Kodi Kudana ndi Anthu Amitundu ina N’koyenera?
Lingaliro la Baibulo
Kodi Kudana ndi Anthu Amitundu ina N’koyenera?
KODI mungamve bwanji anthu ena atamakuganizirani kuti ndinu tambwali, munthu wankhanza, wachabechabe, kapena kuti ndinu wamakhalidwe oipa, chabe chifukwa chakuti ndinu wamtundu winawake? * Mosakayikira zimenezo zingakupwetekeni kwambiri. Mwatsoka, zimenezo n’zimene zakhala zikuchitikira anthu ambirimbiri. Komanso kuyambira kale kwabasi, anthu ambirimbiri osalakwa akhala akuchitidwa nkhanza mwinanso kuphedwa kumene, chifukwa cha fuko kapena mtundu wawo basi. Ndipotu nkhondo zoopsa kwambiri zimene zikuchitika masiku ano, chiyambi chake chimakhala kudana ndi anthu amitundu inayake. Koma chonsecho anthu ambiri amene amagwirizana nazo nkhanza zoterozo amati amakhulupirira Mulungu ndiponso Baibulo. Ndiyeno palinso anthu ena amene amati kusankhana mitundu ndi mmene anthu anapangidwira, ndipo sikudzatha mpaka kalekale.
Kodi Baibulo limalola kuti chidani choterechi chikhalepo? Kodi zilipo zochitika zina zimene zingalungamitse zodana ndi anthu osiyana nawo chikhalidwe kapena fuko? Kodi tingayembekezere kuti kutsogoloku sikudzakhalanso zodana ndi anthu a mitundu ina? Nanga Baibulo limati bwanji?
Anawaweruza Mogwirizana ndi Zochita Zawo
Munthu atangoŵerenga mothamanga zimene poyambirira Mulungu ankachita ndi anthu onse akhoza kumva molakwa, n’kungoganiza kuti basi, Mulungu ankalimbikitsa zodana ndi mitundu ina. Suja nkhani zingapo m’Baibulo zimasonyeza kuti Mulungu ankapha anthu onse m’mitundu ina ndiponso m’mayiko ena? Inde zilidi choncho, koma titaonanso bwinobwino tipeza kuti Mulungu anaweruza anthuŵa chifukwa cha kuswa malamulo ake osati chifukwa chokhala a mitundu inayake ayi.
Mwachitsanzo, Yehova Mulungu anaweruza Akanani chifukwa chakuti anali ndi miyambo yonyansa yochita zachiwerewere ndi zauchiwanda. Anafika mpaka pomaotcha ana awo popereka nsembe kwa milungu yonyenga! (Deuteronomo 7:5; 18:9-12) Komabe nthaŵi zina Akanani ena ankayamba kukhulupirira Mulungu n’kulapa. Zikatero, Yehova ankawapulumutsa n’kuwadalitsa. (Yoswa 9:3, 25-27; Ahebri 11:31) Mkazi wina wa ku Kanani, dzina lake Rahabe anafikanso mpaka pokhala m’gulu la makolo a Yesu Kristu, yemwe ndi Mesiya amene anthu analonjezedwa.—Mateyu 1:5.
Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisrayeli chimasonyeza kuti iye alibe tsankho. Koma m’malo mwake, iye amaganizira zoti anthu onse azikhala osangalala. Pa lemba la Levitiko 19:33, 34, timapezapo lamulo lokoma mtima limene Mulungu anauza Aisrayeli kuti: “Mlendo akagonera m’dziko mwanu, musamam’sautsa. Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; um’konde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m’dziko la Aigupto; ine ndine Yehova Mulungu wanu.” Malamulo ena otere timawapeza m’mabuku a Eksodo ndi Deuteronomo. N’zoonekeratu apa kuti Yehova sankalungamitsa zodana ndi mitundu ina. Iye ankalimbikitsa zoti mitundu yosiyanasiyana izigwirizana.
