Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ziŵerengero Zochititsa Mantha za AIDS!

Ziŵerengero Zochititsa Mantha za AIDS!

Ziŵerengero Zochititsa Mantha za AIDS!

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA

THEMBEKA ndi mtsikana wazaka 12 yemwe amakhala m’dera la kumidzi kumwera kwa Africa. Makolo ake anamwalira ndi AIDS, ndipo iye ndiye amasamalira ang’ono ake atatu; wazaka 10, wazaka 6, ndi wazaka 4. “Atsikanaŵa alibe njira iliyonse yopezera ndalama ndipo amadalira anansi achifundo pa chilichonse . . . buledi, ndi mbatata zoŵerengeka,” anatero mtolankhani. Chithunzi cha atsikana anayi amasiyeŵa, chinaikidwa patsamba loyamba la nyuzipepala ya ku South Africa yomwe inafotokoza za msonkhano wokambirana za matenda a AIDS wa 13th International Aids Conference womwe unachitika mu July 2000, ku Durban, m’dziko la South Africa.

Mamiliyoni a ana amasiye omwe makolo awo anamwalira ndi AIDS ali mumkhalidwe wofanana ndi wa Thembeka ndi ang’ono akewo. Nthumwi za ku msonkhanowo, zinakambirana njira zochepetsera kufala kwa mliri wa AIDS, monga kuphunzitsa anthu mmene angapewere AIDS mwa kugwiritsa ntchito makondomu, kugwiritsa ntchito mankhwala otsikirapo mtengo omwe akupezeka tsopano; ndi kupeza ndalama zambiri zofufuzira katemera wa AIDS. Anakambirananso mfundo yakuti akazi ndiwo ali pangozi yaikulu, makamaka atsikana ang’onoang’ono.

N’zomvetsa chisoni kuti ana ambiri omwe ndi amasiye chifukwa cha AIDS, amagonedwa ndi amuna amene amakhulupirira kuti kugona ndi namwali kumachiza matenda opatsirana mwakugonana. Kuwonjezera apo, amuna ambiri sakwatira mtsikana pokhapokha atabereka mwana choyamba. Choncho, makondomu amaoneka monga cholepheretsa ukwati ndi kubereka.

Mwatsoka, atsikana ambiri sazindikira kuopsa kwa AIDS. Nyuzipepala ya Sowetan ya ku South Africa inathirira ndemanga pa lipoti lomwe bungwe la United Nations Children’s Fund (UNICEF) linatulutsa pamsonkhanowo: “Malinga ndi kufufuza komwe a Unicef anachita, atsikana 51 mwa atsikana 100 alionse azaka 15 mpaka 19 ku South Africa, sankadziŵa kuti munthu wathanzi angakhale ndi kachilombo ka HIV ndipo akhoza kuwapatsira.”

Mchitidwe wina umene umafalitsa AIDS ndiwo kugona ndi akazi mokakamiza. Ranjeni Munusamy, yemwe anali nawo pamsonkhanopo analemba m’nyuzipepala ya Sunday Times ya ku Johannesburg, ku South Africa kuti: “Kuchitira nkhanza akazi, kumene ndi mphamvu yoipitsitsa imene amuna amagwiritsa ntchito, kudakali chopinga chachikulu pa kupewa ndi kusamala za HIV. Mwanjira zake zambiri—kugwiririra, kugonana pachibale, kumenya akazi ndi kugona nawo mokakamiza—kukusonyeza kuti kaŵirikaŵiri kugonana kumachitika mokakamiza, ndipo ndiwo mchitidwe waukulu kwambiri wofalitsa kachilombo ka HIV.”

Ziŵerengero zomwe zinatulutsidwa pamsonkhanowo zinali zochititsa mantha, monga mmene tchatichi chikusonyezera. Tsiku lililonse, achinyamata pafupifupi 7,000, ndi ana ang’ono 1,000 amatenga HIV. M’chaka chimodzi, cha 1999, ana 860,000 a m’mayiko a mu Africa a kumwera kwa chipululu cha Sahara, aphunzitsi awo anamwalira ndi AIDS.

Malinga ndi kafukufuku wofalitsidwa ndi a Medical Research Council of South Africa, anthu 4.2 miliyoni a ku South Africa ali ndi kachilombo ka HIV, ndiko kuti, munthu mmodzi mwa anthu 10 alionse. M’mayiko oyandikana nalo, zinthu zafika poipa kwambiri. Nyuzipepala ya Natal Witness inafalitsa ziŵerengero zomwe bungwe la U.S. Census Bureau linapeza: “Chiŵerengero cha anthu m’mayiko a mu Africa momwe AIDS yafala kwambiri, posachedwapa chiyamba kuchepa pamene mamiliyoni a anthu akufa ndi matendaŵa, ndipo zaka zomwe anthu amayembekezera kukhala ndi moyo, zichepa kufika pafupifupi 30 pakutha kwa zaka 10.”

Mliri wa AIDS ulinso umboni wakuti mtundu wa anthu ukukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zomwe Baibulo linaneneratu kuti zidzaoneka “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5) Okonda Mawu a Mulungu, Baibulo, amayembekezera njira yeniyeni ndiponso yokhalitsa yothetsera AIDS ndi mavuto ena onse omwe akusautsa anthu. Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu udzayamba kuyendetsa zinthu padziko lapansi. M’dziko latsopano lachilungamo, umphaŵi ndi kuponderezana zidzakhala zinthu zakale. (Salmo 72:12-14; 2 Petro 3:13) M’malo mwake, anthu okhala padziko lapansi adzakhalanso ndi thanzi langwiro, ndipo palibe yemwe adzati: “Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Padziko lonse pali ana amasiye 13,000,000 omwe makolo awo anafa ndi AIDS

[Tchati/Mapu patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

CHIŴERENGERO CHA ANTHU (AZAKA 15 mpaka 49) OMWE ANALI NDI HIV/AIDS, KUMAPETO KWA 1999

Kumpoto kwa America 890,000

Caribbean 350,000

Latin America 1,200,000

Kumadzulo kwa Ulaya 520,000

Kum’maŵa ndi Pakati pa Ulaya 410,000

Kumpoto kwa Africa ndi ku Middle East 210,000

Mayiko a mu Africa a Kumwera kwa

Chipululu cha Sahara 23,400,000

Kumwera ndi Kumwera cha Kum’maŵa kwa Asia 5,400,000

Kum’maŵa kwa Asia ndi ku Pacific 530,000

Australia ndi New Zealand 15,000

[Mawu a Chithunzi]

Gwero: UNAIDS

[Chithunzi patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

PERESENTI YA ANTHU (AZAKA 15 mpaka 49) OMWE ANALI NDI HIV/AIDS M’MAYIKO 16 A MU AFRICA, KUMAPETO KWA 1999

1 Botswana 35.8%

2 Swaziland 25.2

3 Zimbabwe 25.0

4 Lesotho 23.5

5 Zambia 20.0

6 South Africa 20.0

7 Namibia 19.5

8 Malawi 16.0

9 Kenya 14.0

10 C.A.R. 14.0

11 Mozambique 13.2

12 Djibouti 11.7

13 Burundi 11.3

14 Rwanda 11.2

15 Côte d’Ivoire 10.7

16 Ethiopia 10.6

[Mawu a Chithunzi]

Gwero: UNAIDS

[Chithunzi]

Thembeka ndi ang’ono ake

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi: Brett Eloff