Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuŵerengera Ana Anu Mokweza Mawu?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuŵerengera Ana Anu Mokweza Mawu?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuŵerengera Ana Anu Mokweza Mawu?

“Anandipeza, ndipo anakwera pa miyendo panga kwinaku akukoka buku limene masamba ake anali opindika m’makona komanso opakika . . . chiponde ndipo anapempha kuti, ‘Ababa, ndiŵerengereniko bukuli; chonde ndiŵerengereniko.’”—Pulofesa wa maphunziro wotchedwa Dr. Clifford Schimmels anatero.

ANA amaphunzira zinthu mofulumira kwambiri. Ofufuza amati ubongo wa ana osakwana zaka zitatu umafulumira kwambiri kukula. Zimene makolo amachita tsiku lililonse monga kuŵerenga, kuimba ndiponso kumam’konda mwana wawo zingathandize kwambiri kuti mwanayo akule bwino. Komabe malingana ndi zimene ananena ofufuza ena, akuti pafupifupi theka lokha la makolo a ana a zaka ziŵiri mpaka zisanu ndi zitatu ndiwo amaŵerengera ana awo tsiku lililonse. Mungafunse kuti, ‘Kodi kumuŵerengera mwana wanga n’kothandizadi?’

Kum’pangitsa Kukonda Kuŵerenga

Akatswiri amati yankho la funso limeneli n’lakuti; inde, n’kothandizadi. Buku lolimbikitsa kuŵerenga lakuti Becoming a Nation of Readers limati, “Chinthu chimene chingathandize kwambiri munthu kuti adzakhale wodziŵa bwino kuŵerenga ndicho kumuŵerengera adakali mwana. Zimenezi zingatheke makamaka mwana akakhala pamsinkhu wopita kusukulu yamkaka.”

Ana akamamvetsera nkhani zimene zikuŵerengedwa m’buku, amaphunzira adakali aang’ono kuti zilembo zimene zili patsambapo zimagwirizana ndi mmene timalankhulira. Iwo amazoloŵeranso kumva mmene amalongosolera nkhani m’mabuku. Buku lina lokhudza za kuŵerenga mokweza mawu limati, “Nthaŵi ina iliyonse imene tikumuŵerengera mwana, ndiye kuti tikutumiza ku ubongo wake uthenga ‘wosangalatsa.’ Tinganenenso kuti ndi uthenga wothandiza mwana kuona kuti mabuku ndiponso nkhani zolembedwa n’zosangalatsa.” Makolo amene amalimbikitsa ana awo kukonda mabuku angawalimbikitse anawo kukhala ndi chilakolako chachikulu chofuna kukhala anthu okonda kuŵerenga m’moyo wawo wonse.

Kuwathandiza Kumvetsa Zinthu Zosiyanasiyana

Makolo amene amaŵerengera ana awo mokweza mawu angawapatse mphatso yapamwamba zedi, mphatso ya kudziŵa anthu, malo ndiponso zinthu zina. Pogwiritsa ntchito ndalama zochepa kwambiri, iwo angathe “kuyendera” dziko lonse poŵerenga m’mabuku. Taonani chitsanzo cha Anthony, mwana wa zaka ziŵiri, amene amayi ake anayamba kumuŵerengera atangobadwa. Amayi akewo anati: “Ulendo wake woyamba wa ku malo osungirako zinyama unali ngati ulendo wachiŵiri.” Unakhala bwanji ulendo wachiŵiri? Inde, ngakhale kuti kanali koyamba kuti Anthony aone mbidzi, mikango, akadyamsonga ndiponso nyama zina pamasom’pamaso, iye anali atazidziŵa kale nyamazi.

Amayi ake anapitiriza kunena kuti: “Pamene Anthony anali ndi zaka ziŵiri zokha, anali atadziŵa kale anthu ambiri, zinyama zambiri, komanso zinthu zosiyanasiyana, ndipo zonsezi anazidziŵira m’mabuku.” Inde, kuŵerengera ana mokweza mawu adakali aang’ono kungathandize kwambiri kuti amvetse zinthu zosiyanasiyana.

