Amasai—Anthu Odabwitsa Ndiponso Ochititsa Kaso
Amasai—Anthu Odabwitsa Ndiponso Ochititsa Kaso
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU KENYA
NYIMBO imene kamwana kamtundu wa Amasai (Maasai) kankaimba mokweza kwambiri inkangomveka m’chidikha chonsecho chifukwa cha kuomba kwa mphepo yozizira ya m’chisisira cha m’maŵa. Dzuŵa limati likamakwera, nakonso kamwanaka kanali kuimba mokweza kwambiri ndi mawu ake okoma, n’kumangokhala ngati kambalame kaja kamalira mokweza dzuŵa likamatuluka kumene.
Ndinamvetsera, ndipo kuwala kwa dzuŵa kunandithandiza kuona kamnyamata koŵeta ng’ombeka kali chilili pakati pa ng’ombe za abambo ake. Katadzikulunga ndi nsalu yofiira imene sinaphimbe thupi lake lonse, kamnyamataka kanangoima njoo ndi mwendo umodzi ngati chidokowe, kwinaku katatsamira mkondo wake komanso kakuimbira nyimbo ziŵeto zake zimene zinali kudya mtima uli m’malo. Taimani ndikuuzeni zina za anthu odabwitsaŵa.
Takulandirani Kuno Kudera la Amasai
Amasai, ndi mtundu wa anthu okonda ziŵeto mochititsa kaso kwambiri, ndipo amakhala m’dera lalikulu kwambiri m’chigwa cha ku East Africa cha Great Rift Valley. Anthuŵa amapezeka m’mayiko a Kenya ndi Tanzania, ndipo ndi mtundu wotsala wa Amasai omwe analipo kalekalelo. Iwo amangokhala monga mmene ankakhalira azigogo awo kalelo. Iwo nthaŵi alibe nayo ntchito, chawo chimangokhala kuona kutuluka ndi kuloŵa kwa dzuŵa ndiponso kusintha kwanyengo basi.
Amasai ali ndi maluso osiyanasiyana ndipo limodzi mwa malusoŵa ndilakuti amatha kukhala bwinobwino m’malo oopsa komanso amiyalamiyala a m’chigwachi. Chifukwa chakuti amayenda mwachifatse koma akuponya mwendo patali, iwo amayenda mtunda wautali kwambiri pofufuza malo odyetsa ndiponso kumwetsa ng’ombe zawo. Amayang’anira ng’ombe zawo pakati pa nyama zakutchire monga mbidzi, akadyamsonga ndiponso nyama zina zokhala m’chigwa zimene zimakhalanso komwe iwo amakhala.
Ndi Anthu Okonda Ng’ombe Kwambiri
Amasai amakhulupirira kuti ng’ombe zonse padzikoli n’zawo. Iwo amakhulupirira chonchi chifukwa cha nthano yakalekale imene imati pachiyambi Mulungu anali ndi ana atatu ndipo mwana aliyense anam’patsa mphatso. Mwana woyamba analandira muvi woti azisakira zinyama, wachiŵiri analandira khasu loti azilimira ndipo wachitatu analandira chikwapu chokusira ng’ombe. Ndipo mwana wachitatuyu, ndiye amene amati anakhala kholo la mtundu wa
Amasai. Ngakhale kuti mitundu ina ilinso ndi ng’ombe, Amasai amakhulupirira kuti eni ake enieni a ng’ombezi ndi iwowo basi.M’chikhalidwe cha Amasai, munthu amatchuka n’kukhala wofunika kwambiri malingana ndi ng’ombe ndiponso ana amene ali nawo. Ndithudi, iwo amaona kuti munthu amene ali ndi ng’ombe zosapitirira 50 ndi wosauka. Mothandizidwa ndi ana ndiponso akazi ake ambiri, mwamuna wa chimasai amatha kupeza ng’ombe zochuluka kwambiri zimene zingafike mpaka sauzande.
