Kugwiritsa Ntchito Galamukani! Mwanjira Yabwino
Kugwiritsa Ntchito Galamukani! Mwanjira Yabwino
ALI ndi zaka 16, mtsikana wina wa ku United States, dzina lake Vanessa, yemwe ali m’gulu la Mboni za Yehova, anauzidwa kuti alembe lipoti la kusukulu lokhudza matenda enaake om’lepheretsa munthu kukonda zakudya. Iye anati: “Ndinafufuza m’mabuku osiyanasiyana, koma ndinangopezamo nkhani zochepa chabe. Ndinawauza makolo anga za nkhani imeneyi, ndipo iwo anandiuza kuti ndiifufuze m’mabuku athu.”
Atafufuza m’mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, Vanessa anapeza zinthu zambiri zoti alembe m’lipoti lakelo. Iye anati: “Komatu imeneyi inali mbali yochepa chabe ya ntchito imene anatipatsayo. Nditatha zonsezi, ndinafunikanso kuti ndikakambe zimene ndinapeza pamaso pa aphunzitsi athu ndi ophunzira anzanga okwana 20!” Kodi Vanessayo anatha bwanji kuchita chintchito chovutachi?
Monga mmene amachitira a Mboni za Yehova padziko lonse, Vanessa amaphunzira kulankhula pagulu m’Sukulu ya Utumiki wa Teokalase imene imachitikira pa Nyumba ya Ufumu ya kufupi ndi kwawo. Vanessayo anati: “Chifukwa cha sukulu imeneyi timakhala okonzeka mokwanira kupita kukatumikira ndiponso kukalankhula ndi anthu ena. Amatilangizanso zimene tiyenera kuchita kuti anthu amve bwinobwino zimene tikuwauza.” Ndiye kodi Vanessa anakhoza bwanji pa mayeso atachita khama chonchi? Iye anati: “Ndinapambana kuposa ena onse.”
Vanessa ali m’gulu la achinyamata ambiri amene akugwiritsa ntchito bwino kwambiri mabuku ozikidwa pa Baibulo ndiponso maphunziro ena auzimu. Tiyenera kuwayamikira kwambiri achinyamata otereŵa chifukwa chakuti akumvera mawu olimbikitsa a pa Mlaliki 12:1, amene amati: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.”