Kuwathandiza Kuti Azikondana Nanu Kwambiri

Ana savuta kuphunzira zinthu adakali aang’ono ndipo amayamba kuphunzira zinthu zimene zimadzaonekera pa zochita zawo za m’tsogolo. Choncho makolo amafunika kuyambiratu kuwathandiza kuti azidzakondana nawo kwambiri, kukhulupirirana, kulemekezana ndiponso kumvetsetsana. Kuŵerenga kungathandize kwambiri pa ntchito imeneyi.

Makolo akakhala ndi nthaŵi yoyangata ana awo n’kumawaŵerengera, anawo amadziŵa kuti amakondedwa. Mayi wina wa ku Canada dzina lake Phoebe ananena mawu aŵa okhudza za kuŵerengera mwana wake wamwamuna yemwe tsopano ali ndi zaka 8: “Ine ndi mwamuna wanga timaona kuti kuchita zimenezi kwathandiza kwambiri kuti Nathan azitikonda kwambiri. Iye amakhala womasuka nafe ndipo amatiuza zimene akuganiza. Zatithandiza kukhala okondana kwambiri.”

Cindy anangozoloŵera kumuŵerengera mokweza mwana wake wamkazi kuyambira ali ndi chaka chimodzi akuphunzira kukhala tsonga n’kumamvetsera kwa kanthaŵi kochepa chabe. Kodi khama lakelo pochita zimenezo linathandiza? Cindy anati: “Chimene chimam’pangitsa Abigail kuti azikhala womasuka kutiuza zimene zinachitika kusukulu kapena ngati mnzake anam’vutitsa ndicho kugwirizana ndiponso bata limene limakhalapo tikamaŵerengera limodzi. Kodi lilipo kholo limene silingakonde kuti mwana wawo akhale wotere?” Kunena zoona, kuŵerenga mokweza mawu kungathandize kuti pakhale mgwirizano weniweni pakati pa makolo ndi mwana wawo.

Kuwaphunzitsa Maluso Ofunika Kwambiri M’moyo

Buku lolongosola za banja lotchedwa 3 Steps to a Strong Family limati, “Masiku ano ana athu amadzazitsa maganizo awo ndi zinthu zambiri zopanda pake zimene amaona pa TV ndiponso malo ena ndi ena, mwakuti kusiyana ndi m’mbuyomu, iwo akufunika kuwakonza maganizo, kuwathandiza kuti aziganiza mozama, kuti akhale ndi nzeru, kuti azikhazikika maganizo n’kumachita zinthu zimene zili zofunikadi kwa iwo ndiponso kuti aziona zinthu zowachitikira m’moyo wawo m’njira yoyenera.” Makolo ndiwo ali oyenereradi kuwathandiza anaŵa kuti akule ndi maganizo abwino.

Mwana akazoloŵera kuŵerenga ziganizo zazitali ndiponso zolembedwa bwino m’buku zingam’thandize kwambiri kuphunzira kulankhula ndiponso kulemba momasuka. Dorothy Butler yemwe analemba buku lolimbikitsa kuŵerengera ana lakuti Babies Need Books, ananena kuti: “Kaganizidwe ka munthu kamadalira mmene munthuyo amadziŵira chinenero chake. Ndithudi, kudziŵa zinthu ndiponso kukhala ndi nzeru kumadalira chinenero.” Kutha kulankhulana bwinobwino ndi anthu ndiko chinthu chofunika kwambiri kuti munthu azigwirizana ndi ena.

Kuŵerenga mabuku oyenera kungawonjezerenso makhalidwe abwino. Makolo amene amaŵerenga ndiponso kukambirana ndi ana awo angawathandize kuphunzira maluso othetsera mavuto. Pamene Cindy anali kumuŵerengera nkhani mwana wake wamkazi Abigail, iye anali kuonetsetsa mwachidwi mmene nkhanizo zinkam’khudzira. “Pakuti ndife makolo ake, tingathe kudziŵa makhalidwe ake ena ovuta kuwatulukira ndipo mwinanso tingam’thandize kupeŵa kuganiza moipa adakali mwana wamng’ono.” Ndithudi, kuwaŵerengera ana mokweza mawu kungawathandize kuti akhale ndi maganizo ndiponso mtima wabwino.

