Ana Ayenera Kufunidwa Ndiponso Kukondedwa
Ana Ayenera Kufunidwa Ndiponso Kukondedwa
“MUKONDENI chabe mwanayo ndipo mapeto ake adzakuchitirani zazikulu.” Analemba motero mngelezi wotchedwa John Ruskin wolemba ndiponso wofufuza wa m’zaka za m’ma 1800. Mosakayikira, makolo ambiri angavomereze kuti munthu ukamakonda ana ako zimathandizadi, osati chifukwa cha zabwino zokha zomwe makolowo angalandire koma kwenikweni, chifukwa cha zabwino zomwe chikondicho chidzawachititse anawo.
Mwachitsanzo, buku lakuti Love and Its Place in Nature (Chikondi Ndiponso Ntchito Yake M’chilengedwe) linanena kuti popanda chikondi “ana amangofa.” Ndipo Ashley Montagu, amene ali katswiri wodziŵika wa sayansi ya chikhalidwe cha anthu wa ku Britain anafika ponena kuti: “Mwana amene sakondedwa, makemikolo a thupi lake, thupi lake lenilenilo, ndiponso maganizo ake zimasiyana kwambiri ndi za mwana amene amakondedwa. Mwana wosakondedwayo amakula mosiyana kwambiri ndi amene amakondedwa.”
Nyuzipepala ya Toronto Star inapereka lipoti pa kafukufuku yemwe potsiriza pake anapeza mfundo yofananayo. Nyuzipepalayo inati: “Ana amene amaleredwa popanda kumawakumbatira kapena kumawasisita. . . nthaŵi ndi nthaŵi, amakhala ndi mahomoni ofooketsa ochuluka monkitsa.” Ndithudi, kunyalanyaza kuyangata ana akadali aang’ono “kungakhale ndi zotsatirapo zokhalitsa zoopsa zomwe zingakhudze kuphunzira kwawo ndiponso kukumbukira kwawo zinthu.”
Mfundo zimenezi zikugogomezera kufunika koti makolo azikhalapo. Ngati apo ayi, kodi chibale pakati pa kholo ndi mwana chingakule bwanji? Koma n’zomvetsa chisoni kuti ngakhale kumadera otukuka a padziko lapansi, tsopano kuli chizoloŵezi chomafuna kupatsa mwana zinthu zofunika koma popanda kum’patsa makolo ake. Ana amangowatumiza kusukulu, ku Sande sukulu, kuntchito, ku kampu kopita ndi anzawo, mwinanso kungowapatsa ndalama n’kuwatumiza ku malo achisangalalo. Ana ambiri ngati sakuchita nawo zinthu pamodzi ndi banja kapena ngati sakuŵerengedwa m’banjamo, mwachibadwa mwinanso mosazindikira n’komwe, amadziona kukhala onyanyalidwa, osafunidwa, ndi osakondedwa, ndiponso amadziona ngati ali pakati pa anthu achikulire ankhanza okhaokha. Maganizo ofala ameneŵa ndiwo amachititsa ana pafupifupi 3,000 kumakhala m’misewu ku Berlin. Chitsanzo chenicheni ndi wachinyamata Micha yemwe ananena kuti: “Palibe ndi m’modzi yemwe amene ankandifuna.” Mwana wina wa ku Germany wa zaka zisanu ndi zinayi anadandaula chimodzimodzi amvekere: “Ndingasangalale n’takhala galu wathuyu.”
Ana Amazunzidwa M’njira Zambiri
Kunyalanyaza mwana ndiyo njira imodzi ya kuzunza imene imasonyeza kusoŵa chimene Baibulo limatcha kuti “chikondi chachibadwidwe.” (Aroma 1:31; 2 Timoteo 3:3) Khalidwe limeneli lingachititse kuzunza ana m’njira zina zoipa kwambiri. Mwachitsanzo, kuchokera m’Chaka Choganizira Mwana cha 1979, kuzunza ndiponso kugona ana ndiwo mavuto amene asamalidwa kwambiri. N’zoona kuti kupeza ziŵerengero zolondola pankhaniyi n’kovuta, ndiponsotu ziŵerengerozo zimasiyanasiyana m’madera madera. Komabe, mfundo yosakayikitsa n’njakuti mavuto omwe ana amene amagonedwa amakula nawo amakhala ovuta kuwathetsa.
