Mmene Mungakhalire Tate Wabwino
Mmene Mungakhalire Tate Wabwino
NKHANI ya m’magazini yotchedwa Economist yonena za kuloŵa pansi kwa moyo wa banja inayamba ndi mawu odzutsa chidwi akuti: “N’zosavuta kuti munthu akhale ndi ana, koma kuti akhale tate wabwino si nkhani yapafupi.”
Zinthu zambiri m’moyo n’zovuta kuchita, koma chinthu chimodzi chovuta kwambiri, ndiponso chofunika kwambiri, ndicho kukhala tate wabwino. Tate aliyense ayenera kufuna kukhala tate wabwino, chifukwa umoyo wabwino ndi chimwemwe cha banja lake zimadalira iyeyo.
Chifukwa Chake Si Nkhani Yapafupi
Mwachidule, chifukwa chachikulu chimene chimachititsa kuti kukhala tate wabwino kukhale kovuta ndi kupanda ungwiro kumene timabadwa nako, makolo ndi ana omwe. Baibulo limati: “Ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.” (Genesis 8:21) Choncho wolemba Baibulo wina anavomereza kuti: “Mayi wanga anandilandira m’zoipa.” (Salmo 51:5; Aroma 5:12) Chilakolako chofuna kuchita zinthu zoipa chifukwa cha uchimo wobadwa nawo ndi chimodzi chabe mwa zopinga zimene zimachititsa kuti kukhala tate wabwino kukhale kovuta.
Dzikoli, kapena kuti dongosolo la zinthu lino, ndi chopinga chinanso chachikulu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti, monga momwe Baibulo limafotokozera, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” amene amadziŵika kuti ndiye “wotchedwa mdyerekezi ndi Satana.” Baibulo limanenanso kuti Satana ndiye “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano.” M’pake kuti Yesu ananena kuti, mofanana ndi iyeyo, otsatira ake sayenera kukhala “a dziko lapansi.”—1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9; 2 Akorinto 4:4; Yohane 17:16.
Kuti munthu akhale tate wabwino m’pofunika kwambiri kuti azikumbukira nthaŵi zonse kuti tinabadwa opanda ungwiro, kuti kunja kuno kuli Satana Mdyerekezi, ndi kuti dzikoli likulamulidwa ndi iye. Zopinga zimenezi si zongolota ayi. N’zenizeni! Koma kodi munthu angaphunzire kuti za mmene angalimbanirane ndi zopinga zimenezi kuti akhale tate wabwino?
Chitsanzo cha Yehova ndi Yesu
Kuti athandizidwe kulimbana ndi zopinga zomwe tazitchula pamwambazo, tate angaŵerenge Baibulo. Mmenemo muli zitsanzo zabwino kwambiri. Yesu anatchula chitsanzo chabwino kwambiri kuposa zonse pamene anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: ‘Atate wathu wa Kumwamba.’ Powafotokoza Atate athu a kumwamba, Baibulo limanena mwachidule kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” Mateyu 6:9, 10; 1 Yohane 4:8; Aefeso 5:1, 2.
Kodi munthu amene ali tate ayenera kuchita chiyani potsanzira chitsanzo chachikondi chimenechi? Mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu, . . . ndipo yendani m’chikondi.”—Ngati ndinu tate, taganizirani zimene mungaphunzire pa chochitika chimodzi chokha chokhudza Mulungu ndi Mwana wake Yesu. Lemba la Mateyu 3:17 limatiuza kuti pa ubatizo wa m’madzi wa Yesu, mawu a Mulungu anamveka kuchokera kumwamba, oti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” Kodi tingaphunzire chiyani pa mawu ameneŵa?
Choyamba, taganizirani mmene mwana amamvera bambo ake akamauza munthu wina mosangalala kuti, ‘Uyu ndi mwana wanga wamwamuna’ kapena ‘Uyu ndi mwana wanga wamkazi.’ Ana amamva bwino kwambiri makolo awo akamawalabadira, makamaka akamawayamikira chifukwa cha zabwino zimene achita. Mosakayikira mwana amene amayamikiridwa adzayesetsa kuchita khama kwambiri kuti amuyamikirenso.
