Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Gwiritsani Ntchito Mankhwala Mwanzeru

Gwiritsani Ntchito Mankhwala Mwanzeru

Gwiritsani Ntchito Mankhwala Mwanzeru

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA

DOKOTALA wanu akakulemberani mankhwala, mosakayikira iye amakhala akufuna kuti muchire, ndipo amakulemberani mankhwalawo mogwirizana ndi matenda amene wapeza, mmene iyeyo amadziŵira mankhwala, ndiponso mmene amadziŵira ntchito yake. Komabe, wodwalayo sayenera kuganiza kuti dokotalayo ndiye ali ndi udindo wonse woonetsetsa kuti iyeyo achire. Wodwalayo ndiye ali ndi udindo pa mankhwala alionse amene akumwa.

Mukamamwa mankhwala amene dokotala wakulemberani, ganizirani malangizo aŵa amene dokotala wina anapereka:

● Mankhwala alionse amabweretsanso vuto linalake munthu akawamwa. Muli ndi ufulu wodziŵa mankhwala amene mukumwa ndiponso kuti kodi mankhwalawo angabweretse mavuto otani. Ngati dokotala sanakuuzeni zimenezi musaope kumufunsa. Nthaŵi zambiri mankhwala amachiritsa ndipo sabweretsa mavuto oposa matendawo. Koma kuti musankhe zinthu mwanzeru muyenera kuzidziŵa bwino.

● Mankhwala amakhudza anthu m’njira zosiyanasiyana. Dokotala sangadziŵe ndendende kuti mankhwala enaake amene wakupatsani angakukhudzeni bwanji. Ngati mwadabwa ndi vuto linalake lobwera chifukwa chomwa mankhwalawo, kaonaneni ndi dokotala.

● Funsani kuti mudziŵe pamene mudzasiyire kumwa mankhwalawo. Muyeneranso kudziŵa ngati mankhwalawo amavuta kuwasiya.

● Peŵani kuti musasiye kumwa mankhwala mongofuna nokha, mwina chifukwa chakuti mwayamba kupezako bwino. Kusiya mankhwala mwamsanga kungakulitse vuto lanu. Koma muziyamba mwafunsa dokotala wanu.

● Nthaŵi zonse muzimwa mankhwala amene dokotala wakulemberani motsatira malangizo ake.