Kodi Maelementi Anakhalako Mwamwayi?
Kodi Maelementi Anakhalako Mwamwayi?
“Chinthu chilichonse m’Chilengedwe Chonse, ngakhale nyenyezi zokhala kutali kwambiri, n’zopangidwa ndi maatomu,” imatero The Encyclopedia of Stars & Atoms. Atomu imodzi imakhala yaing’ono kwambiri mwakuti siingaoneke, koma akakhalapo kagulu amapanga maelementi odziŵika. Ena mwa maelementi ameneŵa ndi zinthu zolimba zimene tingathe kuziona; ena ndi mpweya wosaoneka. Kodi zinthu zimenezi zinakhalako mwamwayi?
Maelementi Nambala 1 Mpaka 92
Ngakhale kuti n’kosavuta kumvetsa kapangidwe ka atomu ya hydrogen, ndiyo imachirikiza nyenyezi monga dzuŵa ndipo n’njofunika pamoyo. Atomu ya hydrogen ili ndi pulotoni imodzi mu nyukiliyasi yake ndipo ili ndi elekitironi imodzi yomwe imazungulira nyukiliyasiyo. Maelementi ena monga carbon, oxygen, golide, ndi mercury, ali ndi maatomu okhala ndi maelekitironi ambiri omwe amazungulira nyukiliyasi yokhala ndi mapulotoni ndi ma nyutuloni ambiri.
Zaka 450 zapitazo, maelementi 12 okha ndiwo ankadziŵika. Atatulukira ambiri, asayansi anazindikira kuti ali mu ndondomeko inayake yachilengedwe. Ndipo maelementi ameneŵa ataikidwa pa mndandanda wokhala ndi mizere yopingasa ndi yopita m’munsi, asayansi anatulukira kuti maelementi opezeka mumnzere umodzi wopita m’munsi anali ofanana zochitika. Koma mndandandawu unalinso ndi mipata kusonyeza kuti panali maelementi ena osadziŵika. Izi zinachititsa kuti wasayansi wa ku Russia wotchedwa Dmitry Mendeleyev aneneretu kuti pali elementi ina dzina lake germanium yokhala ndi ma pulotoni 32 mu nyukiliyasi yake. Ananeneratunso za maonekedwe ake, kulemera kwake, ndiponso mlingo wa kutentha umene ungaisungunule. Zimene Mendeleyev “ananeneratu zokhudza maelementi ena amene panalibe monga gallium ndi scandium, zinadzapezekanso kuti zinali zolondola kwambiri,” linatero buku la sayansi la 1995 lotchedwa Chemistry.
M’kupita kwa nthaŵi, asayansi ananeneratu zakuti kulinso maelementi ena osadziŵika ndipo anatchulanso zochita zawo. Mpaka maelementi onse amene anali osadziŵika anawapeza. Palibenso mipata iliyonse pa mndandandawo. Ndondomeko yachilengedwe ya maelementi n’njozikidwa pa kuchuluka kwa mapulotoni mu nyukiliyasi ya atomu, ndipo imayamba ndi elementi ya pa nambala 1, hydrogen, mpaka elementi yotsirizira imene nthaŵi zambiri imapezeka mwachilengedwe padziko lapansi, ya pa nambala 92 yomwe ndi uranium. Kodi zimenezi zinangochitika mwamwayi?
Taganiziraninso kusiyanasiyana kwa maelementi ameneŵa. Golide ndi mercury ndi maelementi amene ali ndi maonekedwe onyezimira mwapadera zedi. Enawo ndi chitsulo, enawo ndi amadzimadzi. Koma, anakhala motsatizana pa nambala 79 ndi 80. Atomu ya golide ili ndi maelekitironi 79, mapulotoni 79, ndi manyutuloni 118. Atomu ya mercury ili ndi elekitironi ndiponso pulotoni imodzi chabe kuposa apa, ndipo ili ndi manyutuloni ochuluka mosasiyana kwenikweni.
