Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupezerera Ena ndi Vuto la Padziko Lonse

Kupezerera Ena ndi Vuto la Padziko Lonse

Kupezerera Ena ndi Vuto la Padziko Lonse

“Ngati maŵa ubwere kusukulu, tidzakupha.”—Mwana wasukulu wina wa ku Canada dzina lake Kristen anaopsezedwa choncho pa telefoni ndi mtsikana wina yemwe sanatchule dzina lake. *

“Sindichita zinthu mothamanga magazi, koma ndinafika poti sindinkafuna kupita kusukulu. M’mimba munali kundipweteka, ndipo m’maŵa uliwonse ndikadya ndinali kusanza.”—Anatero Hiromi, mtsikana wapasukulu ku Japan, pokumbukira zimene ana opezerera anzawo anali kumuchitira.

KODI munayamba mwakhalapo ndi munthu wokonda kupezerera anthu ochepa mphamvu? Ambiri a ife panthaŵi inayake tinakhalapo ndi anthu oterowo. Mwina kunali kusukulu kapena kuntchito. Kapenanso panali panyumba pamene, chifukwatu masiku ano zimamveka kaŵirikaŵiri kuti anthu akuzunzana panyumba. Mwachitsanzo, nkhani ina ya ku Britain inayerekezera kuti anthu akuluakulu 53 mwa 100 alionse, amuna awo kapena akazi awo ngakhalenso munthu woti anangoloŵana naye, amawalankhula mowapweteketsa mtima. Anthu opezerera anzawo ochepa mphamvu angakhale amuna kapena akazi ndipo angakhale wina aliyenseyo kwina kulikonseko padziko lapansi.

Kodi tikati kupezerera anthu ochepa mphamvu tikunena chiyani makamaka? Si kofanana kwenikweni ndi kuzunza kapena kuukira munthu wina. Wopezerera anzake amachitira anzakewo tinthu ting’onoting’ono tambiri kwa nthaŵi yaitali, osati kuchita chinthu chimodzi chokha kapena zingapo chabe. Katswiri wa zamaganizo Dan Olweus, yemwe anayambitsa zochita kafukufuku pa nkhaniyi, anatchula zimene zimaoneka mwa anthu ambiri amene ali ndi khalidweli. Iye anati, amachita zamtopola ndiponso amaonekeratu kuti ndi amphamvu kuposa amene akuwapezererawo.

N’zosatheka kupereka tanthauzo limodzi la kupezerera ochepa mphamvu lomwe lingafotokoze chilichonse chokhudza khalidweli, koma ena anena kuti ndiko “kudzipatsa dala chilakolako chofuna kupweteka munthu wina n’kumuchititsa kukhala wopanikizika.” Munthuyo amapanikizika osati kokha ndi zimene zimachitika, komanso chifukwa choopa zimene zingachitike. Wopezerera anzakeyo angachite zimenezi mwa kunyazitsa mnzakeyo, kumangomunena nthaŵi zonse, kumunyoza, kumunena miseche, ndi kumuuza kuchita zinthu zosatheka.—Onani bokosi patsamba 4.

Kristen, mtsikana tinamutchula poyamba uja, anali kumupezerera nthaŵi zambiri pamene anali pasukulu. Ali kupulayimale, ana ena ankamuika chingamu m’tsitsi, ankamuseka chifukwa cha mmene amaonekera, ndipo ankamuopseza kuti amumenya. Zinthu zinanyanyira atapita kusekondale, mpaka anafika polandira matelefoni omuopseza kuti amupha. Iye tsopano ali ndi zaka 18, ndipo anadandaula kuti: “Kusukulu ndi kumalo kumene timapita kukaphunzira, osati kukaopsezedwa kuti akupha kapena kukavutitsidwa.”

Katswiri wina wa zamaganizo anati: “Ndi zomvetsa chisoni koma zimachitika kaŵirikaŵiri pakati pa anthu. Anthu ena amasangalala ndi kunyozetsa anzawo.” Khalidweli likapitirira, lingachititse wopezereredwayo kubwezera mwachiwawa kapenanso ngakhale kupha anthu kumene. Mwachitsanzo, mwamuna wina wogwira ntchito m’kampani ya maulendo, yemwe anali kulankhula movutikira, anzake ankamuseka ndi kumupezerera kwambiri moti mpaka iye anapha anzake folo ogwira nawo ntchito kenako iyenso n’kudziombera.