Chachiŵiri, Mulungu anafotokoza mmene ankamvera mumtima mwake akamaona Yesu, ndipo anamutcha “wokondedwa.” Pamene Yesu anamva mawu osonyeza chikondi amenewo ochokera kwa Atate ake, ayenera kuti anamva bwino kwambiri mumtima. Ana anu nawonso adzalimbikitsidwa ngati muwasonyeza kuti mumawakonda kwambiri mwa mawu anu, komanso mwa kucheza nawo mokwanira, kuwalabadira, ndi kuwaganizira.
Chachitatu, Mulungu anauza Mwana wake kuti: “Mwa Iwe ndikondwera bwino.” (Marko 1:11) Chimenechonso n’chinthu chofunika kwambiri kuti tate azichita, kutanthauza kuti, kuuza ana ake kuti amakondwera nawo. N’zoona kuti mwana amalephera pa zinthu zambiri. Tonsefe timalephera nthaŵi zina. Koma monga tate, kodi mumafunafuna mipata youza ana anu kuti mumakondwera ndi zinthu zabwino zimene amachita ndi kunena?
Yesu anaphunzira bwino kwambiri kwa Atate ake akumwamba. Ali padziko lapansi, anasonyeza mwa zimene ananena ndi kuchita mmene Atate ake amamvera mumtima mwawo akamaona ana Ake apadziko lapansi. (Yohane 14:9) Ngakhale pamene Yesu anali wotanganidwa ndiponso wotopa, anapatula nthaŵi yoti akhale pansi n’kulankhula ndi ana. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse.” (Marko 10:14) Kodi atatenu mungatsatire chitsanzo cha Yehova Mulungu ndi Mwana wake kwambiri kuposa mmene mukuchitira panopa?
Kupereka Chitsanzo Chabwino N’kofunika Kwambiri
Kupereka chitsanzo chabwino kwa ana anu n’kofunika kwambiri. Kuyesetsa kwanu kuti “muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye” kudzakhala kopanda phindu lililonse ngati inuyo simukumvera malangizo a Mulungu ndi kuwatsatira pa moyo wanu. (Aefeso 6:4) Komabe, ndi thandizo la Mulungu, mungagonjetse zopinga zilizonse zimene zingakulepheretseni kumvera lamulo lake loti muzisamalira ana anu.
Taganizirani chitsanzo cha Viktor Gutschmidt, wa Mboni za Yehova wa ku dziko limene kale linali Soviet Union. Mu October 1957, iye anaweruzidwa kuti akakhale kundende zaka khumi chifukwa cholankhula za chikhulupiriro chake. Anasiya m’mbuyo ana aang’ono aŵiri aakazi ndi mkazi wake, Polina. Ali m’ndende, ankaloledwa kulembera banja lake makalata koma samaloledwa kunena chilichonse chokhudza Mulungu kapena nkhani iliyonse yachipembedzo. Ngakhale ali pamavuto aakulu chonchi, Viktor anafunitsitsa kuti akhale tate wabwino, ndipo anadziŵa kuti kuphunzitsa ana ake za Mulungu kunali kofunika kwambiri. Choncho, kodi anachita chiyani?
Viktor akufotokoza kuti: “Ndinkapeza nkhani m’magazini a ku Soviet Union otchedwa Young Naturalist ndi Nature. Ndiyeno ndinkajambula zithunzi za zinyama ndi anthu pa mapositikhadi n’kulembapo nkhani kapena zochitika zina zokhudza chilengedwe.”
Polina akufotokoza kuti: “Tikangolandira mapositikhadi ameneŵa, nthaŵi yomweyo tinkawagwirizanitsa ndi nkhani za m’Baibulo. Mwachitsanzo, akamasonyeza kukongola kwa chilengedwe, nkhalango, kapena mitsinje, ndinkaŵerenga Yesaya chaputala 65,” chimene chimafotokoza za lonjezo la Mulungu loti adzasintha dzikoli kukhala paradaiso.
Mwana wamkazi wa Viktor, Yulia akufotokoza kuti: “Ndiyeno Amayi ankapemphera nafe, ndipo tinkalira. Makadi ameneŵa anatithandiza kwambiri pamene tinali kukula.” Polina akufotokoza kuti chifukwa cha zimenezi, “atsikanawo anakhala okonda Mulungu kwambiri kuyambira ali ana.” Kodi panopa zinthu zili bwanji m’banja limeneli?
Viktor akufotokoza kuti, “Panopa ana anga anakwatiwa ndi akulu achikristu, ndipo onse aŵiri ali ndi mabanja olimba mwauzimu ndiponso ali ndi ana amene akutumikira Yehova mokhulupirika.”
Kupereka chitsanzo chabwino kumafuna osati luso lokha, komanso khama lalikulu. Mitima ya ana mosakayikira idzakhudzidwa akaona bambo awo akuchita khama kwambiri. Mwana wamwamuna amene anakhala zaka zambiri akuchita utumiki wa nthaŵi zonse ananena mawu otsatiraŵa oyamikira bambo ake: “Nthaŵi zina Bambo ankakhala otopa kwambiri akamachokera ku ntchito moti ankangofuna atagona basi, koma tinkachitabe phunziro lathu la Baibulo, ndipo zimenezi zinatithandiza kuona kufunika kwa phunzirolo.”
Zoonadi, kupereka chitsanzo chabwino, mwa zimene timanena ndi kuchita, n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale tate wabwino. Muyenera kuchita zimenezo ngati mukufuna kuti zimene mwambi wa m’Baibulo wotsatirawu umanena zidzakuchitikireni, woti: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”—Miyambo 22:6.
Choncho kumbukirani kuti si zimene mumanena zokha zimene zili zofunika, koma makamaka zimene mumachita, chitsanzo chimene mumapereka. Katswiri wina wa ku Canada wa maphunziro a ana aang’ono analemba kuti: “Njira yabwino kwambiri yothandizira ana athu kukhala ndi khalidwe labwino [limene tikufuna] ndiyo kusonyeza khalidwe limenelo eni akefe.” Indedi, ngati mukufuna kuti ana anu aziyamikira zinthu zauzimu, m’pofunika kuti inuyo muzichita zimenezo.
Pezani Nthaŵi Yocheza Nawo!
Ana anu ayenera kuona chitsanzo chanu chabwino. Zimenezo zikutanthauza kuti muyenera kucheza nawo nthaŵi zambiri, osati kungocheza nawo mwa apa ndi apo. Mwanzeru, mverani malangizo a m’Baibulo oti muyenera ‘kuombola nthaŵi,’ kutanthauza kuti, kusiya zinthu zosafunika kwenikweni kuti mukhale ndi nthaŵi yocheza nawo. (Aefeso 5:15, 16, NW) Ndipo kodi n’chiyani chimene chili chofunika kwambiri kuposa ana anu? Kodi ndi kuonerera TV, kuchita maseŵera a mtundu winawake, kukhala ndi nyumba yokongola, kapena kugwira ntchito yanu?
Ngati atate sapeza nthaŵi yosamalira ana awo akadali aang’ono, atatewo adzavutika patsogolo. Atate amene ana awo ali ndi khalidwe lachiwerewere kapena ali ndi moyo wosafuna zinthu zauzimu nthaŵi zambiri amadandaula kwambiri akaganizira za kale. Amadandaula kuti analephera kucheza mokwanira ndi ana awo ali aang’ono panthaŵi imene ankafunikira kwambiri kukhala ndi bambo awo.
Kumbukirani kuti, pa nthaŵi imene ana anu ali aang’ono m’pamene mufunika kuganizira zotsatira za zinthu zimene mumasankha kuchita. Baibulo limati ana anu ndi “cholandira cha kwa Yehova,” chinthu chimene Mulungu wakuikizani kuti muchisamalire. (Salmo 127:3) Choncho musamaiwale kuti Mulungu adzafuna kudziŵa mmene mwawalerera!
Thandizo Lilipo
Tate wabwino amasangalala kulandira thandizo limene lingapindulitse ana ake. Mngelo atauza mkazi wa Manowa kuti adzakhala ndi mwana, Manowa anapemphera kwa Mulungu kuti: “Atidzerenso munthu wa Mulungu mudam’tumayo, natilangize icho tizichitira mwanayo akadzabadwa.” (Oweruza 13:8, 9) Mofanana ndi makolo masiku ano, kodi Manowa anafunika thandizo lotani? Tiyeni tione.
Brent Burgoyne, mphunzitsi wa pa yunivesite ya Cape Town, ku South Africa, anati: “Mphatso imodzi yabwino kwambiri imene munthu angapatse mwana ndiyo kum’phunzitsa mfundo zoti aziyendera pamoyo wake.” Tingaone kuti ana amafunika kuphunzitsidwa mfundo zoterozo pa lipoti limene linalembedwa mu nyuzipepala ya ku Japan yotchedwa Daily Yomiuri. Lipotilo linati: “Kafukufuku [winawake] wasonyeza kuti ana 71 pa ana 100 alionse ku Japan sanauzidwepo ndi atate awo kuti asamaname.” Kodi zimenezo si zomvetsa chisoni?
Kodi ndani angapereke mfundo zabwino zoyendera pamoyo? Ndi yemweyo amene anapatsa Manowa malangizo, Mulungu mwiniwake. Kuti athandize anthu, Mulungu anatumiza Mwana wake wokondedwa, Yesu, monga Mphunzitsi, dzina limene anthu ambiri ankamuitanira. Panopa, buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, limene lili ndi malangizo ochokera ku zimene Yesu anaphunzitsa, lilipo m’zinenero zambiri kuti muziligwiritsa ntchito mukamaphunzitsa ana anu.
Buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso sikuti limangofotokoza mfundo zochokera m’Mawu a Mulungu basi, lilinso ndi zithunzi zogwirizana ndi zimene zikufotokozedwazo zokwana 160 zimene pambali pake kapena pansi pake pali mafunso ochititsa munthu kuganiza. Mwachitsanzo, mutu 22, woti “Chifukwa Chake Tiyenera Kupewa Bodza,” uli ndi chithunzi chomwe chili patsamba 32 la magazini ino. Mawu amene ali patsamba limene pali chithunzi chimenechi amati: “Kapena mwinamwake mnyamata akuuza atate ake kuti: ‘Ayi, sindine ndinaponyera mpira m’nyumba.’ Koma bwanji ngati iye ndiye anaponyeramo mpirawo? Kodi ndi kulakwa kunena kuti sanaponyeremo?”
Palinso maphunziro abwino kwambiri amene akupezeka m’mitu yakuti “Kumvera Kudzakuteteza,” “Tifunika Kukana Ziyeso,” “Phunziro la Kukhala Wokoma Mtima,” “Usakhale Wakuba!,” “Kodi ndi Mapwando Onse Amene Amakondweretsa Mulungu?,” “Zimene Tingachite Kuti Tikondweretse Mulungu,” ndi “Chifukwa Chake Tifunikira Kugwira Ntchito,” kungotchulapo mitu yochepa chabe pa mitu 48 imene ili m’bukuli.
Mawu oyamba m’bukuli pamapeto pake amati: “Ana afunika makamaka kuwatsogolera kwa Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu, yemwe ndi Gwero la nzeru zonse. Izi n’zimene Mphunzitsi Waluso, Yesu, anali kuchita nthaŵi zonse. Tili otsimikiza kuti buku lino lidzakuthandizani inuyo ndi banja lanu kukonza moyo wanu kuti uzikondweretsa Yehova, ndipo motero mudzapeza madalitso osatha.” *
Choncho, kukhala tate wabwino kumaphatikizapo kupereka chitsanzo chabwino kwa ana anu, kucheza nawo nthaŵi zambiri, ndi kuwathandiza kutsatira mfundo za Mulungu pamoyo wawo, zomwe zimapezeka m’Baibulo.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 35 Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, ndi Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja ndi mabuku ena amene Mboni za Yehova zimafalitsa othandiza mabanja.
[Chithunzi patsamba 24]
Ngakhale anali m’ndende, Viktor Gutschmidt anakwanitsa kukhala tate wabwino
[Zithunzi pamasamba 24, 25]
Ali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chake, Viktor anajambula zithunzi zimenezi kuti aphunzitse ana ake
[Chithunzi patsamba 25]
Ana a Viktor mu 1965
[Chithunzi patsamba 26]
Atate ayenera kuphunzitsa ana awo mwakhama