Kodi ndi mwayi chabe kuti kusintha kwapang’ono chabe kwa dongosolo la zidutswa za mu atomu kumabweretsa maelementi osiyanasiyana chonchi? Nanga bwanji za mphamvu zimene zimagwirizanitsa pamodzi tizidutswa ta maatomu? “Chinthu chilichonse m’Chilengedwe Chonse chimatsatira mfundo zimene malamulo a sayansi amalongosola, kuyambira pa kanthu kakang’ono kwambiri kufika pa gulu lalikulu kwambiri la nyenyezi,” imatero The Encyclopedia of Stars & Atoms. Taganizani zimene zingachitike itasintha imodzi mwa mfundo zimenezo. Mwachitsanzo, kodi chingachitike n’chiyani mphamvu imene imatheketsa maelekitironi kuyenda mozungulira nyukiliyasi ya atomu itasintha pang’ono?
Mphamvu Zachilengedwe Zolinganizika Bwino
Taganizirani zimene zingachitike itachepa mphamvu yokoka yotchedwa elekitiromaginetizimu. “Maelekitironi sangathenso kumatirira ku maatomu,” anatero Dr. David Block m’buku lake lakuti Star Watch. Kodi zimenezi zingachititse chiyani? “Tingakhale ndi chilengedwe chosalola maatomu kusanganikirana kuti apange zinthu zina zatsopano!” iye anawonjezera choncho. Tiyeneradi kuyamikira kwambiri malamulo okhazikika amene amatheketsa zinthu monga zimenezi kuchitika! Mwachitsanzo, maatomu aŵiri a hydrogen amaphatikizana ndi atomu imodzi ya oxygen n’kupanga molekyu ya madzi ofunikawo.
Mphamvu yokoka yotchedwa elekitiromaginetizimu ndi yofookerapo nthaŵi 100 kuyerekeza ndi mphamvu yochuluka yokhala mu nyukiliyasi ya atomu imene imamanga pamodzi nyukiliyasiyo. Kodi chingachitike n’chiyani mphamvuzi zitasintha? “Ngati mphamvu za mu nyukiliyasi ndi mphamvu yokoka yotchedwa elekitiromaginetizimu zimene zimadalirana zikanati zisiyane pang’ono chabe ndi mmene zilili, ndiye kuti maatomu a carbon si bwenzi alipo,” akutero asayansi aŵiri John Barrow ndi Frank Tipler. Pakanapanda carbon ndiye kuti sipakadakhala moyo. Maatomu a carbon ali mbali imodzi mwa mbali zisanu zilizonse za kulemera kwa zinthu zonse zamoyo.
Chofunikanso kwambiri ndicho kuchuluka kwa mphamvu yokoka ya elekitiromaginetizimu poiyerekezera ndi mphamvu yokoka ya giravite. “Kusintha kwakung’ono kwambiri kwa mphamvu yokoka ya giravite ndi elekitiromaginetizimu kungasandutse nyenyezi monga Dzuŵa kukhala nyenyezi zabuluu zazikulu kwadzaoneni [zotentha kwambiri kwakuti moyo sungakhalepo] kapena kukhala nyenyezi zazing’ono zofiira [zosatentha mokwanira kuti moyo ukhalepo],” inatero magazini yotchedwa New Scientist.
Mphamvu ina, yotchedwa mphamvu yochepa ya mu nyukiliyasi, imayendetsa kusakanikirana kwa maatomu mu dzuŵa pamlingo woyenera. “Ndi yochepa mokwanira kulola hydrogen imene ili m’dzuŵa kuyaka pang’onopang’ono ndiponso mokhazikika,” anatero wasayansi wotchedwa Freeman Dyson. Palinso zitsanzo zina zambiri zosonyeza mmene moyo wathu umadalira malamulo olinganizika mosamala zedi ndiponso mikhalidwe imene ili m’thambo. Wolemba zasayansi, pulofesa Paul Davis anayerekeza malamulo ndiponso mikhalidwe ya m’thambo imeneyi ndi mabatani ndipo ananena kuti: “Zikuoneka kuti mabatani osiyanasiyanaŵa ayenera kutchunidwa bwino zedi kuti thambo likhale loti moyo n’kukhalamo.”
Zaka zambiri Bambo Isaac Newton asanatulukire lamulo la mphamvu yokoka, Baibulo linatchulapo za malamulo okhazikika ameneŵa. Yobu anafunsidwa kuti, “Kodi ndiwe unaika malamulo amene amayendetsa zakumwamba, kapena kukhazikitsa malamulo a chilengedwe padziko lapansi?” (Yobu 38:33, The New English Bible) Mafunso ena osonkhezera munthu kudzichepetsa anali akuti, “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi?” ndi “Analemba malire ake ndani, popeza udziŵa?”—Yobu 38:4, 5.