Kaya ana akuzunzidwa m’njira yanji, iwo amazindikirabe kuti sakondedwa ndiponso sakufunidwa. Ndipo vutoli likuoneka kuti likukulirakulira. Malinga ndi zimene nyuzipepala ya ku Germany yotchedwa Die Welt inanena, “ana amene akukula ndi makhalidwe opotoka akuchulukirachulukira.” Nyuzipepalayo inawonjezera kuti: “Ana amasoŵa mtendere wapanyumba. Malinga ndi zomwe ananena [Gerd Romeike yemwe ndi mkulu wa pa sukulu ina yolangiza ana yotchedwa Hamburge], kugwirizana pakati pa ana ndi makolo kukumka kucheperachepera, mwinanso sikukhalapo n’komwe. Ana otereŵa amadziona kukhala onyanyalidwa ndipo chikhumbo chawo chofuna kutetezedwa chimangofera m’mazira.”
Ana amene alibe mwayi wokhala ndi ufulu wofunidwa ndiponso kukondedwa angakhale aukali, kuwasonyeza amene awanyalanyazawo mwinanso anthu ena onse kuti akhumudwa nawo. Pafupifupi zaka khumi zapitazo, lipoti la kagulu kena ka
ku Canada linasonyeza kufunika kwa kuchitapo kanthu mwamsanga, apo ayi, ndiye kuti mbadwo wonse wa ana “amene amaganiza kuti anthu sawasamalira” usokonekera.Achinyamata amene sakondedwa ndiponso kuonedwa monga ofunika angayese kuchoka panyumba kuti athaŵe mavuto, koma mapeto ake amakangoloŵa m’mavuto ena aakulu akapita m’mizinda yodzala ndi chiwawa, mankhwala osokoneza bongo, ndiponso chiwerewere. Ndipotu, zaka zopitirira makumi aŵiri m’mbuyomo, apolisi ananena kuti pafupifupi achinyamata othaŵa panyumba okwana 20,000 osakwana zaka 16 ankakhala mumzinda umodzi wokha wa ku United States. Achinyamatawo akuti “nthaŵi zambiri anali ochokera m’mabanja osudzulana ndiponso ankhanza zadzaoneni chifukwa chakuti kaŵirikaŵiri makolo awo anali zidakwa za moŵa kapena za mankhwala osokoneza bongo. Achinyamatawa amangoyendayenda m’misewu kugulitsa matupi awo mwakuchita zachiwerewere kuti azipeza ndalama zogulira zinthu zofunika m’moyo wawo. Ndipo akamenyedwa ndi mabwana awo ndiponso akasiya kudziona monga oyenera ulemu, iwo amakhala mwamantha kuopa kuti adzawakhaulitsa ngati atayesa kuthaŵa ntchito yokakamizayo.” N’zomvetsa chisoni kuti khalidwe loipali likadalipobe ngakhale kuti anthu ayesetsa moona mtima kuti lithe.
Ana amene amakulira m’mikhalidwe yomwe yafotokozedwa pamwambayi nthaŵi zambiri amadzakhala opepera akadzakula, osakhoza kulera bwino ana awo. Popeza kuti iwowo sakuonedwa ngati ofunika ndiponso sakukondedwa, patsogolo pake nawonso amabereka ana otero amene amadziona ngati osafunidwa ndiponso osakondedwa. Munthu wina wandale wa ku Germany ananena mosapita m’mbali kuti: “Ana osakondedwa amadzakhala ankhanza akadzakula.”
N’zoona kuti makolo ambiri akuyesetsa kwabasi kuti ana awo azidziŵa kuti amafunidwa ndiponso kukondedwa. Iwo sikuti amangowauza chabe anawo komanso amawasonyeza zimenezi mwa kuwasamalira mwachikondi ndiponso kuwapatsa zofunika zomwe mwana aliyense payekha amafunikira. Komabe, mavuto adakalipo ndipo ndi oti anthu sangakwanitse kuwathetsa. Mwachitsanzo, m’madera ena adziko lapansi, kayendetsedwe ka chuma ndiponso ndale kosalongosoka ka anthu, kalephera kuchititsa kuti ana akhale ndi chithandizo chokwanira chamankhwala, maphunziro oyenera, chakudya chokwanira komanso kalephera kuwateteza ku mliri wa kugwiritsa ntchito ana mwaukapolo ndiponso ku mikhalidwe ina yoipa. Ndipo nthaŵi zambiri mikhalidwe imeneyi imakula chifukwa cha umbombo, ziphuphu, kudzikonda, ndiponso kusaganizira anthu ena komwe anthu aakulu ena ali nako.
Mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations a Kofi Annan anatchulapo mavuto ena aakulu amene ana akukumana nawo masiku ano pamene analemba kuti: “Ana miyandamiyanda adakali pamavuto ochotsa ulemu obwera ndi umphaŵi wadzaoneni; ena zikwi mazana ambiri akuvutika chifukwa cha nkhondo ndi mavuto azachuma; ena zikwi makumi ambiri akupundulidwa pankhondo; ndipo ena ambirimbiri ndi amasiye mwinanso akumwalira ndi matenda a HIV/AIDS.”
Komabe, sikuti nkhani zonse n’zoipa ayi! Mabungwe a UN monga la United Nations Children’s Fund (UNICEF) ndiponso la World Health Organization ayesetsa kupititsa patsogolo zinthu zambiri zokhudza ana. A Annan ananena kuti: “Ana ambiri akubadwa athanzi ndipo ambiri
amalandira katemera owateteza kumatenda, ena ambiri amatha kulemba ndi kuŵerenga, ambiri ali omasuka kuphunzira, kuseŵera, ndiponso ngakhale kungokhala monga ana kusiyana ndi mmene tinkaganizira ngakhale pambuyo pa zaka khumi zapita posachedwazi.” Komabe, iye anachenjeza kuti: “Ino sindiyo nthaŵi yoti tikhutire ndi zomwe tachita m’mbuyomu.”Ana Amene Amayenera Chisamaliro Chapadera
Ana ena amayenera chisamaliro chapadera. Kumayambiriro kwa m’ma 1960, dziko lonse linadabwa kumva malipoti ochokera m’mayiko ambiri onena za kubadwa kwa ana opuwala chifukwa cha mankhwala otchedwa thalidomide. Amayi oyembekezera akamwa m’bulu wa mankhwala ofooketsa ndiponso ogonetsa ameneŵa, mankhwalaŵa ankayambitsa matenda ena osayembekezereka amene ankachititsa amayiwo kubereka ana opuwala kapena opandiratu manja kapena miyendo. Nthaŵi zambiri manja ndiponso miyendo inkakhala yopyapyala kwabasi kungokhala ngati nkhafi zopalasira bwato.
Patapita zaka makumi anayi chinthu chodziŵika kwambiri pa kupundula ana ndicho mabomba okwirira pansi. * Anthu ena amati mabomba oti angathe kuphulika okwiriridwa kulikonse m’nthaka ya padziko lonse lapansi alipo 60 miliyoni kapena mpaka kufika 110 miliyoni. Anthu pafupifupi 26,000 kuphatikizapo ana amaphedwa kapena kupundulidwa chaka n’chaka. Kuyambira m’chaka cha 1997 pamene Jody Williams anapata mphoto ya Nobel Peace Prize chifukwa cha mfundo zake zokopa anthu kuti aletse mabomba okwirira pansi, anthu ayesetsa kwambiri kulimbana ndi vuto limeneli. Komabe, madera omwe adakwirirako mabomba otereŵa adakalipobe. Ponenapo za ntchito yochotsa mabombaŵa, munthu wina wandale wa ku Germary ananena kuti: “Kulingati kuyesa kuchotsa madzi odzaza ndowa pogwiritsa ntchito sipuni uku mpopi ukuthira madzi ena m’ndowamo.”
Ana amasiye ndiwo gulu linanso la ana amene ayenera kusamalidwa mwapadera. Yehova Mulungu, Mlengi wa anthu, anafuna kuti ana azikula uku akusamalidwa mwachikondi ndi amayi ndiponso abambo awo omwe. Mwana amafunika ndiponso amayenera kuleredwa motero.
Malo osamalirako ana amasiye ndiponso mabungwe olera ana amasiye amayesa kuthandiza pa zinthu zimene ana omwe alibe makolo onse aŵiri amasoŵa. Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti nthaŵi zambiri ana ena osoŵa thandizo amene akufunadi kwambiri thandizolo ndiwo amanyalanyazidwa—ana odwala, ana omwe sangathe kuphunzira bwinobwino, opuwala, kapenanso amene akuleredwa ndi makolo ochokera kunja.
Kwapangidwa mabungwe olimbikitsa anthu kuti azipereka ndalama nthaŵi ndi nthaŵi kuti potero “akhale kholo” la mwana wokhala m’dziko linalake losauka. Ndalama zomwe amaperekazo zimagwiritsidwa ntchito yophunzitsira mwanayo kapenanso kum’gulira zofunika pamoyo wake. Ngati kuli koyenera, angatumizirane zithunzi komanso makalata kuti alimbikitse ubale wawo. Ngakhale kuti zimenezi n’zothandiza, makonzedwe ameneŵa sakukwana monga njira yoyenera yothetsera mavuto a ana.
