Kodi Angandiyankhe Ndani?
Kodi Angandiyankhe Ndani?
Anthu ambiri masiku ano amafunsa funso limeneli. Mphunzitsi wina mumzinda wa Novosibirsk, m’dziko la Russia anatchulapo kuti n’kovuta kupeza mayankho a mafunso okhudza Mulungu ndiponso chipembedzo omwe ana ake a kusukulu amafunsa. Iye analongosola motere m’kalata imene analemba:
“Tsiku lina nditafika kunyumba, ndinapeza kuti munthu wina wasiyako kathirakiti ka mutu wakuti ‘Chifukwa Chake Mungadalire Baibulo.’ Ineyo ndimaphunzitsa mbiri yakale, ndipo nthaŵi zambiri ana amene ndimawaphunzitsa ndimakambirana nawo nkhani za zipembedzo, Baibulo, ndiponso za Mulungu. Nthaŵi zina mafunso amene anaŵa amafunsa amavuta kwambiri kuyankha.
“M’mbuyomu, ndinkaganiza kuti anthu amangoganiza za Mulungu akakhala pa mavuto basi. Koma tsopano ndikukhulupirira kuti sizili choncho ayi chifukwa chakuti munthu akakhala phee amadzifunsanso kuti: ‘N’chifukwa chiyani zimenezi zinandichitikira ineyo? Kodi ndine chiyani makamaka? Kodi ndinachokera kuti? Kodi ndikadzafa ndidzapita kuti?’ Ndibwino kwambiri kupeza mayankho a mafunsoŵa. Zikuoneka ngati kuti Baibulo limatchula mfundo zokhutiritsa kwambiri.”
Mphunzitsiyo anamaliza kalatayo ndi mawu akuti: “Ndalemba kalatayi chifukwa chakuti ndikufuna ndilidziŵe bwino Baibulo ndiponso Mulungu.”
Mboni za Yehova zimauza anthu kuti m’Baibulo ndimo muli mayankho a mafunso awo. Mungagwiritse ntchito buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. M’bukuli muli mitu 19 ndipo ina n’njakuti: “Kodi Mulungu Woona Ndani?,” “Kodi N’chifukwa Ninji Timakalamba ndi Kufa?,” ndiponso “Kodi Mulungu Waloleranji Kuvutika?” Mungathe kuitanitsa buku lothandiza kuphunzira Baibulo limeneli, lomwe lili ndi masamba 192, polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.
□ Nditumizireni buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.