M’banja lachimasai amakondana nazo kwambiri ng’ombe zawo. Aliyense wa m’banjalo amadziŵa bwinobwino kulira kwa ng’ombe iliyonse komanso zochitika zake. Nthaŵi zambiri ng’ombezi amazilembalemba mizere yaitali yoyenda mozungulira ndiponso amazilemba mizere ina yopanga maluŵa ojambulidwa mwaluso zedi n’cholinga chakuti ng’ombezo zizioneka mokongola. Amaimba nyimbo zimene zimafotokoza kukongola kwa ng’ombe zina ndiponso mmene amazikondera. Nkhunzi za nyanga zikuluzikulu zopotana amazinyadira kwambiri, ndipo thole amalisamala ndi kuliyang’anira kwambiri ngati kuti ndi khanda lobadwa kumene.
Mwachikhalidwe cha Amasai, azimayi ndi amene amamanga nyumba ndipo amazimanga ndi nthambi za mitengo pamodzi ndi udzu kenaka n’kuziphoma ndi ndowe za ng’ombe. Nyumbazi amazimanga mkati mwa chimpanda chachikulu chozungulira chimene muli khola logona ng’ombezo kukada, ndipo nyumba zimenezi zimaoneka mozungulira ngati dzira. Malo onsewo amawaikira mpanda wa minga zikuluzikulu potchingira afisi, akambuku ndiponso mikango yolusa kuti zisawagwire kapena kugwira ng’ombe zawo.
Moyo wa Amasai umadalira thanzi ndiponso mphamvu za ng’ombe zawo. Iwo amamwa mkaka wa ng’ombezo, ndipo ndowe zake amaphomera ndi kuzirira nyumba zawo. Kaŵirikaŵiri anthuŵa sapha ng’ombe zawo kuti apeze ndiwo; koma amaŵeta nkhosa ndi mbuzi pang’ono zoti azidya. Koma akapha ng’ombe imodzi, amagwiritsa ntchito chiwalo china chilichonse cha ng’ombeyo. Nyanga zake amazigwiritsa ntchito monga moikamo zinthu; mapazi ndiponso mafupa ake amapangira zinthu zokongoletsera; ndipo zikopa zake amapangira nsapato, amavala, amagonera ndiponso amapangira zingwe.
Ndi Ochititsa Kaso Ndiponso Odabwitsa
Amasai ndi anthu aataliatali ndiponso ochepa thupi ooneka mokongola. Zovala zawo n’zokongola kwambiri. Amadzikulunga thupi lawo lofeŵa mokhwepa ndi nsalu yokongola yooneka mwina mofiira mwina mobiriŵira. Kaŵirikaŵiri azimayi amavala m’khosi mwawo mikanda ikuluikulu yozungulira ngati mbale ndiponso amamanga timalamba tamitundumitundu m’mutu mwawo. Nthaŵi zina amavala makoza ofufuma amkuwa ali othina m’manja
ndi mu akakolo. Nthaŵi zambiri akazi ndi amuna omwe amachititsa kuti makutu awo akhale alendelende povala ndolo zolemera ndiponso zinthu zina zowakongoletsa zokhala ndi mikanda. Amatenga dothi linalake lofiirira n’kulipera kwambiri kusanduka laufaufa n’kusakaniza ndi mafuta a ng’ombe, ndipo mwaluso amadzola zimenezo.Tsiku lina usiku, moto ukuwala ndinkayang’ana gulu la anthu a chimasai atasonkhana pamodzi kuti azivina. Ataima mozungulira, iwo anayamba kuvina mogwirizana. Kuvinako kutafika pa mponda chimera, mikanda ya atsikana yam’khosi yolemerayo inkagundana m’mapewa awo mogwirizana bwino podzutsa ndi kuŵeramitsa mitu yawo. Kenaka, Amasai odziŵa kumenya nkhondo achimuna ankapatsana mpata woloŵa mmodzimmodzi pakati pagululo, ndipo ankadumphadumpha mochititsa chidwi kwambiri, kenakanso ankadumphira m’mwamba kwambiri. Amatha kuvina mpaka kuda bii, kenaka n’kuleka onse atatoperatu.
