Mwana Wanu Akatentha Thupi
Mwana Wanu Akatentha Thupi
“Sindikumva bwino!” Mwana wanu akamalira momvetsa chisoni chonchi, mungafune kudziŵa mofulumira ngati thupi lake latentha. Ngati thupi lake latentha, mungayambe kuda nkhaŵa.
Malinga ndi kafukufuku wina amene a chipatala cha ana cha Johns Hopkins Children’s Center ku Baltimore, Maryland, U.S.A., anachita, anapeza kuti makolo 91 mwa makolo 100 aliwonse amakhulupirira kuti “ngakhale kungotentha thupi pang’ono chabe kungachititse vuto linalake ndithu, monga kudwala matenda aakulu mwadzidzidzi kapena kuwonongeka kwa ubongo.” Kafukufuku yemweyo anasonyezanso kuti “makolo 89 mwa makolo 100 aliwonse anapatsa ana awo mankhwala ochepetsa kutentha kwa thupi, thupilo lisanatenthe kufika 38.9 digiri seshasi.”
Kodi muyenera kuda nkhaŵa motani mwana wanu akatentha thupi? Nanga kodi njira zabwino zochepetsera kutentha kwa thupi n’ziti?
Kufunika kwa Kutentha Thupi
Kodi chimayambitsa kutentha thupi n’chiyani? Ngakhale kuti thupi likamatentha bwinobwino limatentha cha m’ma 37 digiri seshasi (akayeza m’kamwa), kutentha kwa thupi kuyambira m’maŵa kufika madzulo nthaŵi zambiri kumasintha ndi digiri imodzi kapena ambiri. * Choncho kutentha kwa thupi lanu kungakhale kotsika mmaŵa ndipo kungakhale kokwera chakumadzulo. Kachiwalo kotchedwa hypothalamus komwe kali mmunsi mwa ubongo, kamayendetsa kutentha kwa thupi mofanana ndi chipangizo chamagetsi chimene chimapangitsa kuti kutentha kapena kuzizira kusapitirire mlingo woyenera. Thupi limayamba kutentha ngati mphamvu ya thupi yotiteteza kumatenda, polimbana ndi mabakiteriya kapena mavairasi amene aloŵa m’thupilo, ikutulutsa timadzi tam’magazi totchedwa pyrogens, timene timachititsa kuti thupi litenthe. Zimenezi zimachititsa mbali ya ubongo imene imalamulira kutentha kwa thupi “kuchuna” kuti thupi lizitentha kwambiri.
Ngakhale kuti kutentha kwa thupi kungachititse kuti munthu asamve bwino ndiponso kungachepetse madzi a m’thupi, sikuti ndi koopsa kwenikweni.
Mogwirizana ndi zimene bungwe lochita kafukufuku la Mayo Foundation for Medical Education and Research linapeza, zikuoneka kuti kutentha thupi n’kofunika kwambiri pothandiza thupi kuti lizilimbana ndi mabakiteriya ndi mavairasi. “Timavairasi timene timayambitsa chimfine ndi matenda ena okhudzana ndi kupuma timakonda nyengo yozizira. Choncho, ngati thupi lanu likutentha pang’ono lingakhale likulimbana ndi mavairasi.” Motero, ochita kafukufuku ameneŵa anapitiriza kunena kuti “kuchepetsa kutentha thupi kosadetsa nkhaŵa n’kosayenera ndipo kungafooketse mphamvu zochiza zachibadwa za mwana wanu.” N’zochititsa chidwi kuti chipatala china ku Mexico chimachiza matenda ena powonjezera kutentha kwa thupi ndipo chithandizo chimenechi amachitcha kutenthetsa thupi.Dr. Al Sacchetti wa ku American College of Emergency Physicians anati: “Nthaŵi zambiri kutentha thupi pakokha si vuto. Komabe ndi chizindikiro chakuti m’thupi mwaloŵa tizilombo toyambitsa matenda. Choncho, mwana akatentha thupi, muyenera kuyang’anitsitsa zimene mwanayo akuchita, ndi matenda amene angakhale m’thupi mwake, osati mmene thupi la mwanayo likutenthera.” A bungwe la American Academy of Pediatrics anati: “Kutentha thupi kosafika 38.3 digiri seshasi nthaŵi zambiri n’kosafunika kukuziziritsa pokhapokha ngati mwana wanu akuvutika kapena ngati ali kale ndi vuto limene limayamba chifukwa chotentha thupi. Ngakhale kutentha thupi kwambiri pakokha sikoopsa pokhapokha ngati mwana wanu ali kale ndi vuto la matenda a khunyu kapena matenda okhalitsa. M’pofunika kuonetsetsa kwambiri mmene mwana wanu akuchitira zinthu. Ngati akudya ndi kugona bwino, ndipo nthaŵi zina akuseŵera bwinobwino, mwina sakufunikira chithandizo chilichonse.”
Zimene Mungachite Mwana Akatentha Thupi
Zimenezi sizikutanthauza kuti palibe chimene mungachite kuti muthandize mwana wanu. Akatswiri ena odziŵa zachipatala amavomereza njira zotsatirazi zochepetsera kutentha thupi pang’ono: Chipinda cha mwana wanu chikhale chozizira * (Zakumwa zokhala ndi mankhwala otchedwa caffeine monga kokakola kapena tiyi, zimachititsa kukodzakodza ndipo zingachititse madzi kucheperachepera m’thupi.) Muyenera kupitiriza kuyamwitsa ana oyamwa. Pewani zakudya zovuta kugaya chifukwa kutentha thupi kumachititsa kuti m’mimba musamagwire ntchito kwambiri.
bwino. Vekani mwanayo zovala zopepuka. (Zovala zokhuthala zingawonjezere kutentha kwa thupi.) Limbikitsani mwana kumwa zinthu monga madzi, madzi azipatso osungunula, ndi msuzi, chifukwa kutentha thupi kungachititse kuti madzi athe m’thupi.Mwana wanu akatentha thupi mopitirira 38.9 digiri seshasi, kaŵirikaŵiri mungam’patse mankhwala osachita kukulemberani kuchipatala othandiza kuchepetsa kutentha kwa thupi, monga panado kapena bulufeni. Komabe, m’pofunika kwambiri kutsatira kamwedwe kamene alemba pa chikutiro chake. (Musapatse ana osakwana zaka ziŵiri mankhwala ena aliwonse musanauzidwe ndi dokotala.) Mankhwala othandiza kuchepetsa kutentha kwa thupi sapha mavairasi oyambitsa matenda. Choncho, sachiza mwamsanga mwana ngati akudwala chimfine kapena matenda ena ofanana ndi ameneŵa, koma angachepetseko vutolo. Akatswiri ena amati ana amene sanakwanitse zaka 16 asamapatsidwe asipulini kuti achepetse kutentha thupi, chifukwa akhoza kuyambitsa matenda a Reye syndrome omwe ndi matenda oopsa kwambiri. *
Mungathe kuchepetsanso kutentha thupi mwa kumusambitsa mwanayo pongomupukuta ndi kansalu konyowa. Muikeni mwanayo m’bafa losambira limene mwathiramo madzi ofunda ochepa, ndipo mupukuteni ndi kansalu konyowa. (Musagwiritse ntchito mankhwala amene amagwiritsa ntchito potikita minofu, chifukwa angakhale oopsa.)
Bokosi limene lili m’nkhani ino lili ndi mfundo zothandiza zokhudza nthaŵi imene munthu angapite kwa dokotala. Kulandira chithandizo kuchipatala n’kofunika kwambiri makamaka kwa munthu amene amakhala ku dera limene matenda otenthetsa thupi modetsa nkhaŵa monga zingwangwa, mavairasi a Ebola, tayifodi, kapena matenda amene thupi la munthu wodwalayo limasanduka lachikasu, ndi ofala.
Komabe, cholinga chanu kwenikweni ndi choti mwana wanu apeze bwino. Kumbukirani kuti sizichitika kaŵirikaŵiri kuti kutentha thupi kukhale koopsa kwambiri moti n’kuchititsa matenda osokoneza bongo kapena imfa. Ngakhale kuti matenda aakulu adzidzidzi oyamba chifukwa cha kutentha thupi angakhale oopsa, nthaŵi zambiri sakhalitsa.
N’zoona kuti kupeŵa ndi mankhwala abwino, ndipo njira yogwira mtima kwambiri yotetezera mwana wanu ku matenda ndi kum’phunzitsa ukhondo. Ana ayenera kuphunzitsidwa kusamba m’manja mwawo nthaŵi ndi nthaŵi, makamaka asanayambe kudya, akachoka ku chimbudzi, akachoka pagulu, kapenanso akamaliza kuseŵera ndi ziweto. Ngati zitachitika kuti ngakhale mutayesetsa motani mwana wanu akutenthabe thupi, musapupulume. Monga mmene taoneramu, pali zambiri zimene mungachite kuti muthandize mwana wanu kupeza bwino.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Kutentha kwa thupi kumasiyanasiyana malinga ndi malo amene mwayeza ndi mtundu wa choyezera kutentha kwa thupi chotchedwa thermometer chimene mwagwiritsa ntchito.
^ ndime 10 Onani mu Galamukani! ya April 8, 1995 tsamba 11, za mmene mungapangire mankhwala obwezeretsa madzi m’thupi amene mungagwiritse ntchito ngati mwana watentha thupi ndiponso akutsegula m’mimba kapena kusanza.
^ ndime 11 Matenda a Reye syndrome ndi matenda oopsa okhudza ubongo amene amagwira ana ndipo amayamba chifukwa cha mavairasi.
[Bokosi patsamba 29]
Pitani kwa Dokotala Ngati Mwana Wotentha Thupi . . .
▪ Ali ndi miyezi itatu kapena sanakwane miyezi itatu ndipo kotulukira chimbudzi kukutentha 38 digiri seshasi kapena kupitirira pamenepo
▪ Ali ndi miyezi ya pakati pa itatu ndi isanu ndi umodzi ndipo akutentha thupi 38.3 digiri seshasi kapena kupitirira pamenepo
▪ Ndi woposa miyezi isanu ndi umodzi ndipo akutentha thupi 40 digiri seshasi kapena kupitirira pamenepo
▪ Akukana zakumwa ndipo ali ndi zizindikiro zakuti alibe madzi m’thupi
▪ Wadwala matenda aakulu mwadzidzidzi kapena ndi wofooka kwambiri
▪ Akutenthabe thupi patapita masiku atatu
▪ Akulira mosatonthozeka kapena akusonyeza zizindikiro za matenda a khunyu kapena kubwebweta
▪ Watuluka nsungu pakhungu, akupuma movutikira, akutsegula m’mimba, kapena akusanza mobwerezabwereza
▪ Sakutha kutembenuza khosi kapena akudwala mutu modetsa nkhaŵa
[Mawu a Chithunzi]
Kumene zachokera: The American Academy of Pediatrics