Chimene Anthu Akusinthira
Chimene Anthu Akusinthira
“Kodi chofunika kwambiri m’moyo n’chiyani?”
Anthu 50,000 a m’mayiko 60 anafunsidwa funso limeneli. Ofufuza anati anthu ambiri pafupifupi m’madera onse adzikoli ankayankha kuti chofunika kwambiri ndicho “kukhala ndi banja labwino” ndiponso “kukhala wathanzi.”
POPANDA kuganizira mozama, munthu ungaone ngati kuti anthu onse padziko amaganiza mofanana pa nkhani ya mfundo zabwino zoyenera kuzitsatira m’moyo. Komatu munthu angakhumudwe atadziŵa zoona zenizeni zokhudza nkhaniyi. M’mbuyomo, anthu ankatsatira mfundo zogwirizana ndi miyambo ya chipembedzo komanso chikhalidwe chawo. Komano zinthu zikusintha msangamsanga masiku ano. Pofotokoza zimene zikuchitika ku Italy, wofufuza wina, Marisa Ferrari Occhionero, anati: “Mfundo zimene ana akutsatira sizikuchokeranso kwa makolo awo, chikhalidwe chawo ngakhalenso chipembedzo chawo.” Anthu ena onse padziko lonse, akulu ndi ana omwe, akuchitanso chimodzimodzi.
Pulofesa Ronald Inglehart, amene anatsogolera kafukufuku wina wofuna kuona za makhalidwe a anthu padziko lonse, anati: “Pali umboni wochuluka wosonyeza kuti maganizo a anthu akusintha kwambiri.” Kodi n’chiyani chikuchititsa kusintha kumeneku? Pulofesa Inglehart anati: “Zikungokusonyeza kusintha kumene kukuchitika pa ntchito zachuma ndiponso zaumisiri.”
Mwachitsanzo, pa kafukufuku uja anapeza kuti m’mayiko olemera anthu saona kukhala pantchito ngati chinthu chofunikira kwambiri m’moyo. Komano kwa anthu a m’mayiko osauka, kukhala pantchito n’chinthu chofunikira kwambiri! Inde, anthu akakhala osauka, nkhaŵa yawo yaikulu imakhala yakuti tsiku limenelo apeza bwanji chakudya. Mayiko akamatukuka pazachuma, anthu amayamba kuganizira kwambiri zofuna kukhala munthu wathanzi, wa banja labwino, ndiponso wodzipangira zofuna zake.
Chifukwa chakuti ntchito zaumisiri zikupita patsogolo, n’zosachita kufunsa kuti nawonso anthu a m’mayiko osauka adzatengera maganizo atsopanoŵa. Magazini yotchedwa The Futurist inati: “Anthufe timakhulupirira ndiponso kutengera zinthu zinazake malingana ndi zimene timaona ndi kumva.” Motero anthu a kumayiko a azungu asintha kwambiri potengera zinthu za m’manyuzipepala, ma TV, ndi mawailesi. Magazini ya The Futurist inati: “Zinthu zimenezi zikuchititsa kuti anthu asinthe padziko lonse.”
Ndiyeno kodi n’kusintha kotani kumene tikuona pa kaganizidwe ndiponso makhalidwe a anthu? Kodi kusintha kwa zinthu kumeneku kukukukhudzani motani inuyo ndiponso banja lanu?