Uchigaŵenga Utha Posachedwapa!
Uchigaŵenga Utha Posachedwapa!
BASI ku Jerusalem, nyumba ya boma ku Oklahoma, kapena nyumba yokhalamo anthu ku Moscow, zonsezi zigaŵenga zingathe kuziphulitsa. Ngakhale zimaoneka kuti zigaŵenga zimafuna kupereka uthenga wamphamvu kwambiri kwa andale, akuluakulu a asilikali, kapena kwa akuluakulu a zachuma, nthaŵi zambiri zimaoneka kuti zofuna za zigaŵengazo sizigwirizana ndi zomwe zimawononga. Nthaŵi zambiri anthu wamba ndiwo amavutika—anthu oti sizikuwakhudza n’komwe zinthu zomwe zigaŵengazo zimanena motsindika kuti ndizo zikufuna. Nanga n’chifukwa chiyani anthu osafuna kumva za ena amachita zauchigaŵenga?
N’chifukwa Chiyani Amachita Zauchigaŵenga?
Uchigaŵenga umachitika mwadongosolo, ndiponso amaukonzekera bwino. Cholinga chake chenicheni sikupha kapena kuvulaza anthu ambirimbiri ayi. Kupulula miyoyo mwanjira imeneyo kumawathandiza kupeza zomwe akufuna, ndipo ndi njira ina yopangitsa kuti anthu azikhala mwamantha yomwe zigaŵenga zimatsata pofuna kuti anthu asamakhulupirire boma ndi kuti ena amve zolinga zawo zenizeni. Taonani zina mwa zifukwa zomwe zimachititsa kuti zigaŵenga zichite ziwawa.
Chidani. “Chidani . . . chimalimbikitsa uchigaŵenga,” anatero Louis J. Freeh, mkulu wa bungwe lofufuza la U. S. Federal Bureau of Investigation. “Anthu omwe amasungira chidani choterocho amakhala m’madera amene salolera maganizo a anzawo, okonda zachiwembu, ndiponso odzala ndi umbuli.”
Kuponderezana. “M’pofunika kudziŵa kuti pali atsogoleri ena a magulu ndi mayiko omwe zolinga zawo zosimbwa ndizo kupululutsa mitundu ina ya anthu,” anatero Stephen Bowman m’buku lake lakuti When the Eagle Screams. “Komanso n’zodziŵikiratu kuti uchigaŵenga wochuluka umachitika chifukwa chotaya mtima.”
Kukhumudwa. “Nthaŵi zambiri . . . chinthu chachikulu chomwe chimalimbikitsa uchigaŵenga ndicho kukhumudwa koopsa chifukwa cha mabungwe a zandale, zachikhalidwe, ndi a zachuma omwe amaoneka ngati kuti sangasinthe,” anatero mkonzi wa buku la Urban Terrorism.
Kusoŵa Chilungamo. “Uchigaŵenga ndi chizindikiro choti pali vuto, sindiwo gwero lenileni la vuto,” anatero Michael Shimoff m’chikalata chake chakuti “Mfundo Zolimbana ndi Uchigaŵenga.” Anapitiriza kuti: “Cholinga chathu nthaŵi zonse chiyenera kukhala choti tithetse mavuto a zandale ndi zachikhalidwe omwe amayambitsa uchigaŵenga. . . . Pamene tikulimbana ndi uchigaŵenga, tiyeneranso kuyesetsa mofananamo kulimbikitsa ufulu, kulemekezana, chilungamo, ndiponso kuthandizana. Khama limenelo likadzagwira ntchito pamenepo ntchito yathu yolimbana ndi uchigaŵenga idzatha.”
Zimene zimachititsa uchigaŵenga komanso mbiri ya uchigaŵengawo zatsimikizira kuti mawu aŵa a m’Baibulo ndi oona: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Baibulo linaloseranso za makhalidwe omwe alimbikitsa uchigaŵenga. Limati: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, . . . opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima.”—2 Timoteo 3:1-4.
Choonadi chake n’chakuti zoyesayesa za anthu zofuna kuthetsa uchigaŵenga, ngakhale atatsimikiza mtima chotani, sizingathetseretu magwero ake. Baibulo limanena molondola kuti: “Njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Koma ngakhale kuti anthu sangathe kupeza njira yothetsera uchigaŵenga, kwa Mulungu imeneyi si nkhani yovuta.
Njira Yothetsera Uchigaŵenga
Anthu omwe anzawo anawalakwira kapena kuwapondereza ndipo ali okhumudwa angalimbike mtima ndi lonjezo lodalirika ili la m’Baibulo lakuti: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”—Miyambo 2:21, 22.
Lonjezo la Mulungu limeneli likwaniritsidwa posachedwapa. Wolamulira wake, Mfumu Yesu Kristu, adzachita zimenezo. Ulosi wa m’Baibulo ponena za Kristu umati: “Sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera; koma ndi chilungamo adzaweruza aumphaŵi, nadzadzudzulira ofatsa a m’dziko moongoka.”—Yesaya 11:3, 4.
Inde, Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, adzachotsa posachedwapa kusoŵa chilungamo konse limodzinso ndi anthu osoŵetsa chilungamo. M’dongosolo latsopano lolungama la Mulungu, uchigaŵenga ndi ziwawa za mtundu uliwonse zidzakhala mbiri yakale. Ndiyeno aliyense padziko lapansi adzakhala motetezeka, osaopanso kuvulala.—Chivumbulutso 21:3, 4.
[Chithunzi patsamba 20]
Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa Mulungu adzathetseratu kuponderezana konse ndiponso kusoŵa chilungamo