Kodi Ndizisankha Motani Matepi a Nyimbo Oti Ndizionera?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndizisankha Motani Matepi a Nyimbo Oti Ndizionera?
“Ndikaona dzina la gulu lokayikitsa la oimba kapena nyimbo yokayikitsa, nthaŵi yomweyo ndimasintha tchanelo chomwe ndikuoneracho.”—Anatero mnyamata wotchedwa Casey.
ACHINYAMATA AMBIRI amaona kuti kuonera matepi a nyimbo n’kosangalatsa kwambiri. Koma m’nkhani ina yotereyi ya mwezi watha tinanena kuti matepi ambiri oonetsa anthu oimba amakhala ndi zinthu zonyansa kwambiri zolaula ndiponso zachiwawa. * Inde, Mkristu sayenera kuonera china chilichonse chimene amasangalala nacho ngati chikulimbikitsa zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Komabe sikuti matepi onse a nyimbo amaonetsa khalidwe loipa ayi. Ena angakhale abwino ndithu. Enanso angaoneke ngati kuti alibe vuto lililonse ayi. Komano amakhala oti munthu akawaonera, angathe kuyamba kuganizira zinthu zina zosemphana ndi Mawu a Mulungu.
Ngati makolo anu amakulolani kuonera matepi a nyimbo, ndi bwino kuti muzisankha ndiponso kukhala ‘ozindikira’ mfundo za m’Baibulo kuti muzitha kuona kuti ichi n’chabwino kapena n’choipa kuonera. (Ahebri 5:14) Kodi mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni pa nkhaniyi n’ziti? Mwina malemba a m’Baibulo ndiponso ndemanga zotsatirazi zingakuthandizeni.
Miyambo 4:23: “Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” Kodi muli ndi chinthu chinachake chomwe mumaona kuti n’chapamtima? N’zosakayikitsa kuti mumayesetsa kwambiri kuchisunga ndi kuchiika pamalo abwino nthaŵi zonse. Simungayerekeze dala kungochisiya pamsewu, ngakhale kwa kanthaŵi kochepa chabe, poopera kuti chingawonongeke kapena kubedwa. Ndithudi, mumachitchinjiriza kwambiri. N’chimodzimodzi ndi zimenezi, muyenera kutsimikiza kuti mutchinjirize mtima wanu, osatayirira ngakhale pang’ono, n’kumaonera zinthu zosayenera.
Aefeso 2:1, 2: “[Mulungu] anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu, zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro [wa mpweya] wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” Mpweya umenewu ndiwo mzimu wa dzikoli, kapena kuti zoganiza za anthu zimene zimawachititsa makhalidwe amene Mulungu amadana nawo. Mzimu woterewu umasonyezedwa m’matepi ambiri a nyimbo ndipo ndi wosemphaniranatu ndi mzimu wa Mulungu womwe umam’chititsa munthu kukhala wachimwemwe, wamtendere, ndi wodziletsa.—Agalatiya 5:22, 23.
2 Timoteo 2:22: “Thaŵa zilakolako za unyamata.” Kuonerera zithunzi zolaula, ngakhale kwa kanthaŵi kochepa chabe, kumangowonjezera chilakolako chofuna kugona ndi mwamuna kapena mkazi. Achinyamata ambiri amavomereza kuti akaona zoterozo saiwala msanga, moti pena amati akakhalakhala amangoona kuti zomwe zija zawabwereranso m’mutu mwawo. Mnyamata wina dzina lake Dave anaonera tepi ina yotenthetsa munthu m’thupi, ndipo anaulula kuti: “Nditangoionera, nthaŵi zonse ndinkangoti ndikamva nyimboyo ndinkangokumbukira zomwe ndinaonazo.” Choncho kuonera matepi otere kungathe kukupangitsani kufuna kuchita zachiwerewere.—1 Akorinto 6:18; Akolose 3:5.
Miyambo 13:20: “Mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” Dzifunseni kuti, ‘Kodi anthu ochita chiwawa, amizimu, zidakwa, kapena ochita zachiwerewere ndingawaitane m’nyumba mwanga?’ Kuonera anthu otere pa TV n’chimodzimodzi n’kuwaitana kudzacheza nawo m’nyumba mwanu. Kodi kuchita zimenezo ‘sikungakupweteketseni’? Kimberly ananena kuti: “Ndaonapo nthaŵi zina atsikana pa phwando atatengera kavalidwe kapena kuvina kokopa amuna komwe amakhala ataonera kumene pa tepi ya nyimbo.” N’kutheka kuti mwina inunso munaonapo zina zotere. Potengera anthu amene sakonda makhalidwe amene Mulungu amafuna, achinyamata ameneŵa amaonetsa kuti ayamba kale ‘kupwetekedwa.’ Ndiye zivute zitani, peŵani “mayanjano [ena alionse] oipa.”—1 Akorinto 15:33.
Salmo 11:5: “Yehova ayesa wolungama mtima: koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” Ngati timaonera matepi a nyimbo amene amangolimbikitsa kuchita zachiwawa, kodi sizingapangitse anthu ena kuona kuti ndife ‘okonda chiwawa’?
Kusankha N’kovuta
Popeza kuti ‘dziko lonse lapansi likugona mwa woipayo,’ kupeza chinachake choti n’kusangalala nacho chomwe sichinaipitsidwe ndi nzeru ndiponso malingaliro a dzikoli kwayamba kuvuta kwambiri. (1 Yohane 5:19) Matchanelo ena a nyimbo amatha kuonetsa nyimbo zambiri zoipa. Ngakhale nyimbozo zitapanda kukhala zoonetseratu zinthu zoipa kapena zachiwawa, nthaŵi zambiri zimalimbikitsabe mzimu wa dzikoli. Katswiri wina woimba ananena kuti tchanelo chinachake chotchuka kwambiri choonetsa nyimbo “chachoka paja pomati ndi tchanelo cha nyimbo n’kufika pokhala ‘tchanelo cholimbikitsa khalidwe linalake.’”