Mabanja a Amasai
Kunatentha tsiku lonselo mpaka madzulo, ndipo ndinakhala ndi gulu la azimayi achimasai pansi pamtengo wa kesha n’kumangowaonerera akusokerera mikanda mwaluso pa zikopa zoyanikidwa. Chifukwa chotanganidwa ndi kuseka ndiponso kulankhulana, iwo sankamva n’komwe kusokosera kwa mbalame zimene zinali pamutu pawo, zomwe zinkamanga zisa zawo ndi udzu wouma. Dzuŵa likamakwera, azimayi amatanganidwa ndi kutunga madzi ndiponso kutola nkhuni, kukonzakonza nyumba, ndiponso kusamala ana awo aang’onoang’ono.
Dzuŵa likapepa, azibusa amayamba kubwerera ndi ng’ombe zawo. Pang’onopang’ono gulu la ng’ombelo limayang’ana msana wa njira ulendo wa kunyumba. Ng’ombezo zikamayenda, chifumbi cha katondo chimangoti koboo n’kumaoneka kuwala chifukwa cha kuloŵa kwa dzuŵalo. Azimayiwo akachionera patali chifumbichi, amasiya msangamsanga ntchito yawo pokonzekera kufika kwa ng’ombezo.
Ndiye zikaloŵa mkati mwa khola limene limakhala lotetezeka bwino, azibambowo amaziyendera ng’ombe
zawozo, n’kumasisita nyanga za nkhunzi pogoma ndi kukongola kwake. Kamnyamata kakukama ng’ombe n’kutcherezera mkakawo mkamwa mwake ndipo nthaŵi yomweyo amayi ake akukakalipira kwambiri. Atsikana amaloŵerera n’kumatulukanso m’chipiringu cha ng’ombezo, akukama mkaka mogometsa n’kumaudzazitsa m’zipanda zitalizitali mpaka kusefukira.Usiku tinaunjikana tonse kuzungulira moto umene unachititsa kuti malo onsewo akhale ofunda bwino. Cha kufupi ndi komwe kuli ng’ombezo kukumveka fungo la utsi ndiponso kununkhira kwa nyama yowotcha komanso fungo lochokera ku khola la ng’ombe zomwe zinali pafupi pomwepo. Bambo wina wachikulire wangokhala ndipo akusimba tinkhani ta mbiri ya Amasai ndiponso kupambana kwa Amasai pa nkhondo. Akumaima kaye akamva kulira kwa mkango chapatali, ndipo kenaka n’kupitiriza kulakatula mwatsatanetsatane nkhani yake imene ikuwasangalatsa anthu amene akuimverawo. Pamapeto pake anthuwo akuyamba kuchoka mmodzimmodzi ndipo mpaka onse akupita kukagona m’nyumba zawo zozungulira zadothi. Usiku wonse wangoti zii chifukwa cha mdima wa ndiwe yani ndiponso poti n’kutchire la kutali kwambiri, ndipo chomwe chikungomveka n’kupuma kwa ng’ombe zomwe zagona basi.
Ubwana wa Amasai
Anthuŵa amachita zinthu zosiyanasiyana dzuŵa likatuluka. Ana aang’onoang’ono amaseŵera pamphepo ya mmaŵa atangovala mikanda m’chiuno ndiponso m’khosi mwawo. Makolo awo amawakonda kwambiri ndipo tsogolo ngakhale moyo wawo weniweniwo umadalira anawo. Choncho anawo akamakondwa kumtima kwa makolowo kumangokhala kwa mbee.
Ana saleredwa ndi makolo awo okha, koma munthu aliyense wachikulire pamudzipo angathe kudzudzula ndiponso kulanga mwana wina aliyense wosamvera. Ana amawaphunzitsa kulemekeza akuluakulu, ndipo amaphunzira msangamsanga mmene zinthu zimafunika kukhalira m’banja la Amasai. Akakhala aang’onoang’ono amangochita zimene akufuna, koma akayamba kukula, atsikana amayamba kuwaphunzitsa kugwira ntchito zapakhomo ndipo anyamata amawaphunzitsa kusamala ndiponso kuyang’anira ziŵeto. Makolo amawauza ana awo kuti adziŵe mankhwala a zitsamba ndiponso amawaphunzitsa za miyambo ndi chikhalidwe chonse cha Amasai.
