Vuto la Mankhwalaŵa Litha Posachedwapa Padziko Lonse
Vuto la Mankhwalaŵa Litha Posachedwapa Padziko Lonse
Ingoyerekezani kuti padziko lonse palibenso vutoli.
MLEMBI WAMKULU wa bungwe la United Nations a Kofi Annan analimbikitsa mayiko onse kuti ayesetse kuti zimenezi zidzathekedi. Iwo anati: “Tipeze njira zatsopano ndiponso zokhwima kuti tithetse vuto losautsali limene lawononga ana athu ambiri.”
Atsogoleri angathe kugwirizana kuti kupanga ndiponso kugulitsa mankhwalaŵa kuchepe padziko lonse, komano kukwanitsa zimenezi si ntchito yamaseŵera ayi. Hennadiy Udovenko wa ku Ukraine, amene anali wapampando wa msonkhano wapadera wa bungwe la United Nations General Assembly, ananena kuti “katangale wa mankhwala osokoneza bongo ali m’gulu la akatangale a ndalama zochuluka kwambiri . . . omwe amatha kusokoneza kayendedwe ka chuma cha padziko lonse. Anthu ochita katangale ameneyu amapeza ndalama zokwana pafupifupi madola 400 biliyoni pachaka.” Iye anapitiriza kunena kuti vutoli “lafalikira padziko lonse ndipo palibe dziko limene lingaone kuti silikukhudzidwa ndi vutoli.”
M’povuta kuganiza kuti padziko pano vutoli lidzatheratu. Ndipotu n’zosachita kufunsa kuti maboma a anthu alephereratu kulithetsa. Koma palibe aliyense amene angaletse Mulungu Wamphamvuyonse kukwaniritsa lonjezo lake losandutsa dzikoli paradaiso, ndipo m’paradaisomo zinthu zonse zofunika pa moyo wa munthu ndi zauzimu zomwe zidzakwaniritsidwa. (Salmo 145:16; Luka 23:43; 2 Petro 3:13) Mneneri Yesaya ananena kuti mawu a Mulungu sadzabwerera kwa iye chabe, koma adzachita chimene iyeyo akufuna, ndipo adzakwaniritsa zimene wawatumizira mosakayika n’komwe.—Yesaya 55:11.
Kuyembekezera malonjezo amenewo kungatipindulitse kwambiri ngakhale panopo. Mwachitsanzo, Edmundo anali ndi vutoli. Koma atayamba kukhulupirira lonjezo la m’Baibulo lakuti kukubwera dziko latsopano anaganizira mofatsa za moyo wake. Edmundo anati: “Ndachita zinthu zopusa kwambiri powononga nthaŵi yanga pachabe.” Koma chifukwa chofunitsitsa kuti Mulungu azimuyanjabe, panopo anatsimikiza mtima kuti asayambirenso khalidwe limeneli. Inde, kudziŵa Mulungu ndiponso zimene amalonjeza kungatilimbikitse ‘kuvala umunthu watsopano, umene unalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’—Aefeso 4:24.
Palinso anthu ena ambiri amene kale anali ndi vutoli koma tsopano anayamba kukondana kwambiri ndi Mlengi wawo. Anthu otere mawu a wamasalmo amangokhala ngati akunena za iwowo. Mawuŵa ndi akuti: “Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu: mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova. Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima: chifukwa chake adzaphunzitsa olakwa za njira.” (Salmo 25:7, 8) Koma ndiyetu n’zolimbikitsa kwambiri kwa makolo a ana oloŵerera kudziŵa kuti ana awo angathe kusintha! Atamayesetsa, makolo angathe kuthandiza ana awo kuti asiye mankhwalaŵa komanso kuti “akagwire moyo weniweniwo,” umene ukubwera m’dziko latsopano la Mulungu.—1 Timoteo 6:19.
[Zithunzi patsamba 10]
Chifukwa chofuna kudzakhala m’dziko latsopano la Mulungu, anthu ambiri anasiya mankhwalaŵa