Kuthetsa vutoli kungaoneke ngati n’kophweka: Si nanga n’kungosintha tchanelocho ngati akuonetsapo zinthu zachabechabe? Koma vuto n’lakuti, m’pofunikanso kukhala wosamala ndi matchanelo amene musinthirekowo. Matchanelo ambiri amachita kusonyezeratu zinthu zachiwawa kapena zolaula kwambiri kapenanso kusonyeza anthu akuchita zinthu zamanyazi. Inde tisakane ayi, nthaŵi zina zimagwetsadi ulesi mwinanso kukhumudwitsa kumene, kuti muziti uku mukusangalala ndi zimene mukuonera komanso panthaŵi yomweyo n’kumangokhala muli tcheru kuti musinthe tchanelocho. Ndipo nthaŵi zina zimathekanso kuti mukamasintha tchanelocho, mumakhala mutaona kale zonyansazo. Zithunzi zachabechabe zimakhala zitaloŵa kale m’mutu mwanu. Komabe, dziŵani kuti Yehova Mulungu angakuthandizeni mutamayesetsa kutchinjiriza mtima wanu.—2 Samueli 22:21.
Pali njira zinanso zimene zingakuthandizeni kwambiri. Casey, amene tam’tchula kale uja, anafotokoza zimene iye amaona kuti n’zothandiza kwambiri. Iye anati: “Kaŵirikaŵiri dzina la gulu la oimba ndi mutu wa nyimbo amazionetsa kumayambiriro kwa tepiyo. Gulu lililonse loimba limatchuka ndi zinazake, motero sizivuta kwenikweni kuti mudziŵe magulu oimba kapena nyimbo zimene angathe kuonetsamo zachabechabe. Choncho ndikaona dzina la gulu lokayikitsa la oimba kapena nyimbo yokayikitsa, nthaŵi yomweyo ndimasintha tchanelo chomwe ndikuoneracho. Sindichedwanso ayi!”
‘Kunena Zoonadi Mumtima Mwanu’
Ngakhale mutakhala munthu wodziŵa kwambiri mfundo za m’Baibulo, n’zothekabe kuti mungayambe kulekerera zinthu zachabechabe. Mungatero motani? Pomadzikhululukira mukamaonera zinthu zoipa. (Yakobo 1:22) Baibulo limatiuza kuti bwenzi la Yehova ndiye munthu amene ‘amanena zoonadi mumtima mwake.’ (Salmo 15:2) Ndiyetu muzinena chilungamo mumtima mwanu, musamadzinamize. Mukamaonera zinazake zokayikitsa koma n’kumadzikhululukira, dzifunseni kuti: ‘Kodi Yehova angagwirizane nazo zoti ineyo ndizionera zimenezi?’ Musaiwale kuti nthaŵi zambiri vuto silikhala kungodziŵa chabe zabwino kapena zoipa, koma kutsimikiza kuchitadi zabwinozo! Ubale wanu ndi Yehova muziuona kuti ndi chinthu chofunika kwambiri kuposa zinthu zongosangalatsa.—2 Akorinto 6:17, 18.
Ngati mukufuna kumasankha bwino matepi a nyimbo musamakayikekayike. Ngati mwaganiza zimenezo koma musanatsimikize mtima kwenikweni, zolinga zanuzo zingathe kufera m’mazira. Baibulo limatiuza mmene munthu wa Mulungu, Yobu anatsimikizira mtima kukhalabe wokhulupirika kwa mkazi wake. Iye anati: “Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?” (Yobu 31:1) Mwaonatu! Yobu anachita kulonjeza, kapena kuti kutsimikiza mtima kuti sadzalola kuti maso ake aone zinazake. N’zotheka kuti inunso muchite zomwezo. Tsimikizirani ndi mtima wonse kuti musamaonere zinthu zimene zili zachabechabe. Dziikireni malire oti zikangofika pakutipakuti, basi simuoneranso. Muzipemphera kuti zimenezo zithekedi. Ndiyeno muzichitadi zimene mwanenazo ndipo mukhoza kuchita kuzilemba penapake ngati kulembako kungakuthandizeni. Ngati zonsezi zakanika ndiye mukufuna kuti wina akuthandizeni, bwanji osauza nkhaniyo winawake wachikulire amene mumam’khulupirira, mwina makolo anu?
Poona kuipa kwake, achinyamata ena Achikristu anangoganiza zolekeratu kuonera matepi a nyimbo. Kaya inuyo mungakonde kuchita zotani pa nkhaniyi, chitani zimenezo mukuzindikira zimene mukuchita. Musawononge chikumbumtima chanu. Mukamaonera zinthu zosangalatsa zimene zili zabwino ndiponso zokuiwalitsani nkhaŵa zanu, simungadzigwetse m’mavuto komanso mungakhalabe bwenzi la Yehova.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Ndizionera Matepi a Nyimbo?” yomwe ili mu Galamukani! ya March 8, 2003.
[Chithunzi patsamba 21]
Matepi a nyimbo ena amene sachita kuonetseratu zoipa amalimbikitsabe munthu kuchita zoipa
[Chithunzi patsamba 22]
Tsimikizani ndi mtima wonse kusaonera zinthu zimene Mulungu amadana nazo