu,” koma ndi “mulungu” n’kogwirizana ndi galamala yachigiriki ndiponso zimene Baibulo limaphunzitsa.—Yohane 1:1.
analembedwa mofanana ndi lemba laTaonani momwe Yohane anamufotokozera “Mawu” m’chaputala choyamba cha Uthenga wake wabwino. Iye analemba kuti, ‘Mawu anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero [osati wonga wa Mulungu koma] wonga wa wobadwa yekha wa Atate.’ Choncho, “Mawu,” amene anakhala ndi thupi lanyama, anakhala padziko lapansi monga munthu wotchedwa Yesu ndipo anthu anamuona. Choncho, sakanakhala Mulungu Wamphamvuyonse, amene ponena za iye Yohane anati: “Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse.”—Yohane 1:14, 18.
Koma wina angafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Tomasi ataona Yesu ataukitsidwa anakuwa kuti, “Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga”?’ Monga momwe taonera kale, Yesu ndi mulungu m’lingaliro lakuti iye ndi waumulungu, koma iye si Atate. Yesu anali atangouza kumene Mariya wa Magadala kuti: ‘Ndikwera kumka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.’ Chinanso, kumbukirani chifukwa chimene Yohane analembera Uthenga wake wabwino. Yohane atatha kufotokoza nkhani ya Tomasi, mavesi atatu patsogolo pake anafotokoza kuti analemba zimenezi kuti anthu akhulupirire kuti ‘Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu,’ osati kuti ndi Mulungu.—Yohane 20:17, 28, 31.
Kodi “Mulungu wa Nthawi Ino ya Pansi Pano” Ndi Ndani?
Mwachionekere, pali milungu yambiri. Ina mwa milungu imeneyi, monga momwe taonera, inatchulidwa m’Baibulo. Komabe, anthu amene anaona mphamvu za Yehova kalekale anafuula kuti: “Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.” (1 Mafumu 18:39) Koma pali mulungu winanso amene ali ndi mphamvu. Baibulo limati: “Mulungu wa nthawi ino ya pansi pano unachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira.”—2 Akorinto 4:4.
Usiku woti afa mawa lake, Yesu anachenjeza ophunzira ake katatu za mulungu ameneyu, ndipo anamutcha “mkulu [“wolamulira,” NW] wa dziko ili lapansi.” Yesu anati wolamulira, kapena kuti mulungu ameneyu, “adzatayidwa kunja.” (Yohane 12:31; 14:30; 16:11) Kodi Mulungu ameneyu ndi ndani, ndipo kodi dziko limene amalamulira ndi liti?
Iye si winanso kupatulapo mngelo wopanduka, Satana Mdyerekezi. Tikudziwa bwanji zimenezi? Baibulo limafotokoza kuti pamene Satana ankamuyesa Yesu, anamuonetsa “mayiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo; nati kwa iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.” (Mateyu 4:8, 9) Chimenechi sichikanakhala chiyeso n’komwe ngati Satana akanamuuza Yesu kuti adzamupatsa zinthu zomwe Satanayo analibe. Indedi, mtumwi Yohane anati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.
Kumbukirani kuti Yesu analonjeza kuti ‘wolamulira wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja.’ (Yohane 12:31) Ndipo dziko lino, kapena kuti dongosolo la zinthu lino, limodzi ndi wolamulira wake, zidzachotsedwa. Mtumwi Yohane ananeneratu zimenezi pamene anati: “Dziko lapansi lipita.” Komabe, Yohane anawonjezera kuti: “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi yonse.” (1 Yohane 2:17) Tsopano tiyeni tione zolinga zosangalatsa zimene Mulungu woona yekha ali nazo ndi zomwe tiyenera kuchita kuti tidzapindule nazo.
[Chithunzi pamasamba 20, 21]
Anthu a ku Lustra ankaona Paulo ndi Barnaba ngati milungu
[Chithunzi pamasamba 20, 21]
Yesu anauza Mariya wa Magadala kuti ‘Ndikupita kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu’