Mafuta—Kodi Adzatha?
Mafuta—Kodi Adzatha?
“Popanda [mphamvu zoyendetsera zinthu zosiyanasiyana] mafakitale sangayende . . . Galimoto, sitima za pamtunda, za pamadzi kapenanso ndege sizingapangidwe . . . Popanda mphamvu zotere, nyumba zingakhale zozizira ndiponso zamdima, chakudya nacho sichingaphikidwe. . . . Popanda zinthu zimene zili ndi mphamvu zoterezi tingabwererenso pomakhala moyo wakumbuyo wanthaŵi ya makedzana.”—Zachokera m’lipoti lotchedwa “U.S. Geological Survey World Petroleum Assessment 2000.”
AKATSWIRI oona za mphamvu zoyendetsera zinthu zosiyanasiyana amati n’kutheka kuti zitsime za mafuta zidzauma m’tsogolo muno. Ena amati kwatsala zaka zoyambira pa 63 mpaka 95 kuti mafuta amene angathe kukumbidwa padziko lonse atheretu. Pakali pano, anthu akugwiritsanso ntchito mphamvu zochokera ku zinthu zina, ndipotu zina mwa izo azigwiritsira ntchito kwa zaka zambiri. Zina mwa mphamvuzi n’zoti zimabwereramo mwamsanga mukatha kuzigwiritsa ntchito ndipo zimachokera ku zinthu monga izi: dzuŵa, mphepo, kunjenjemera kwa zinthu zinazake, magetsi ochokera ku madzi, ndiponso kutentha kwa m’nyanja. Koma pakali pano mavuto aakulu adakali okhudza njira zotulutsira mphamvuzo kuchokera ku zinthuzi ndiponso kupititsa mphamvuzo m’madera ena.
Inde n’zofoola kuganiza kuti zikadzatha zinthu zonse zimene zimatulutsa mphamvu zosatha kubwereramo, m’pamene tidzayambe kugwiritsira ntchito zinthu zina zotulutsa mphamvu zimene zimatha kubwereramo. Makampani oyenga mafuta a pansi panthaka akuchita zonse zimene angathe kuti apope mafuta ambiri zedi pa nthaŵi yochepa imene akuti mafuta akhala alipobe. Tsoka ilo pali zifukwa zokwanira zoyembekezera kuti kwa nthaŵi yonse imeneyo nawonso mavuto okhudza anthu ndiponso chilengedwe amene amabwera chifukwa cha mafuta adzakhalapobe. Koma n’zachidziŵikire kuti chimayambitsa mavutoŵa sikuti ndi mafutawo paokha ayi. Umbombo wa anthu ndiponso mtima wofuna kulamulira ena n’zimene zachititsa kuti mbiri ya mafuta iipe motere.
Mwayi wake, tsogolo la mafuta, ndiponso la zinthu zonse zimene zili ndi mphamvu zotere, silili m’manja mwa anthu. Kwenikweni, lili m’manja mwa Mlengi wa dzikoli amenenso ali Wolisamala, Yehova Mulungu. Iyeyu walonjeza kuti posachedwapa sikudzakhalanso vuto lililonse lokhudza chilengedwe kapenanso anthu lomwe lilipo chifukwa cholephera kugwiritsira ntchito bwino ndi kuwononga zinthu za padziko lapansi. (Chivumbulutso 4:11) Baibulo limati, nthaŵi imene Mulungu ‘adzawononge iwo akuwononga dziko’ yayandikira. Ulamuliro wolungama wa Mulungu udzabweretsa “m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano,” lomwe silidzakhala ndi khalidwe logwiritsira ntchito zinthu mwaumbombo ndiponso losoŵa chilungamo, ndipo m’dzikomo zinthu za padziko lapansi zidzagwiritsiridwa ntchito mokomera anthu onse omvera Mulungu.—Chivumbulutso 11:18; 21:1-4.
[Zithunzi patsamba 12]
Zinthu zina zomwe zimapanga mphamvu zoyendetsera zinthu ndi mapanelo ogwira mphamvu ya dzuŵa ndiponso makina opanga mphamvu kuchokera ku mphepo