Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngati Mwana Wanu Wakhanda Sasiya Kulira

Ngati Mwana Wanu Wakhanda Sasiya Kulira

Ngati Mwana Wanu Wakhanda Sasiya Kulira

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU CANADA

MADOKOTALA anatsimikizira zimene mayiwo amangoganizira. Mwana wawo wakhanda anali ndi matenda a ntchofu. Nyuzipepala ya Globe and Mail ya ku Canada inati matendaŵa “amagwira mwana mmodzi pa ana anayi alionse.” Mwana amadziŵika kuti ali ndi matendaŵa mwina ngati akulira kwa maola angapo kwa masiku osachepera atatu pamlungu. Kodi makolo amene akuda nkhaŵa angachitepo chiyani? Madokotala a ana amati nthaŵi zambiri makolowo ndi anawo amafunika kungodikira basi. Koma kodi angadikire kwa nthaŵi yaitali motani?

Zimene afufuza posachedwapa ku Canada pakati pa amayi a ana odwala ntchofu zaonetsa kuti ana 85 pa 100 alionse odwala matendaŵa amachira akakwanitsa miyezi itatu. Kafukufukuyu, yemwe anayambitsidwa ndi Dr. Tammy Clifford, amene ali mkulu woona za matenda pa bungwe la Children’s Hospital of Eastern Ontario Research Institute, anaonetsanso kuti kukhala ndi mwana wodwala ntchofu sikusokoneza maganizo a mayiyo kwa nthaŵi yaitali. Dr. Clifford anati: “Potha miyezi sikisi amayi ameneŵa amangokhala ngati amayi ena onse opanda ana odwala ntchofu. Zimakhala ngati kuti mwanayo akaleka kulira, basi mayiwo amaiwala zonse zimene wakumana nazo.”

Nyuzipepala ya Globe ija inati zimene afufuza posachedwazi, zomwe zinafalitsidwa ndi Dr. Clifford ndi anzake, “zathandiza kwambiri pa zimene asayansi akudziŵa za matenda a ntchofu chifukwa zaonetsa kuti ana odwala matendaŵa alipo magulu atatu. Pali ana amene amagwidwa ndi matendaŵa n’kuchira pasanapite miyezi itatu. Ndiye pali ana ena amene matendaŵa amawatengetsa kwa miyezi ingapo popanda kuchepako. Ndiyenso pali kagulu kochepa ka ana amene amadzadwala matendaŵa mochedwerapo, patatha miyezi ingapo atabadwa.” Pakali pano ayambanso kufufuza kuti atsate bwinobwino kakulidwe ka ana a ntchofu, ndipo gulu lomalizali ndi limene makamaka akufuna kulimvetsa bwino.

Zikuoneka kuti kulira mosalekeza n’kumene kumachititsa kuti ana akhale ndi vuto lobwera chifukwa chowagwedeza. Malingana ndi zimene nyuzipepala ya Globe inanena, “kulirako pakokha sikuvulaza mwana ayi, koma kugwedeza mwanayo kwambiri pomutonthoza, ngakhale kwa kanthaŵi kochepa chabe, kungathe kumuwononga ubongo, mwinanso kumupha kumene.”

Komano, kulirako pakokha, ngakhale kutakhala kosalekeza, kungakhale m’pabwino pake. Nyuzipepala ya Globe inati, “ofufuza apeza kuti ana amene amakonda kulira amasamalidwa kwambiri ndipo amawasisita, kuwamwetulira, kuwalankhula ndiponso kuwakumbatira kaŵirikaŵiri.”