Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata Amene Sachita Manyazi Kulankhula za Chikhulupiriro Chawo

Achinyamata Amene Sachita Manyazi Kulankhula za Chikhulupiriro Chawo

Achinyamata Amene Sachita Manyazi Kulankhula za Chikhulupiriro Chawo

PAKATI pa Mboni za Yehova pali achinyamata ambiri. Amakonda Mulungu ndipo amayesetsa kutsatira mfundo zake zimene zinalembedwa m’Baibulo. Achinyamata ameneŵa amanyadira chikhulupiriro chawo, ndipo amalankhula momasuka ndi anzawo kusukulu za chikhulupiriro chawocho. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

▪ Pamene Holly anali mu sitandade sikisi, kapena kuti m’giredi sikisi, iye ndi anzake a m’kalasi mwawo anapatsidwa ntchito yoti akalembe nkhani pa funso lakuti: “Kodi mungathetse bwanji vuto la uchigaŵenga popanda kuchita zachiwawa?” Holly anagwiritsa ntchito mwayi umenewu kulemba za chiyembekezo chake cha m’tsogolo chogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Iye anafotokoza kuti m’mbiri yonse ya anthu, munthu ‘wakhala akupweteka mnzake pom’lamulira.’ (Mlaliki 8:9) Ndiyeno anasonyeza chiyembekezo chokhacho chimene anthu ali nacho, Ufumu wa Mulungu. Iye analemba kuti: “Popeza Yesu ndi amene ali Mfumu yoikidwa ya Ufumu umenewo, mavuto onse, kuphatikizapo uchigaŵenga, adzatha.” Holly anafotokoza mmene Yesu adzachitire zinthu zimene palibe wolamulira wina amene angathe kuzichita. Iye analemba kuti: “Yesu ali padziko lapansi, anasonyeza kuti adzakhala wolamulira wotani. Iye anali wachikondi ndipo ankasamalira anthu. Anasonyeza mphamvu imene ali nayo mwa kuchiza matenda ndi kuukitsa akufa. Palibe boma la anthu limene limatha kuukitsa anthu akufa. Koma Ufumu wa Mulungu udzachita zimenezo.” Holly anamaliza nkhani yakeyo ponena kuti: “Mulungu ndi amene adzathetse vuto limeneli, osati anthu.”

Pamunsi pa nkhaniyo, aphunzitsi ake analemba kuti: “Walemba mfundo zogwira mtima kwambiri, Holly. Ndipo wazisanja bwino kwambiri.” Aphunzitsiwo anachitanso chidwi kwambiri ndi Malemba amene Holly anagwiritsa ntchito. Zimenezi zinamupatsa Holly mwayi wouza aphunzitsi akewo za Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, imene Mboni za Yehova zimakhala nayo mlungu uliwonse ndipo cholinga chake n’kuthandiza anthu kudziŵa kulankhula ndi kuphunzitsa. Aphunzitsi ake analandira mosangalala buku limene limagwiritsidwa ntchito mu Sukulu ya Utumiki imeneyi.

Jessica nayenso anatha kulankhulapo za chikhulupiriro chake polemba nkhani za kusukulu. Iye anati: “Ndatha kulemba nkhani zitatu zokhudza chikhulupiriro changa. Imodzi inali yonena zimene Mboni za Yehova zachita pa nkhani ya ufulu wopembedza wa anthu. Aphunzitsi anga anaika nkhaniyo mu laibulale kuti ofuna azitha kuiŵerenga. Posachedwapa ndinalemba za ubatizo wanga ndi mmene tsiku limenelo linalili lofunika kwambiri kwa ine. Ana asukulu amatha kuonetsana nkhani zawo asanazimalize, choncho ndinaonetsa anthu a m’kalasi mwanga nkhani yangayo kuti aiŵerenge. Ataiŵerenga, mtsikana wina anati: ‘Wailemba bwino kwambiri. N’zothandiza kudziŵa zimene munthu amafunika kuchita akakhala wa Mboni za Yehova. N’zosangalatsanso kuti unabatizidwa.’ Mtsikana wina ananena kuti: ‘Nkhani yako inali yochititsa chidwi kwambiri! Ndasangalala kwambiri kudziŵa kuti chikhulupiriro chako n’cholimba chonchi!’ Mnyamata wina anangolemba kuti: ‘Ndiwe munthu wanzeru zedi. Walemba bwino kwambiri.’”

▪ Pamene Melissa anali ndi zaka 11, anali ndi mwayi wapadera wolankhula za chikhulupiriro chake. “Tsiku lina anesi a kusukulu kwathu anabwera m’kalasi yathu ya sayansi kudzatiuza za mphamvu ya thupi lathu yotiteteza ku matenda. Kenaka anatchulapo nkhani ya kuikidwa magazi. Titatuluka m’kalasi ndinauza aphunzitsi anga a sayansi za vidiyo yathu inayake yonena za magazi. Ndinaibweretsa kusukulu tsiku lotsatira ndipo aphunzitsi anga anaitengera kwawo n’kukaionera ndi banja lawo. M’maŵa mwake anaibweretsa kusukulu ndipo anaionetsa m’makalasi aŵiri, kuphatikizapo kalasi langa. Ndiyeno ananena zinthu zabwino zokhudza Mboni za Yehova, ndipo anauza kalasilo kuti pakanapanda Mboni za Yehova, zikanakhala zovuta kupeza njira zina zochiritsira popanda magazi. Pamene ankandibwezera vidiyoyo anandifunsa kuti, ‘Ndingachite chiyani kuti ndipeze vidiyo imeneyi yoti ndikaike mu laibulale ya kusukulu kuno?’ Ndinawapatsa vidiyo ina imodzi. Anasangalala nayo kwambiri, ndipo inenso ndinasangalala!”

Holly, Jessica, ndi Melissa ndi ena mwa Mboni zachinyamata za Yehova zimene zimatsatira malangizo a m’Baibulo oti akumbukire Mlengi wawo. (Mlaliki 12:1) Kodi nanunso mukuchita zimenezo? Ngati mukutero, dziŵani kuti mukukondweretsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11; Ahebri 6:10.

Achinyamatanu mukamalankhula za chikhulupiriro chanu kwa anzanu a kusukulu ndi aphunzitsi anu, mumachitira umboni wabwino kwambiri za Yehova Mulungu ndi zolinga zake. Zimalimbitsanso chikhulupiriro chanu ndipo zimakuchititsani kukhala onyadira pokhala mmodzi wa atumiki a Mulungu. (Yeremiya 9:24) Kulalikira kusukulu kumakutetezaninso. Jessica anafotokoza zimenezi motere: “Ubwino umodzi wolankhula za chikhulupiriro changa ndi woti anzanga a kusukulu sandikakamiza kuchita zinthu zosemphana ndi zimene Baibulo limanena.”

[Zithunzi patsamba 12]

Holly

[Zithunzi pamasamba 12, 13]

Jessica

[Chithunzi patsamba 13]

Melissa