Yesu Analimbikitsa Zoti Mitundu Izigwirizana
Panthaŵi imene Yesu anali pano padziko lapansi, Ayuda ndi Asamariya ankakonda kunyozana. Nthaŵi inayake anthu a m’mudzi winawake wa ku Samariya anakana kulandira Yesu kokha chifukwa chakuti anali Myuda ndipo ankapita ku Yerusalemu. Mukanakhala inu mukanatani zimenezo zitakuchitikirani? N’kutheka kuti ophunzira a Yesu anaonetsa mtima watsankho womwe unali wofala m’nthaŵi imeneyo pamene anafunsa kuti: “Ambuye, kodi mufuna kuti ife tiuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo?” (Luka 9:51-56) Kodi Yesu analola zoti atengeke ndi kuipidwa kwa ophunzira ake? Ayi ndithu, m’malo mwake iye anawadzudzula ndipo anangochoka mwamtendere n’kukafuna malo ena ogona m’mudzi wina. Kenaka posakhalitsa, Yesu anakamba fanizo la Msamariya wachifundo. Fanizoli linasonyezeratu kuti sikuti munthu akakhala wochokera kumtundu kwinakwake ndiye kuti ameneyo ndi mdani. Zoona n’zakuti munthuyo amatha kusanduka mnansi wabwino kwambiri!
Anthu Amitundu Yosiyanasiyana Mumpingo Wachikristu
Nthaŵi imene Yesu ankatumikira ali pansi pano, iye anali kuphunzitsa makamaka anthu amtundu wake. Komano anasonyeza kuti m’kupita kwanthaŵi anthu amitundu ina adzakhalanso otsatira ake. (Mateyu 28:19) Kodi zikanatheka kuti anthu ochokera m’mitundu yonse akhale ovomerezeka? Inde kumene! Mtumwi Petro ananena kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Kenaka mtumwi Paulo anadzathirira umboni pamfundo imeneyi pamene anafotokoza momveka bwino kuti mumpingo wachikristu zilibe ntchito zakuti kaya munthu ndi wochokera kumtundu wanji.—Akolose 3:11.
Umboni wina wakuti Mulungu amavomereza anthu ochokera m’mitundu yonse ukupezeka m’buku la Chivumbulutso, m’Baibulo. M’masomphenya ochokera kwa Mulungu, mtumwi Yohane anaona “khamu lalikulu” la anthu opulumutsidwa ndi Mulungu “ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9, 10) “Khamu lalikulu” limeneli lidzakhala chiyambi cha gulu latsopano la anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana amene azidzakhalira pamodzi mwamtendere ndiponso ali ogwirizana chifukwa cha kukonda kwawo Mulungu.
Pakali pano, Akristu ayenera kupeŵa kamtima komaweruza ena chifukwa chosiyana nawo mtundu. Chinthu chabwino kuchita ndiponso chosonyeza chikondi ndicho kutenga munthu aliyense payekha n’kumamuona monga mmene Mulungu amamuonera, osati kumangoganizira zakuti ndi wochokera kumtundu wakutiwakuti. Kodi si mmene inuyo mumafunira kuti anthu ena azikuonerani? Moyenerera Yesu amatilimbikitsa kuti: “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Zimakhala bwino kwambiri tikamakhala popanda kudana ndi anthu amitundu ina. Zimachititsa kuti moyo tiziumva kukoma ndiponso kuti tizikhalitsana bwino ndi anzathu. Koma chachikulu n’chakuti kuteroko kumachititsa kuti tikhale anthu ogwirizana ndi Mlengi wathu wopanda tsankho, Yehova Mulungu. Chimenechitu n’chifukwa chokwaniradi chopeŵera kudana ndi anthu amitundu ina!
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Mawu akuti “mtundu” mu nkhani ino akutchula za anthu ofanana fuko, a dziko limodzi, kapena a chikhalidwe chimodzi.