[Bokosi patsamba 6]
MAELEMENTI OFUNIKA
Maatomu a maelementi otchedwa hydrogen, oxygen, ndi carbon alipo 98 pa maatomu 100 alionse m’thupi lanu. Ndiyenso pali nitrogen imene ilipo maatomu 1.4 pa maatomu 100 alionse. Maelementi ena amapezeka mochepa kwambiri koma n’ngofunikabe pamoyo.
[Tchati/Chithunzi pamasamba 6, 7]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Pamene nkhani ino imalembedwa, asayansi anali atapanga maelementi nambala 93 kumka m’tsogolo, mpaka kufika nambala 118. Monga ananeneratu, maelementi ameneŵa amagwirizanabe ndi ndondomeko ya mndandanda wa maelementi.
[Mawu a Chithunzi]
Gwero: Los Alamos National Laboratory
Dzina la elementi Chizindikiro Atomic number (kuchuluka kwa mapulotoni)
hydrogen H 1
helium He 2
lithium Li 3
beryllium Be 4
boron B 5
carbon C 6
nitrogen N 7
oxygen O 8
fluorine F 9
neon Ne 10
sodium Na 11
magnesium Mg 12
aluminum Al 13
silicon Si 14
phosphorus P 15
sulfur S 16
chlorine Cl 17
argon Ar 18
potassium K 19
calcium Ca 20
scandium Sc 21
titanium Ti 22
vanadium V 23
chromium Cr 24
manganese Mn 25
iron Fe 26
cobalt Co 27
nickel Ni 28
copper Cu 29
zinc Zn 30
gallium Ga 31
germanium Ge 32
arsenic As 33
selenium Se 34
bromine Br 35
krypton Kr 36
rubidium Rb 37
strontium Sr 38
yttrium Y 39
zirconium Zr 40
niobium Nb 41
molybdenum Mo 42
technetium Tc 43
ruthenium Ru 44
rhodium Rh 45
palladium Pd 46
silver Ag 47
cadmium Cd 48
indium In 49
tin Sn 50
antimony Sb 51
tellurium Te 52
iodine I 53
xenon Xe 54
cesium Cs 55
barium Ba 56
lanthanum La 57
cerium Ce 58
praseodymium Pr 59
neodymium Nd 60
promethium Pm 61
samarium Sm 62
europium Eu 63
gadolinium Gd 64
terbium Tb 65
dysprosium Dy 66
holmium Ho 67
erbium Er 68
thulium Tm 69
ytterbium Yb 70
lutetium Lu 71
hafnium Hf 72
tantalum Ta 73
tungsten W 74
rhenium Re 75
osmium Os 76
iridium Ir 77
platinum Pt 78
gold Au 79
mercury Hg 80
thallium Tl 81
lead Pb 82
bismuth Bi 83
polonium Po 84
astatine At 85
radon Rn 86
francium Fr 87
radium Ra 88
actinium Ac 89
thorium Th 90
protactinium Pa 91
uranium U 92
neptunium Np 93
plutonium Pu 94
americium Am 95
curium Cm 96
berkelium Bk 97
californium Cf 98
einsteinium Es 99
fermium Fm 100
mendelevium Md 101
nobelium No 102
lawrencium Lr 103
rutherfordium Rf 104
dubnium Db 105
seaborgium Sg 106
bohrium Bh 107
hassium Hs 108
meitnerium Mt 109
110
111
112
114
116
118
[Chithunzi]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Kodi dongosolo komanso kugwirizana kwa maelementi a mu mndandanda wa maelementi zimasonyeza kuti anangokhalako mwamwayi chabe kapena panafunikira luntha?
Atomu ya helium
Elekitironi
Pulotoni
Nyutuloni
[Chithunzi patsamba 7]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Kodi n’chiyani chinachititsa kuti mphamvu zinayi za m’chilengedwe zikhale zotchunidwa bwino?
MPHAMVU YA ELEKITIROMAGINETIZIMU
MPHAMVU YOCHULUKA YA M’NYUKILIYASI
MPHAMVU YOKOKA
MPHAMVU YOCHEPA YA M’NYUKILIYASI
Molekyu ya madzi
Nyukiliyasi ya atomu
Nyenyezi yabuluu yaikulu kwadzaoneni
Nyenyezi yofiira yaing’ono
Dzuŵa