“Nyengo ya Malodza”
“Nyengo ya Malodza”
TANGOGANIZIRANI kuti izi zikuchitika. Zigaŵenga zafalitsa mwachinsinsi tizilombo toyambitsa matenda a nthomba m’sitolo zitatu zazikuluzikulu ku United States. Tizilombo timeneti tikuloŵa m’matupi mwa anthu odzagula zinthu amene sakudziŵa n’komwe. Posakhalitsa patangotha mlungu umodzi wokha madokotala akupeza kuti anthu 20 akudwala matendaŵa. Kenaka m’masiku angapo tizilombo toyambitsa matendaŵa tikufalikira kwa anthu enanso. Anthu akugwidwa ndi mantha kwambiri. Ziwawa zangoti mbwee. Odwala akuchuluka kwambiri mwakuti zipatala zikulephera kuwasamalira. Malire a mayiko akutsekedwa. Chuma cha dziko sichikuyendanso bwino. Patangotha masiku 21 kuchokera tsiku limene anafalitsa tizilomboti, matenda afika kale m’maboma 25 ndiponso mayiko ena 10. Apa n’kuti anthu 16,000 atagwidwa ndi matendaŵa ndiponso 1,000 atafa nawo kale. Madokotala akuona kuti ikamatha milungu itatu, odwala matendaŵa adzakwana 300,000. Ndipo munthu m’modzi pa atatu alionse adzafa.
Izitu sizochitika pa filimu yongokokomeza ya zasayansi. Zinali zinthu zimene anaona pa kafukufuku wina wogwiritsira ntchito kompyuta pofuna kudziŵiratu zimene zingadzachitike ngati patabukadi matenda m’njira imeneyi. Kagulu kenakake ka akatswiri otchuka n’kamene kanachita zimenezi m’mwezi wa June chaka cha 2001. Ndipo kafukufuku ameneyu anamutcha kuti “Nyengo ya Malodza.”
Kwa anthu ambiri zoopsa zimene zinachitika pa September 11, 2001 zinawaonetsa “Nyengo ya Malodza” atsopano komanso oopsa zedi. Kuphwasulidwa kwa Likulu la Zamalonda la Padziko Lonse ku New York City ndiponso
nyumba ya Pentagon ku Washington, D.C., kunaonetsa poyera kuti kunja kuno kuli anthu ankhanza zosaneneka amene sagona tulo poganizira zopha anthu ambirimbiri. Ndiponso zinaonetsa kuti dziko la United States komanso ngakhale dziko lina lililonse, lingathe kuona zoopsa zotere. Masiku athu ano zigaŵenga zouma mtima zingathe kupha anthu miyandamiyanda m’kanthaŵi kochepa chabe.Zoopsa za pa September 11 zitangochitika, anthu andale a ku United States ndiponso anthu ogwira ntchito zofalitsa nkhani analandira makalata amene anali ndi tizilombo toopsa toyambitsa matenda a anthrax. Zimenezi zinachititsa anthu mantha kwambiri. Chimene chikuwonjezera mantha ameneŵa n’chakuti ofalitsa nkhani komanso akatswiri ena anati zigaŵenga zingadzathe kugwiritsira ntchito tizilombo toopsa kuposa ta anthrax, monga ta mliri woopsa wofalitsidwa ndi makoswe kapenanso ta matenda a nthomba. Mwina mayiko enaake osapanganika anali atayamba kale kuŵeta tizilombo totere m’malo achibisira opangirako mankhwala. Taonani zina mwa zinthu zimene zalembedwa posachedwapa pankhaniyi:
Bungwe la American Medical Association linati: “Bungwe la zamankhwala padziko lonse la World Medical Association likudziŵa kuti zida zofalitsa tizilombo topereka matenda zingathe kugwiritsidwa ntchito kuyambitsa miliri yoopsa imene ingathe kufala padziko lonse. Tsoka limeneli lingathe kugwera dziko lililonse. Kufalitsa tizilombo monga toyambitsa nthomba, mliri wofalitsidwa ndi makoswe, ndiponso anthrax kungadwalitse ndiponso kupha anthu osaneneka makamakanso chifukwa cha mantha amene miliriyi ingayambitse.”
Magazini yotchedwa Scientific American inati: “Zida zofalitsa tizilombo topereka matenda n’zosiyana ndi mabomba ndiponso gasi wakupha chifukwa zimapha mwakabisira pakuti matenda ake amangobisala m’thupimu n’kumakula pang’onopang’ono munthuwe usakudziŵa. Poyamba kuchipatala kumangofika anthu ochepa chabe odwala matendawo. Madokotala n’kutheka kuti sangathe kumvetsa bwinobwino vuto lawo kapenanso vuto lawolo lingakhale lofanana ndi matenda enaake ofala. Ndiye azachipatala akamadzadziŵa zimene zikuchitika, matendawo angakhale atafala kale m’mizinda yathunthu.”
Magazini ya Foreign Affairs inati: “Ngati tizilombo toyambitsa matenda a nthomba atatifalitsa panopa, anthu ambiri padziko pano sangathe kudziteteza kumatendaŵa, ndipo pakuti munthu m’modzi pa anthu atatu alionse amene amagwidwa ndi matendaŵa amafa, anthu pafupifupi mabiliyoni aŵiri angathe kufa.”
‘Dziko lililonse lingathe kukhala patsoka. Matendaŵa angafalikire m’mizinda yathunthu. Anthu mabiliyoni aŵiri angathe kufa.’ Izitu n’zoopsa. Komano kodi n’kutheka kuti zigaŵenga zingadzafalitsedi tizilombo todwalitsa? Akatswiri akuganizira funso limeneli mozama. Nkhani yotsatirayi ikuthandizani kumvetsa mfundo zina zokhudza nkhaniyi.
[Chithunzi patsamba 24]
Asilikali akuyeserera zimene angadzachite ngati zigaŵenga zitadzafalitsa tizilombo todwalitsa
[Mawu a Chithunzi]
DoD photo by Cpl. Branden P. O’Brien, U.S. Marine Corps