Kuti Kuŵerenga Kukhale Kosangalatsa

Poŵerenga, “khalani womasuka,” kuti mukhale ngati mukungocheza kuchitira kuti mwanayo azisangalala nazo. Makolo odziŵa bwino ana awo amadziŵa polekera kuŵerenga. Lena anati: “Nthaŵi zina Andrew, yemwe ali ndi zaka ziŵiri amakhala atatopa kwambiri ndipo satha kukhala tsonga kwa nthaŵi yaitali. Timalekera panjira ndime zathu zoŵerenga kuti amve nawo asanayambe kuvutika n’kukhala. Sitifuna kuti Andrew adane n’kuŵerenga, choncho sitimuumiriza ngati watopa.”

Kuŵerenga mokweza mawu sikuti n’kumangotchula chabe mawu olembedwa papepala. Muyenera kudziŵa nthaŵi yovundukulira tsamba lotsatira mukamaŵerenga buku la zithunzi kuti mwanayo achite chidwi poganizira za mmene nkhaniyo iyendere. Ŵerengani mwamyaa. Kusintha mawu ndiponso kuŵerenga motsindika pamene pali poyenera kungapangitsenso nkhaniyo kukhala yosangalatsa. Mukamaŵerenga mokhazikika maganizo mungam’chititse mwana wanu kukhala munthu wosatutumuka ndi zinthu.

Mwana wanu amapindula kwambiri ngati nayenso akulankhulapo. Pakatenga kanthaŵi, muziima kaye n’kufunsa mafunso oti afotokoze. Muziwonjezera zimene mwana wanu wayankha pomuuzanso mayankho ena.

Muzisankha Mabuku Abwino

Komabe, mwina chinthu chofunika kwambiri n’kusankha mabuku abwino. Kuchita zimenezi kumafunika kufufuziratu. Sankhani mabuku mosamala kwambiri ndipo gwiritsani ntchito mabuku okhawo amene ali othandiza kapena ophunzitsa zinthu ndiponso makhalidwe abwino. Yang’anani bwinobwino chikuto, zinthuzi ndiponso kalembedwe kake. Sankhani mabuku osangalatsa inuyo kholo ndi mwana wanu yemwe. Nthaŵi zambiri ana amapempha kuti muwaŵerengere nkhani yomweyo kangapo.

Makolo padziko lonse amaona kuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo * n’lothandiza kwambiri. Bukuli linapangidwa kuti makolo aziliŵerenga pamodzi ndi ana awo aang’ono, ndipo lingathandize anawo kuti adzakhale odziŵa kuŵerenga bwino ndiponso limawapangitsa kuti azichita chidwi ndi Baibulo.

Makolo amene amawaŵerengera ana awo mokweza mawu angawathandize anawo kuti azoloŵere kuŵerenga bwino, ndipo mapeto ake zimenezi zingadzawathandize m’moyo wawo wonse. Ponena za mwana wake wamkazi, JoAnne anati: “Jennifer anayamba kukonda kuŵerenga, ndipo anaphunzira kuŵerengako ndi kulemba asanayambe sukulu. Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti zimenezi zinam’pangitsa kuyamba kukonda Mlengi Wamkulu, Yehova. Jennifer anaphunzira kudalira Baibulo limene lili Mawu ake olembedwa kuti azim’tsogolera pa zochita zake zonse.” Kunena zoona, zinthu zimene mumam’thandiza mwana kuzikonda n’zofunika kwambiri kuposa zimene mumam’thandiza kuziphunzira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 24 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 30]

Poŵerengera Mwana Wanu

• Yambani adakali khanda.

• Ŵerengani pamene mwanayo sakuvutavuta.

• Ŵerengani nkhani zimene nonse mumazikonda.

• Ŵerengani mobwerezabwereza ngati n’kotheka ndipo muziŵerenga mogwira mtima.

• Muzimufunsa mafunso mwana wanu kuti nayenso azilankhulapo.

[Mawu a Chithunzi patsamba 29]

Chithunzi chojambulidwa ku malo osungirako zinyama a bungwe la Wildlife Conservation Society m’tauni ya Bronx