Chitsanzo china chochititsa chidwi kwambiri pa zomwe zachitika pofuna kuthandiza ana ndicho gulu lothandiza ana opanda makolo limene mu 1999 linkakondwerera kuti latha zaka makumi asanu likugwira ntchito.
Mudzi wa Ana Wotchedwa SOS
Mu 1949 m’tauni yotchedwa Imst, ku Austria, munthu wina wotchedwa Hermann Gmeiner anayambitsa bungwe lothandiza ana lomwe analitcha kuti Mudzi wa Ana Wotchedwa SOS. Kuchokera pomwe linayamba kugwira ntchito zake m’madera ochepa, bungweli lafalikira kumadera ambiri mpaka kufikitsa midzi pafupifupi 1,500 ndiponso mabungwe ena otereŵa akupezeka m’mayiko 131 a mu Africa, America, Asia, ndiponso a ku Ulaya.
Gmeiner anaona kuti zinthu zofunika kwambiri pa ntchito yakeyi ndi zinthu zinayi izi, mayi, abale, nyumba, ndiponso mudzi. “Mayi” ndiye maziko a “banja” la ana asanu kapena asanu ndi mmodzi mwinanso kuposerapo. Iye amakhala ndi anawo ndipo amayesetsa kumawasonyeza chikondi ndi chisamaliro chomwe mayi weniweni amayenera kuchisonyeza. Anawo amakhalabe pamodzi ‘m’banja’ limodzi ndiponso ndi “mayi” mmodzi mpaka nthaŵi itafika yoti achoke ‘panyumbapo.’ ‘M’banja’ m’makhala ana amisinkhu yosiyanasiyana. Popeza kuti anawo amakhala ndi “akulu” ndiponso “alongo” awo achikulirepo ndiponso ocheperapo, amaphunzira kusamalirana ndipo zimenezi zimawathandiza kupeŵa kukhala oganizira za iwo okha. Amayesetsa kuyanjanitsa anaŵa akadali aang’ono kuti akhale “banja.” Nthaŵi zonse ana amene alidi pachibale amaleredwa ‘m’banja’ limodzi.
Midzi imakhala ndi mabanja okwana 15, ndipo banja lililonse limakhala m’nyumba yawoyawo. Ana onse amaphunzitsidwa kuthandiza mayi awo kugwira ntchito zofunika panyumba. Ngakhale kuti bambo pangakhale palibe, pamakhala makonzedwe oti mwamuna wina azithandiza kupereka malangizo autate ndiponso kuti azionetsetsa kuti anawo akulangizidwa moyenera akalakwa. Anawo amapita ku sukulu yakumeneko. Banja lililonse limalandira ndalama mwezi uliwonse zomwe anazikhazikitsa kuti azilipirira zinthu zofunika. Chakudya ndi zovala amazigula chakomweko. Cholinga cha zonsezi n’choti anawo azoloŵere moyo weniweni wabanja, mavuto ake, ndiponso zokoma zake kuti athe kukhala moyo wabwino kwambiri. Zimenezi zimawakonzekeretsa kuti adzapeze mabanja awoawo akadzakula.
Kufunafunabe Njira Zoyenera Zothetsera Mavuto a Ana
Mabungwe olera ana amasiye, malo osungirako ana otereŵa, midzi ya SOS ya ana osoŵa thandizo, bungwe la UNICEF ndiponso mabungwe ena amtunduwu kapena magulu ena aanthu, amachita ntchito yabwino akamayesa kuthandiza ana ovutikaŵa. Komabe, palibe limodzi mwa mabungwe ameneŵa limene lingatsutse mfundo yakuti anthu ena akusoŵabe thandizo. Kaya atafunitsitsa motani, iwo sangapereke ziwalo zathanzi kwa ana opuwala, sangakonzenso maganizo a ana a mitu yozizira, sangayanjanitsenso ana ndi makolo awo amene ananyanyalana kapena kusudzulana, ngakhalenso kubwezeranso ana m’manja achikondi a makolo awo omwe anamwalira.
Kaya atayesa motani, anthu sangathe kupereka njira zoyenera zothetsera mavuto a ana. Komabe mavutoŵa adzathetsedwa ndithu! Inde, mwinanso sipatali monga mmene mukuganizira. Koma kodi adzathetsedwa bwanji?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 17 Onani nkhani zotsatizana zomwe zili ndi mutu wakuti “Mabomba Okwirira Pansi—Kodi N’kuthana Nawo Bwanji?” m’magazini yathu ya Galamukani! ya May 8, 2000.
[Zithunzi pamasamba 8, 9]
Mwana amafunika ndiponso amayenera chikondi cha makolo onse aŵiri