Anthu Osautsika Maganizo
Anthu Osautsika Maganizo
NICOLE wakhala akulimbana ndi vuto lokhala wosasangalala kungoyambira ali ndi zaka 14. Koma, atafika zaka 16 anadabwa kuona kuti wayamba kusangalala modabwitsa ndiponso kumakhala ndi mphamvu zosaneneka. Anayamba kuganiza zambirimbiri, kulankhula zosamveka ndiponso kusagona mokwanira komanso anali kunena zinthu zopanda umboni kuti anzake akum’dyera masuku pamutu. Kenaka Nicole anayamba kunena kuti atafuna angathe kusintha mtundu wa chinthu chinachake popanda kuchigwira n’komwe. Zitafika pamenepa mayi ake anazindikira kuti Nicole akufunikira kuonana ndi dokotala, motero anapita naye kuchipatala. Ataonetsetsa zochitika zake, madokotala anadziŵa kuti Nicole akudwala matenda a maganizo omwe munthu amasinthasintha zochitika, kumati pena asangalale monyanyira ndipo kenaka panthaŵi ina n’kungoipidwa kwambiri. *
Monga Nicole, anthu ochuluka zedi padziko lonse ali ndi matenda enaake a maganizo, mwina amene munthu amasinthasintha zochitika kapena amene munthu amangokhala woipidwa. Anthu amasauka nawo kwambiri matendaŵa. Steven, yemwe ali ndi matenda ochititsa munthu kusinthasintha zochitika, anati: “Kwa zaka zambiri maganizo akhala akundisautsa kwabasi. Nthaŵi zina ndinali kulefuka maganizo kwambiri ndipo kenaka m’thupimu munkangobwera mphamvu zochita kunyanya. Kuchipatala anandithandiza ndithu, komabe sizinali zophweka.”
Kodi n’chiyani chimachititsa matenda osiyanasiyana a maganizo? Kodi zimakhala bwanji munthu ukakhala ndi matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa kapena amene amachititsa munthu kusinthasintha zochitika? Kodi odwala matendaŵa ndiponso owasamalira angathandizidwe bwanji pa zimene amafunikira?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Dziŵani kuti zizindikiro zina zotere zimasonyeza kuti munthu akuchita misala, akugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, kapena zingakhalenso zimene zimachitika mwachibadwa wachinyamata akamakula. Munthu angadziŵike kuti alidi ndi matenda ameneŵa pokhapokha ataonedwa bwinobwino ndi dokotala wodziŵa bwino za matendaŵa.