Kodi Mfundo za Makhalidwe Abwino Mungazipeze Kuti?
Kodi Mfundo za Makhalidwe Abwino Mungazipeze Kuti?
TIKUKHALA m’dziko limene anthu akusintha mmene amaonera mfundo za makhalidwe abwino. Zinthu zachinyengo zimene kale anthu ankadana nazo masiku ano amangozinyalanyaza. Mbava ndi anthu oba mwachinyengo nthaŵi zambiri amazitchukitsa ndi kuzitamanda m’manyuzipepala, pa wailesi, ndi pa TV. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri amachita zimene Baibulo limanena, zoti: “Pakuona mbala, uvomerezana nayo.”—Salmo 50:18.
Koma anthu oba mwachinyengo si oyenera kuwasirira. Mlembi wina anati: “Chimene [chimachititsa] anthu oba mwachinyengo kukhala osiyana ndi anthu ena onse ndi luso lachibadwa limene
nthaŵi zambiri amalitulukira ali ana lotha kupusitsa anthu amene akukhala nawo pafupi. Kuwonjezera pamenepo, akapusitsa anthu samva kuti achita chinthu chilichonse cholakwika. M’malo mwake, amasangalala kwambiri, zimene zimawalimbikitsa kupitiriza kupusitsa anthu akafuna kupeza chinthu chilichonse, ndipo alibe nazo ntchito kuti kaya anthu enawo akupwetekedwa bwanji.”N’zoona kuti anthu amamva chisoni akaona mzimayi wamasiye ataberedwa ndalama zake zonse zimene anakhala akusunga moyo wake wonse, koma anthu ambiri samva chisoni munthu akabera kampani yaikulu kapena kampani ya inshuwalansi. Ambiri amati makampani ameneŵa ndi olemera kale, choncho palibe vuto ngakhale atawabera. Koma kuba koteroko sikuti kumangopweteka makampaniwo, kumakhudzanso anthu amene amagula katundu wawo. Mwachitsanzo, ku United States mabanja ambiri amapereka ndalama zina za inshuwalansi zowonjezera zokwana madola 1,000 pa chaka kuti ziziloŵa m’malo mwa ndalama zimene kampani ya inshuwalansiyo imaluza chifukwa cha anthu oba mwachinyengo.
Ndiponso, anthu ambiri sazengereza kugula zinthu zotchipa zimene mayina ake amafanana ndi mayina a zinthu zachilungamodi, monga zovala, mawotchi, mafuta onunkhiritsira thupi, zodzoladzola, ndi zikwama za m’manja. Anthu ameneŵa mwina amadziŵa kuti katundu wachinyengoyu amachititsa kuti makampani aziwononga ndalama zokwana madola mabiliyoni ambiri chaka chilichonse, koma amaganiza kuti zimenezi siziwakhudza iwowo. Koma pamapeto pake, anthu ogula katundu amapereka ndalama zambiri akamagula katundu wachilungamoyo. Kuwonjezera apo, kugula katundu wachinyengo kumachititsa kuti anthu akuba azilemera.
Mlembi wina amene amagwira ntchito yothana ndi kuba mwachinyengo analemba kuti: “Ndikukhulupirira kuti chifukwa chachikulu chimene chikuchititsa kuti masiku ano anthu ambiri aziba mwachinyengo n’chakuti tikukhala m’dziko lopandiratu makhalidwe abwino. Makhalidwe aloŵa pansi kwambiri ndipo zimenezi zachititsa kuti anthu ambiri aziba mwachinyengo. . . . Tikukhala m’dziko limene anthu saphunzitsa makhalidwe abwino kunyumba. Tikukhala m’dziko limene anthu saphunzitsa makhalidwe abwino kusukulu, chifukwa aphunzitsi angathe kuimbidwa mlandu woti akuphwanya ufulu wa ana powasankhira zochita.”
Mosiyana ndi zimenezo, Mboni za Yehova zimaphunzitsa mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’Mawu a Mulungu ndipo zimayesetsa kutsatira mfundo zimenezi. Zimayendera mfundo za makhalidwe abwino monga izi:
● “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.”—Mateyu 22:39.
● “Usanyenge.”—Marko 10:19.
● “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosoŵa.”—Aefeso 4:28.
● ‘Tikufuna kukhala ndi makhalidwe abwino.’—Ahebri 13:18.
Ngakhale kuti anthu a Mboni sadzikweza kapena kudziona kuti iwowo ndiye olungama, amakhulupirira kuti ngati aliyense akanati azitsatira mfundo zimenezi, dziko lapansi likanakhala malo abwino kwambiri okhala kuposa mmene lililimu. Amakhulupiriranso lonjezo la Mulungu loti tsiku lina dzikoli lidzakhala labwino choncho.—2 Petro 3:13.
[Mawu Otsindika patsamba 11]
Aliyense akanati azitsatira mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’Mawu a Mulungu, dziko lapansi likanakhala malo abwino kwambiri okhala kuposa mmene lililimu
[Chithunzi patsamba 10]
Akristu oona amatsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo monga mfundo yakuti, “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini”