Kodi Anthu Akudziwonongera Okha Chakudya?
Kodi Anthu Akudziwonongera Okha Chakudya?
“Vuto lathu lenileni masiku ano si ngongole ndiponso kuwononga ndalama kapena kupikisana kwa mayiko, koma ndilo kufunika kopeza njira yoti tikhale ndi moyo wokhutiritsa, ndiponso wosangalatsa popanda kuwononga zinthu za m’dziko lathuli, zimene zimatheketsa moyo kukhalapo. Kalelonse anthu sanakumanepo ndi vuto loopsa limeneli la kuwonongeka kwa zinthu zimene zimatithandiza kukhala ndi moyo,” anatero katswiri wina wa sayansi ya zachibadwa cha zinthu, David Suzuki.
MPOSAVUTA kuona chipatso cha apulo ngati n’chipatso wamba. Ngati mumakhala m’dera limene mumamera maapulo ambiri mungaganize kuti n’ngosavuta kupezeka moti mutha kuchita kusankha mtundu wa maapulo umene mukufuna. Koma kodi mukudziŵa kuti mwina pali mitundu yochepa kwambiri imene mungasankhe masiku ano kuyerekezera ndi zaka 100 zapitazo?
Kuchokera m’chaka cha 1804 kufika m’chaka cha 1905, ku United States kunkalimidwa mitundu 7,098 ya maapulo. Masiku ano mitundu 6,121 mwa imeneyi, kapena kuti 86 peresenti inasoŵeratu. N’chimodzimodzinso ndi mapeyala. Pafupifupi 88 peresenti ya mitundu 2,683 imene inkadzalidwako tsopano inasoŵa. Ndipo tikanena za mitundu ya ndiwo zamasamba, ndiye yachita kunyanyiranso kuchepa kwake. Indedi, mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zachilengedwe yayamba kusoŵa. Zinthu zake ndizo mitundu ikuluikulu yambiri ya zachilengedwe, komanso mitundu ina yaing’ono yopezeka pakati pa mitundu yaikuluyi. Mitundu ya ndiwo zamasamba zolimidwa ku United States yachepa ndi 97 peresenti pasanathe zaka 80 zokha! Koma kodi n’kofunikadi kukhala ndi mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zamoyo.
Asayansi ambiri amanena kuti inde n’kofunika. Ngakhale kuti anthu sakugwirizana chimodzi pankhani ya kufunika kokhala ndi mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zamoyo, akatswiri angapo a zachilengedwe akunena kuti zimenezi n’zofunika kwambiri m’moyo wapadziko pano. Iwo amanena kuti n’zofunikanso ku mbewu zimene timadzala kuti tizidya monganso ku mbewu zomera m’tchire komanso m’madera a maudzu apadziko lonse. Kusiyanasiyana kwa mtundu umodzi omwewo wa mbewu n’kofunikanso. Mwachitsanzo, pakakhala mitundu yosiyanasiyana ya mpunga, n’kutheka kuti mitundu ina singagwidwe ndi matenda ofala. Motero, nkhani ina yofalitsidwa ndi bungwe la Worldwatch Institute inanena posachedwapa kuti makamaka chinthu chimodzi ndicho chingasonyeze anthu kuopsa kochepetsa mitundu ya zamoyo zapadziko; chinthucho ndicho mmene zimenezi zingawonongere chakudya chathu.
Kusoŵa kwa zomera kungawononge mbewu zodyedwa m’njira zikuluzikulu ziŵiri: yoyamba, n’njakuti kungawononge mbewu zomera zokha zomwe zili m’gulu la mbewu zolimidwa. Mbewu zomera zokhazi angathe kuzigwiritsa ntchito m’tsogolo paulimi wosanganiza mbewu zofanana mitundu. Njira yachiŵiri n’njakuti kungachepetse mitundu yaing’ono yopezeka m’magulu amitundu ya mbewu yodzalidwa. Mwachitsanzo kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, mwina ku Asia kunkalimidwa mitundu yoposa 100,000 ya mpunga wakomweko, ndipo pafupifupi 30,000 inkalimidwa ku India kokha. Pakali pano, 75 peresenti ya mpunga wonse wa ku India ndi mitundu yokwana khumi yokha basi. Kale ku Sri Lanka kunali mitundu yokwana 2000 ya mpunga, koma panopo kuli mitundu 5 basi. Ku Mexico komwe kunachokera chimanga, kukulimidwa mitundu yokwana 20 peresenti yokha mwa mitundu imene inaliko cha m’ma 1930.
Komatu vuto loopsali silikukhudza chakudya chokha. Pafupifupi 25 peresenti yamankhwala amalonda amachokera m’zomera, ndipo anthu akutulukirabe mitengo yomwe ndi mankhwala. Koma anthu akupitirizabe kuwonongeratu zomera. Kodi n’kutheka kuti tikudziphera tokha tsogolo?
Malingana ndi bungwe lina lapadziko lonse loyang’anira zachilengedwe la World Conservation Union, akuti mwa mitundu 18,000 ya zomera ndi zinyama imene aifufuza, yoposa 11,000 ingadzasoŵeretu. M’madera monga ku Indonesia, Malaysia, ndiponso Latin America, kumene tchire lambiri lakhala likuswedwa mphanje, ofufuza akutha kungoganizira chabe kuchuluka kwa mitundu ya zachilengedwe imene yatsala pang’ono kusoŵa, kapena imene yasoŵa kale. Komabe ena akuti kuwononga zachilengedweku “kukupitirira modetsa nkhaŵa zedi,” inatero nyuzipepala ya The UNESCO Courier.
N’zoona kuti dziko likubalabe chakudya chochuluka zedi. Koma kodi pakuti anthu akuchulukirachulukira akhala ndi chakudya kwa nthaŵi yaitali bwanji ngati mitundu ya zachilengedwe padzikoli itachepa? Poda nkhaŵa ndi zimenezi, mayiko ambiri apanga nkhokwe zosungirako mbewu kuti apeze podalira ngati mbewu zofunika zitasoŵa. Mabungwe ena olima maluŵa ayamba kuchita ntchito yosunga mitundu yazomera. Asayansi atulukira zida zamakono zosinthira chibadwa cha zinthu zachilengedwe. Koma kodi nkhokwe zosungirako mbewu ndiponso asayansi angathetsedi vutoli? Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.