Kupezerera Ena Kukuchitika Padziko Lonse

Kulikonse padziko lapansi ana a sukulu ena amapezerera anzawo ochepa mphamvu. Kafukufuku wina amene analembedwa m’magazini yotchedwa Pediatrics in Review anaonetsa kuti ku Norway, ana 14 mwa ana 100 alionse amapezerera anzawo kapena amapezereredwa ndi ena. Ku Japan, ana 15 mwa 100 alionse a kupulayimale amati anzawo amawapezerera, pamene ku Australia ndi ku Spain vutoli limachitikira ophunzira 17 mwa 100 alionse. Ku Britain katswiri wina anaŵerengera kuti ana okwana 1.3 miliyoni amakhudzidwa ndi nkhaniyi.

Pulofesa Amos Rolider wa pa koleji ya Emek Yizre’el anafunsa ana 2,972 m’masukulu 21. Malinga ndi nyuzipepala ya The Jerusalem Post, pulofesayu anapeza kuti “mwa ophunzira 100 alionse, ophunzira 65 anadandaula kuti anzawo amawawomba makofi, kuwamenya mateche, kuwakankha kapena kuwavutitsa.”

Zochitika zina zatsopano zomwe zimavulaza mwakabisira ndizo kutumizirana mauthenga oopsezana pa matelefoni am’manja ndi pamakompyuta. Achinyamata amalembanso nkhani pa Intaneti zosonyeza kudana ndi winawake, ndipo amalongosolanso mmene ena angazindikirire munthuyo. Malinga ndi kunena kwa Dr. Wendy Craig wa pa yunivesite ya Queen ku Canada, kupezerera ochepa mphamvu mwa njira imeneyi “kumawononga kwambiri moyo wa mwana yemwe akumupezererayo.”

Kuntchito

Kupezerera anthu ochepa mphamvu kuntchito ndi chinthu chimodzi mwa zinthu zimene zikuchititsa anthu ambiri kudandaula kuti kuntchito kumachitika zachiwawa. Ndipotu mayiko ena akuti zoterezi n’zofala kwambiri kuposa kusankhana mitundu kapena kuvutitsa akazi. Chaka chilichonse, pafupifupi munthu mmodzi mwa anthu asanu ogwira ntchito ku United States anzake amamupezerera.

Ku Britain, lipoti lina lomwe inatulutsa yunivesite ya Manchester Institute of Science and Technology m’chaka cha 2000 linati mwa anthu 5,300 ogwira ntchito m’mabungwe 70, anthu 47 mwa 100 alionse anati anaonapo zoterezi zikuchitika m’zaka zisanu za m’mbuyomo. Ndipo m’chaka cha 1996 bungwe la European Union linachita kafukufuku mwa kufunsa mafunso 15,800 m’mayiko 15 omwe ali m’bungweli. Kafukufukuyu anaonetsa kuti anthu ogwira ntchito okwana pafupifupi 12 miliyoni, omwe ndi anthu 8 pa 100 alionse, anaopsezedwapo kapena anzawo anali kuwapezerera.

Kaya zikuchitikira kusukulu kapena kuntchito, khalidwe lopezerera ochepa mphamvuli limafanana chimodzi, chomwe ndi kugwiritsa ntchito mphamvu pofuna kupweteka kapena kuchititsa manyazi munthu wina. Komano n’chifukwa chiyani anthu ena amapezerera anzawo? Kodi zotsatirapo zake n’zotani? Nanga kodi pali chilichonse chimene chingachitike pothana ndi vutoli?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha mayina ena.

[Bokosi patsamba 12]

Kupezerera Ena Kumachitika M’njira Izi

Mphamvu: Pa zonse, njira iyi ndi yosavuta kwambiri kuizindikira. Anthu ake amaonetsa ukali wawo mwa kumenya, kukankha, kapena kumenya mateche munthu amene akumupezererayo, mwinanso kumuwonongera zinthu zake.

Mawu: Amene amapezerera anzawo mwa njirayi amalankhula mawu opweteka kapena ochititsa manyazi winawake, mwa kumupatsa mayina achipongwe, kumunyoza, kapena kumunyazitsa mosalekeza.

Kuipitsirana Mbiri: Amafalitsa mphekesera zonyansa zonena za winawake. Khalidweli amalikonda kwambiri ndi akazi.

Kubwezera: Ena amene anali kupezereredwa nawonso amayamba kupezerera anzawo. Komatu sikuti popeza iwo anali kupezereredwa ndiye m’pake kuti nawonso azipezerera ena; kungoti zimathandiza kumvetsa chifukwa chake anayamba kuchita zimenezo.

[Mawu a Chithunzi]

Zachokera m’buku lakuti Take Action Against Bullying, lolembedwa ndi Gesele Lajoie, Alyson McLellan, ndi Cindi Seddon