Kuyamba Kukula
Achinyamata akayamba kukula amaphunzira miyambo ndiponso chikhalidwe chosonyeza kuti akukula. Miyambo ina imene amaphunzira n’njokhudza matenda, malodza, banja ndiponso maliro. Amasai amakhulupirira kuti munthu akalephera kutsatira miyambo imeneyi akhoza kuona malodza.
Makolo a chimasai amatha kulinganiza kuti mwana wawo wamkazi adzakwatiwe ndi winawake iye adakali wakhanda. Mwamuna amene ali ndi ng’ombe zokwanira kulipira malowolo amene bambo a mtsikanayo akufuna ndiye amene amamulonjeza kuti adzakwatira mtsikanayo. Nthaŵi zambiri mtsikana amakwatiwa ndi mwamuna wamkulu kwambiri poyerekezera ndi iyeyo ndipo amakakhala pa mitala.
Anyamata akamakula m’gulu la Amasai, amaseŵerera limodzi ndi anyamata ena amisinkhu yawo. Kugwirizana ndi anzawo kumeneku kumatha kukhala moyo wawo wonse. Amakula limodzi kuyambira ali anyamata wamba mpaka kufika pokhala ankhondo. Monga ankhondo amagwira ntchito yoteteza malo awo, kuyang’anira malo amene amapeza madzi kuti akhale abwino ndiponso amateteza ziŵeto zawo kuzilombo zolusa ndiponso kuti anthu asazibe. Pokhala otchuka chifukwa cha kupanda kwawo mantha ndiponso kulimba mtima kwawo, anthu sanawaonepo Amasai akuyenda opanda mikondo yawo yakuthwa mochita kuti waliwali.
Ankhondoŵa akafika zaka za m’ma 30, ndiye kuti amakhala atafikapo pokhala munthu wamkulu. Ndi chimwemwe chodzala tsaya ndiponso pochitira phwando, amalandiridwa m’gulu la akuluakulu ndipo amaloledwa kukwatira tsopano. Akafika pamenepa, amangolimbana ndi zotenga mkazi n’kumawonjezera ng’ombe zawo ndipo amakhalanso ndi udindo wolangiza ena ndiponso kuthetsa mikangano.
Kodi Tsogolo la Amasai N’lotani?
Masiku ano miyambo ndiponso chikhalidwe chochititsa chidwi cha Amasai chikutha mofulumira. M’madera ena Amasai sakuyendayendanso mwaufulu ndi ng’ombe zawo kuti afufuze malo ena odyetsera ziŵeto zawo. Madera aakulu amene anali malo awo okhala akusandutsidwa nkhalango zosungirako zinyama zakutchire kapena akumangako nyumba ndiponso malo aulimi n’cholinga chothandiza anthu amene akungochulukabe. Chilala ndiponso mavuto a zachuma akupangitsa kuti Amasai ambiri akakamizike kugulitsa ng’ombe zawo zimene amazikonda kuti akhale ndi moyo. Akamasamukira kumizinda ikuluikulu, nawonso akukumana ndi mavuto amene amavutitsa anthu ena onse amasiku ano amene ali nawo pafupi.
Masiku ano Mboni za Yehova zikufika kumidzi ya Amasai ku East Africa. Mabulosha opitirira 6000 akuti Sangalalani ndi Moyo Padziko Lapansi Kosatha! asindikizidwa m’chilankhulo cha chimasai. Motero Amasai akuthandizidwa kuona kusiyana kwa zikhulupiriro zopanda pake ndi choonadi cha m’Baibulo. Indedi, n’zonyaditsa kwambiri kuona kuti Mlengi wathu, Yehova Mulungu, wapereka mpata wakuti anthu odabwitsa ndiponso ochititsa kasoŵa akhale m’gulu la anthu ambiri ochokera mwa “mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe” amene adzapulumuke chiwonongeko cha dziko losokonekera lino.—Chivumbulutso 7:9.
[Chithunzi patsamba 17]
Mudzi wa Amasai
[Chithunzi patsamba 18]
Amasai aunjikana pamodzi kuti avine
[Chithunzi patsamba 18]
Mboni ziŵiri za chimasai